Kulandira Zifundo Zokwana Khumi (10)

عن أبي هريرة أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال: من صلى علي واحدة صلى الله عليه عشرا (صحيح مسلم،  الرقم: ٤٠٨)

Sayyiduna Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Nabi (sallallahu alaihi wasallam) adati, amene anganditumizire Durood kamodzi, Allah Ta’ala adzamulipira munthu ameneyo ndikumpatsa zifundo zokwana khumi.

Nkhani Yabwino Yochokera Kwa Nabi (Sallallahu Alaih Wasallam)

Sayyiduna  Muhammad Utbi (rahimahullah) akufotokoza kuti:

Ndidalowa munzinda wa Madinah munawwarah ndipo ndidaima pafupi ndi manda olemekezeka a Nabi (sallallahu alaih wasallam), pambuyo pake ndidamuona munthu wina atabwera, anaimika ngamira yake pakhomo lanzikiti ndikubweranso pafupi ndi manda a Nabi (sallallahu alaih wasallam), adapeleka salaam modzichepetsa ndimwachikondi, ndipo adapanga duwa kupempha Allah mochititsa kanso.

Kenaka adati, oh Nabi (sallallahu alaih wasallam) makolo anga aperekedwe nsembe chifukwa cha inu, inde! Allah Ta’ala adakusankhani inu mwauzimu kukhala Nabi wake otsiriza, ndipo adakupatsani wahyi (chibvumbulutso cha Qur’an). Adabvumbulutsa bukhu lapaderadera (Qur’an yolemekezeka) lomwe likupezeka ndi chiphunzitso cha aneneri alaihimus salaam atsopano ndi akale. Allah Ta’ala akunena kuti, ndipo mawu ake ndi owona:

وَلَوْ أَنَّهُمْ إِذْ ظَلَمُوا أَنْفُسَهُمْ جاؤُكَ فَاسْتَغْفَرُوا اللَّهَ وَاسْتَغْفَرَ لَهُمُ الرَّسُولُ لَوَجَدُوا اللَّهَ تَوَّاباً رَحِيماً

Ndipo ngati (akapolo anga) pambuyo pochita choipa (kuchimwa) akadabwera kwa iwe, (oh Muhammad sallallahu alaih wasallam) napempha chikhululuko kwa Allah ndipo Nabi ndikwapemphera chikhululuko akadampeza Allah, kuti iye ndi olandira kulapa kwawo komanso wachisoni.

Kenaka munthu uja adati, oh Nabi wa Allah, ndabwera pa manda anu pofuna kukwaniritsa Aaya ya Allah. Ndikuvomera kuti ndadzilakwira ndekha pochimwa kwambiri ndipo ndikukupemphani kuti mundipemphere chikhululuko kwa Allah, kenaka adatembenukira pamandapo ndikulira kwambiri uku akuwerenga ndakatulo iyi:

یا خیر من دفن بالقاع أعظمه،
فطاب من طیبهن القاع والأکم

O iwe Olemekezeka mwa amene akwiliridwa pansi panthaka!

Kudzera mukuwala konunkhira kochokera muziwalo zanu zodalitsika, kudapangitsa maprli ndi zigwa kuti zinunkhire.

نفسی الفداء لقبر أنت ساکنه،
فیه العفاف وفیه الجود والکرم

Moyo wanga uperekedwe nsembe kumanda amene mukuwusa, Manda ake amene aikidwamo thupi loyera, lolemekezeka komanso lowolowa manja (lopereka)

Atamaliza kuwerenga mau abwinowa okhuza kumutamanda ndi kumulemekeza Nabi (salallahu alayhi salaam), Munthu wakumudzi uja adakwera nyama yake ndipo ananyamuka.

Muhammad Utbi (amene akulongosola nkhaniyi) akufotokoza kuti :”Ndinaphimbidwa ndi tulo tofa nato, ndipo mutulomo ndinalota, ndinadalitsidwa ndi maloto omuona Nabi (salallahu alayhi wasallam).

Nabi (sallallahu alayhi wasallam) adandiyankhula nati; O Utba! Fulumira ndipo mupitire munthu wakumudzi uja ndipo ukampatse nkhani yabwino yochokera kwa Ine yoti Allah Ta’ala wamukhululukira machimo ake.’’(Al Qowl-ul-Badee pg. 342)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …