21. Mukamaliza kudzithandizako, dikirani madontho otsalira kunkodzo wanu kuti amalizike musanapange wuzu.
Read More »Kapangidwe Ka Istinja (Kutawasa) Ka Sunnah ~ Gawo Lachinayi
11. Musayankhule pamene mukudzithandiza, pokhapokha patafunikira kuti mulankhule.
Sayyiduna Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati, anthu awiri asakadzithandizire malo amodzi komwe akakhale ndikumayankhulana maliseche awo ali pantetete (osavala) ndithudi Allah Ta'ala amadana ndi nchitidwe otelewu.’’
Read More »Kapangidwe Ka Istinja (Kutawasa) Ka Sunnah ~ Gawo Lachitatu
7. Lowani kuchimbudzi ndiphanzi lamanzere.
8. Musavule chovala chanu chakumusi muli chiimire, m’malo mwake, chotsani chovala chanu chakumusichi mukamayandikira kunjuta pansi kuti pasadutse nthawi yayitali muli chivulire.
Read More »Kapangidwe Ka Istinja (Kutawasa) Ka Sunnah ~ Gawo Lachiwiri
4. Tchingani kumutu kwanu musanalowe kuchimbudzi.
Sayyiduna Habib bin Saalih (rahimahullah) akusimba kuti, Nabi (sallallahu alaih wasallam) ankavala nsapato zake ndikutchinga kumutu (kuvala chisoti) akamalowa kuchimbudzi”
Read More »Kapangidwe Ka Istinja (Kutawasa) Ka Sunnah ~ Gawo Loyamba
1. Mudzithandizire pamalo a nokhanokha posaonedwa ndi anthu.
Sayyiduna Jaabir (radhwiyallahu anhu) akunena kuti, Nabi (sallallahu alaih wasallam) ankati akafuna kudzithandiza, ankapita malo amene sangaonedwe ndi Anthu (anthu sangamuone).
Read More »Chenjezo Kwa Osasamala Za Ukhondo Akamapanga Istinja (Kutawasa)
Hadith yoyamba
Sayyiduna Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati:"Chilango chachikulu (chomwe anthu ambiri amakumana nacho) m'manda ndi chifukwa cha nkodzo (kusasamala nkodzo omwe umadonthekera pathupi komanso unve wina. kotero, wudhu wawo, swalah ndi ibadah ina siidzalandiridwa chifukwa chosowekera ukhondo)"
Read More »Kudzithandiza Komanso Kupanga Istinja (Kutawasa) – Chiyambi
Chisilamu ndichipembedzo chomwe chili ndi ukhondo Kwambiri, chisilamu chimalimbikitsa ukhondo komanso kudziyeretsa m'magawo onse amoyo wamunthu,
Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati:
الطهور شطر الإيمان
"Kudziyeretsa nditheka ya chikhulupiliro"
Read More »
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu