Kupeza Sawabu Zomasura Akapolo Okwana Khumi (10)

عن البراء بن عازب أن النبي صلى الله عليه وسلم قال: من صلى علي كتب الله عز وجل له بها عشر حسنات ومحا عنه بها عشر سيئات ورفعه بها عشر درجات وكن به عدل عتق عشر رقاب (الصلاة على النبي لابن أبي عاصم، الرقم: ٥٢، وقد ذكره المنذري في الترغيب والترهيب بلفظة “عن”، إشارة إلى كونه صحيحا أو حسنا أو ما قاربهما عنده كما بين أصله في مقدمة كتابه ١/٥٠)

Sayyiduna Baraa bin Aazib (radhwiyallahu anhu) akunena kuti Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene angandiwelengere Durood kamodzi, mmalo mwa Durood imeneyo Allah adzamulipira munthu ameneyo sawabu zokwana khumi adzamufufutira (adzamukhululukira) machimo okwana khumi adzamukwezera ulemelero wake ndimasiteji khumi komanso Durood yomwe adawerengayo idzakhala njira yomupatsa sawabu zomasura akapolo khumi.

Khumbo Lofuna Kukhala Limodzi Ndi Nabi (Sallallahu Alaih Wasallam)

Tsiku lina, sahabi wina (radhwiyallahu anhu) adabwera kwa Nabi (sallallahu alaih wasallam) ndipo adati, Oh Nabi (sallallahu alaih wasallam), ndiinu okondedwa kwaine kuposa m’mene ndimadzikondera ine mwini, kuposaso chuma changa ndi banja langa, ndikakhala kunyumba kwanga, ndimayamba kuganiza zainu ndiponso sindimakhazikika, sindimaipeza mtima pokhapokha nditakuonani, Oh Nabi wa Allah (sallallahu alaih wasallam), imfa ndiyosapeweka mukadzamwalira mudzakhala apamwamba kwambiri chifukwa choti ndiinu Nabi komanso Rasul wa Allah Ta’ala pamene ine ndidzatalikirane nanu, Oh Nabi (sallallahu alaih wasllam) nkutheka sindingadzapeze mwayi okuonani, nthawi zonse ndikaganizira zakusiyana kumeneku komwe kudzabwere chifukwa cha imfa ndimakhala okhumudwa ndikhudzidwa kwambiri.”

Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adakhala chete kufikira pamene m’ngero Jibril (alaih salaam) adabwera ndi Ayah iyi:

وَمَنْ يُطِعِ اللهَ وَالرَّسُولَ فَأُولئِكَ مَعَ الَّذِينَ أَنْعَمَ اللهُ عَلَيْهِمْ مِنَ النَّبِيِّينَ وَالصِّدِّيقِينَ وَالشُّهَداء وَالصَّالِحِينَ وَحَسُنَ أُولئِكَ رَفِيقاً

Ndipo amene angamvere Allah ndi Rasulu wake, Iwowo ndi omwe adzakhale pamodzi ndi omwe Allah adawadalitsa, kuyambira aneneri alaihim salaam, Olungama, mashahid (asilamu ofera kunkhondo) ndi anthu abwino. Taonani ubwino wokhala nawo pamodzi iwowo! (Al-Mujamul Awsat #477)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …