عن أنس بن مالك قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم من صلى علي صلاة واحدة صلى الله عليه عشر صلوات وحطت عنه عشر خطيئات ورفعت له عشر درجات (سنن النسائي، الرقم: ١٢٩٧، وسنده حسن كما في المطالب العالية ١٣/٧٨٥)
Sayyiduna Anas bin Maliki (radiyallah anhu) akusimba kuti, Nabi (salallah alayhi wasallam) adati; “Amene angandifunire ine zabwino kamodzi (popanga Durood), Allah Ta´ala adzamutumizira iyeyo madalitso khumi, machimo ake khumi adzakhululukidwa ndiponso levo yake ku Jannah idzakwezedwa ndi masiteji okwanira khumi”.
Mtengo Umene Udapeleka Salaam Kwa Nabi (sallallahu alaih wasallam)
Sayyiduna Ya’ala bin Murrah (radhwiyallahu) anhu akufotokoza:
Tidali paulendo ndi Nabi (sallallahu alaih wasallam) ndipo tidaima malo ena ake, titaima (kuti tipume) Nabi (sallallahu alaih wasallam) adakagona penapake, kenaka tinaona mtengo ukuyenda mong’amba nthaka kufikira mpakana udaudzitsa mthuzi kwa Nabi (sallallahu alaih wasallam), kenaka unabwelera pamalo pake.
Nabi (sallallahu alaih wasallam) a tadzuka, ndidamfotokozera zomwe zidachitikazo, Nabi (sallallahu alaih wasallam) adati,” ndi mtengo umene udapempha mbuye wake kuti ubwere kwaine ndikundipatsa salaam, Allah Ta’ala adaulora kutero.” (Al-Qowlul Badee’ Pg. 162, Musnad Ahmed #17565)