Adhaan Ndi Iqaamah

Ubwino wa Muadhin

6. Anthu ochita Adhaan afotokozedwa mmahadith kuti iwowo ndi akapolo abwino kwambiri mwa akapolo a Allah Taala.

Olemekedzeka Ibn Abi Awfaa radiyallah anhu akusimba kuti, Mtumiki (salallah alayhi wasallam a) adati; "Ndithudi akapolo abwino kwambiri ndiamene amayang´ana (kutuluka ndikulowa) kwa dzuwa, mwezi, nyenyezi ndi kutalika kwa zithuzithuzi cholinga chomukumbikira Allah Taala. (kukwanirisa mapemphero awo (ibaadah) panthawi yake yoyenerera mofanana ndichilamulo cha Allah Taala, uku akusunga nthawi kudzera mukuona dzuwa, mwezi, nyenyezi ndiutaali wazithuzizithuzi monga ngati momwe zafotokozeledwa mumahadith. Muazin akuikidwanso munkhani yabwino imeneyi chifukwa choti iyeyo amasunga nthawi cholinga choti apange azaana panthawi yake yolondola.)

Read More »

Ubwino wa Muadhin

5. Muadhin walonjezedwa kuti adzakhululukilidwa machimo ake Chimodzimozinso kwapatsidwa kwa iye nkhani yabwino yoti kuti Muadhin amadalitsidwa popatsidwa malipiro (sawabu) mofanana ndi amene abwera kudzapemphera malingana kuti iwowo ayankha kuitana kwa Muadhiniyo.

Read More »

Ubwino wa Muadhin

3. Pali mphotho zochuluka zomwe adzalandire ndi munthu amene amapanga Adhaan.

Olemekezeka Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: “anthu akadakhala kuti akudziwa malipiro aakulu amene amapeza mukuchita adhaan komanso kuswali utaima nzere oyamba Ndipo Pamapeto ake sipakadapezeka kusemphana kulikonse posankha kupatula kupanga mayele ndithu akadapanga mayele kuti apanga chiganizo."

Read More »

Ubwino wa Muadhin

Adhaan ndi chimodzi mwazizindikiro za chisilamu, chisilamu chimalemekeza kwambiri anthu amene amapanga Adhaan, kuwaitanira anthu kuti adzaswali.Tsiku lachiweluzo anthu adzawasilira anthu amene ankachita adhaan padziko lino lapansi chifukwa cha ulemelero umene anthuwa adzakhale nawo. Ma hadith ochuluka alongosora za maubwino a muadhin ndi zabwino zimene akalandire patsikuli. 1. Muadhin adzakhala …

Read More »

Adhaan – Chiyambi Chake 1

Mtumiki (sallallahua alaih wasallam) atapanga Hijrah (atasamukira) kupita ku Madina Munawwarah adamanga nzikiti. Atamanga nzikiti adakambirana ndi ophunzira ake nkhani yopezera njira imene angamawaitanire anthu kuti adzaswali. Lidali Khumbo la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti anthu adzisonkhana ndikuswalira pamodzi munzikiti. Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sankasangalatsidwa kuti masahabah adzaswali aliyense payekha …

Read More »