13. Osakweza mawu kapena kusokosera mumzikiti komanso malo onse ozungulira mnzikiti.[1]
عن السائب بن يزيد رضي الله عنه قال كنت نائما في المسجد فحصبني رجل فنظرت فإذا عمر بن الخطاب رضي الله عنه فقال اذهب فأتني بهذين فجئته بهما فقال ممن أنتما أو من أين أنتما قالا من أهل الطائف قال لو كنتما من أهل المدينة لأوجعتكما ترفعان أصواتكما في مسجد رسول الله صلى الله عليه وسلم (صحيح البخاري، الرقم: 470)[2]
Olemekezeka Saib bin Yazeed akusimba kuti; Nthawi ina yake ndinagona munzikiti ndipo munthu wina anandiponya timiyala ting´onoting´ono (ndicholinga chondidzutsa), ndidayang´ana ndipo ndidapeza kuti adali Umar (radhiyallah anhu). Iye adati kwa ine; Pita undibweretsere anthu awiri amenewa kwa ine (amene akusokoserawa), Ndipo ndinawabweretsa kwa Umar (radhiyallah anhu), ndipo anawafunsa nati, Inu ndiochokera kuti? Iwo adayankha nati ndife ochokera ku Taif. Olemekezeka Umar (radhiyallah anhu) adati Inuyo mukadakhala ngati anthu a mmadinah muno ndikadakupatsani chilango chokhwima kwambiri Mukukweza mawu mumzikiti wa Mtumiki (swallallah alayhi wasallama).
عن أبي هريرة رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم إذا اتخذ الفيء دولا والأمانة مغنما والزكاة مغرما وتعلم لغير الدين وأطاع الرجل امرأته وعق أمه وأدنى صديقه وأقصى أباه وظهرت الأصوات في المساجد وساد القبيلة فاسقهم وكان زعيم القوم أرذلهم وأكرم الرجل مخافة شره وظهرت القينات والمعازف وشربت الخمور ولعن آخر هذه الأمة أولها فارتقبوا عند ذلك ريحا حمراء وزلزلة وخسفا ومسخا وقذفا وآيات تتابع كنظام قطع سلكه فتتابع (سنن الترمذي، الرقم: 2211)[3]
Olemekezeka Abuu hurayrah (radhiyallah anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallah alayhi wasallama adati; Pamene chuma chopeza kunkhondo (ya asilamu ndi makafiri) chidzakhale chikutengedwa ngati chuma chawanthu cholinga choti angogawana okha okha, ndipo Chinthu chosingisidwa (amana) nachitengedwa ngati ndichuma chawina aliyense, ndipo zakati nayiwonedwa ngati Mtsonkho, Ndipo maphunziro achipembezo naphunzilidwa ndicholinga chazinthu zina osakhala za dini, Ndipo pamene mwamuna azamvere mkazi wake ndikunyoza mayi ake (makolo ake) nampanganso mnzake kukhala bwezi omuyandikira iye bambo ake ndikuwataya, komanso mawu nakwezedwa mmizikiti, Nakhala anthu oipisisa atsogoleri amibadwo, ndipo nakhala asogoleri anthu apansi kwambiri, nalemekedzedwa munthu kamba kakumuopa kuipa kwake, Komanso tiasika toyimba nyimbo ndizida zoyimbila nyimbo nazikhala ponseponse, komanso mowa naumwedwa mowonekera, ndipo anthu osilizira aumah inu nadzatukwana anthu oyambilila aummah uno (Pamene zizindikiro zimenezi zidzaonekere) anthu akuyenera kudzayembekedzera zinthu izi: Namondwe, Zivomerezi,kumidzidwa kwawanthu ndinthaka,kutembenuzidwa kwankhope, Mvula yamiyala kuchokera kumwamba, ndiponso zizindikiro zina zizakhala zikundondozana mwachangu ngati makanda omwe waduka.
[1] تكره الخصومة في المسجد ورفع الصوت فيه ونشد الضالة وكذا البيع والشراء والاجارة ونحوها من العقود هذا هو الصحيح المشهور (المجموع شرح المهذب 2/141)
[2] قال الحافظ في الفتح (1/656): قوله كنت قائما في المسجد كذا في الأصول بالقاف وفي رواية نائما بالنون ويؤيده رواية حاتم عن الجعيد بلفظ كنت مضطجعا
[3] قال أبو عيسى: وفي الباب عن علي وهذا حديث غريب
وعن علي رضي الله عنه عن النبي صلى الله عليه وسلم قال إذا فعلت أمتي خمس عشرة خصلة فقد حل بها البلاء قيل وما هي يا رسول الله قال إذا كان المغنم دولا وإذا كانت الأمانة مغنما والزكاة مغرما وأطاع الرجل زوجته وعق أمه وبر صديقه وجفا أباه وارتفعت الأصوات في المساجد وكان زعيم القوم أرذلهم وأكرم الرجل مخافة شره وشربت الخمر ولبس الحرير واتخذت القينات والمعازف ولعن آخر هذه الأمة أولها فليرتقبوا عند ذلك ريحا حمراء أو خسفا أو مسخا رواه الترمذي وقال لا نعلم أحدا روى هذا الحديث عن يحيى بن سعيد الأنصاري غير الفرج بن فضالة (سنن الترمذي، الرقم: 2210)