Durood Ndi Salawaat

Kupeza Mwayi Okhala Pafupi Ndi Nabi (Salallah Alayhi Wasallam) Patsiku Lachiweruzo

Sayyiduna Abu umaamah (radhwiyallahu anhu) akusimbanso kuti: Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati: “Chulukitsani kunditumizira Durood ine lachisanu lililonse, Ndithudi Durood imene ummah wanga umachita imabweretsedwa kwa ine lachisanu lililonse. (Choncho) amene amachulukitsa kunditumizira Durood ineyo ndi amene adzakhale kufupi kwambiri ndi ine (patsiku lachiweruzo).

Read More »

Kulandila Mphotho Zokwana Makumi Asanu Ndi Ziwiri

Sayyiduna Abdullah bin Amr bin Aas (radhwiyallahu anhuma) akufotokoza kuti, munthu amene angamfunile zabwino Nabi (sallallahu alaih wasallam) kamodzi, Allah amanchitira chisoni munthu ameneyo kokwana ka 70, angelo amamupemphera chisoni munthu ameneyo kokwana ka 70 komanso ndi madalitso kukhala ngati malipilo a kumfunila mtumiki zabwino kamodzi. Choncho munthu amene akufuna kuti achulukitse kumfunila zabwino Nabi (sallallahu alaih wasallam) ayenera kutero, komanso amene akufuna kuti achepetse akhonzanso kutero (ngati akufuna kuti apeze malipilo ochuluka akuyenera kuchulukitsa kumfunila zabwino Nabiiyo).

Read More »

Kupeza Sawabu Zomasura Akapolo Okwana Khumi (10)

Sayyiduna Baraa bin Aazib (radhwiyallahu anhu) akunena kuti Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati, "amene angandiwelengere Durood kamodzi, mmalo mwa Durood imeneyo Allah adzamulipira munthu ameneyo sawabu zokwana khumi adzamufufutira (adzamukhululukira) machimo okwana khumi adzamukwezera ulemelero wake ndimasiteji khumi komanso Durood yomwe adawerengayo idzakhala njira yomupatsa sawabu zomasura akapolo khumi.

Read More »

Kukhululukidwa Machimo

Sayyiduna Abu Burdah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti, Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati,” amene anganditumizire Durood mwa ummah wanga kuchokera pansi pa mtima, Allah adzamdalitsa munthu ameneyo pompatsa zifundo zokwana khumi, adzamukwezera ulemelero wake ndi masiteji okwana khumi ku Jannah, adzamulipira sawabu zokwana khumi ndikumukhululukira machimo okwana khumi.”

Read More »

Ma Ulemelero Khumi Amakwezedwa

Sayyiduna Anas bin Maliki (radiyallah anhu) akusimba kuti, Nabi (salallah alayhi wasallam) adati; "Amene angandifunire ine zabwino kamodzi (popanga Durood), Allah Ta´ala adzamutumizira iyeyo madalitso khumi, machimo ake khumi adzakhululukidwa ndiponso levo yake ku Jannah idzakwezedwa ndi masiteji okwanira khumi".

Read More »

Nkhani Yabwino Yochoka Kwa Allah Ta’ala Kwa Awo Amene Amawerenga Durood

Sayyiduna Abdul Rahman bin Aufi (radhwiyallahu anhu) akunena kuti, tsiku lina Nabi (sallallahu alaih alaihi wasallam) adachoka kunyumba kwake ndipo ndidamulondora, kufikira mpaka adalowa m'munda wa tende nagwetsa nkhope yake pansi. Nabi (sallallahu alaihi wasallam) adakhala pasajdah kwanthawi yaitali mpaka ndidaganiza ngati Allah wachotsa nzimu wake. Kenaka ndidapita pafupi kuti ndikaone chomwe chanchitikira Nabi (sallallahu alaih wasallam). 

Read More »