5. Muadhin walonjezedwa kuti adzakhululukilidwa machimo ake Chimodzimozinso kwapatsidwa kwa iye nkhani yabwino yoti Muadhin amadalitsidwa popatsidwa malipiro (sawabu) mofanana ndi amene abwera kudzapemphera malingana kuti iwowo ayankha kuitana kwa Muadhiniyo.
عن البراء بن عازب رضي الله عنه أن نبي الله صلى الله عليه وسلم قال إن الله وملائكته يصلون على الصف المقدم والمؤذن يغفر له بمد صوته ويصدقه من سمعه من رطب ويابس وله مثل أجر من صلى معه (سنن النسائي، الرقم: 645)[1]
Olemekezeka Baraa bin Aazib (radiyallah anhu) akusimba kuti nthenga wa Allah madalitso ndi ntendere zipite kwa iye adati; Ndithudi Allah amapereka chifundo chake chapadera kwa amene amaswali ataima munzere oyamba ndiponso angelo amawachitiranso maduwa apadera. Ndipo Muadhin (opanga adhaan) adzalandila chikhululuko chochokera kwa Allah pamtunda onse umene mau ake amakafika popanga adhaanayo (ngati adali ndi machimo ochulukitsitsa kumakafika mpaka komwe nkuwo wake ukumafika, machimo onsewo adzakhululukidwa, kapena nthawi imene iye wagwiritsa ntchito kupanga Adhaan pamoyo wake onse amakhululukidwanso) Ndipo cholengedwa chirichonse kaya chili ndi moyo kapena chakufa chidzamuchitira umboni patsiku La Qiyaamah ndiponso adzalandila malipiro (sawabu) olingana ndi anthu onse amene angapemphere swalah ndi iyeyo. (kapena anthu amenenso angapemphere swalah chifukwa cha Adhaan yake).
[1] سنن النسائي، الرقم: ٦٤٥، وإسناده حسن جيد كما في الترغيب والترهيب للمنذري ١/٢٤٣