Masunnah Ochita Mumzikiti

14. Onesetsani kuti mwathimisa foni yanu pamene mukulowa mumzikiti ndicholinga choti musasokoneze nayo anthu amene ali otangwanika ndimapemphero ndi ma ibaada ena ndi ena.[1]

15. Osajambula mafoto kapena kupanga vidiyo pamene muli mumzikiti. Kujambula foto komanso kupanga vidiyo chinthu chamoyo ndi Haraam mchisilamu. ndipo kuchita zimenezi mumzikiti nditchimo lalikulu.

عن عبد الله رضي الله عنه قال سمعت النبي صلى الله عليه وسلم يقول إن أشد الناس عذابا عند الله يوم القيامة المصورون (صحيح البخاري، الرقم: 5950)

Olemekezeka Abdullah bin Masud (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki Muhammad (sallallahu alaih wasallam) adati, “Ndithudi anthu amene Allah adzawalange ndichilango chachikulu patsiku lachiweruzo ndi amene amajambula zithuzi.

16. Pamene mukuyankhula munzikiti sizabwino kukweza mawu.[2]

مالك أنه بلغه أن عمر بن الخطاب بنى رحبة في ناحية المسجد تسمى البطيحاء وقال من كان يريد أن يلغط أو ينشد شعرا أو يرفع صوته فليخرج إلى هذه الرحبة (موطأ مالك، الرقم: 602)

Imaam Maalik akusimba kuti, Olemekezeka Umar (radhiyallahu anhu) anakhoza malo apadera patali ndipamzikiti amene ankatchedwa kuti Bataihaa.Iye Umar (radhiyallahu anhu) adati: amene akufuna kuchita phokoso kapena kuwerenga ndakatulo kapenanso kukweza mawu akamayankhula akuyenera kutuluka kupita kumalo amenewa (patali ndipamzikiti ndiye azikayankhula kumeneko mmene akufunira)


[1] تكره الخصومة في المسجد ورفع الصوت فيه ونشد الضالة وكذا البيع والشراء والاجارة ونحوها من العقود هذا هو الصحيح المشهور (المجموع شرح المهذب 2/141)

[2] يكره اللغظ ورفع الصوت في المسجد (إعلام الساجد بأحكام المساجد صـ 326)

Check Also

Masunnah Ochita Mumzikiti

27. Khalani mwaulemu ndi modekha pamene muli mumzikiti musakhale moiwala kulemekezeka kwa mzikiti. Anthu ena …