3. Pali mphotho zochuluka zomwe adzalandire ndi munthu amene amapanga Adhaan.
عن أبي هريرة رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه وسلم قال لو يعلم الناس ما في النداء والصف الأول ثم لم يجدوا إلا أن يستهموا عليه لاستهموا (صحيح البخاري، الرقم: 615)
Olemekezeka Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati: “anthu akadakhala kuti akudziwa malipiro aakulu amene amapeza mukuchita adhaan komanso kuswali utaima nzere oyamba Ndipo Pamapeto ake sipakadapezeka kusemphana kulikonse posankha kupatula kupanga mayele ndithu akadapanga mayele kuti apanga chiganizo.”
4. Cholengedwa chilichonse (kuyambila ziwanda, anthu, ndizolengedwa zonse) zimene zimamva mawu amuazin pamene akupanga Adhaan zidzamuchitira umboni patsiku la Qiyaama.
عن عبد الرحمن بن عبد الله بن عبد الرحمن بن أبي صعصعة الأنصاري ثم المازني عن أبيه أنه أخبره أن أبا سعيد الخدري رضي الله عنه قال له إني أراك تحب الغنم والبادية فإذا كنت في غنمك أو باديتك فأذنت بالصلاة فارفع صوتك بالنداء فإنه لا يسمع مدى صوت المؤذن جن ولا إنس ولا شيء إلا شهد له يوم القيامة قال أبو سعيد سمعته من رسول الله صلى الله عليه وسلم (صحيح البخاري، الرقم: 609)
Kunanenedwa ndi olemekedzeka Abdulla bin Abdirahman bin Abi Sa´sa´ah (rahimahullah), Iye adati; Nthawi ina olemekedzeka Abuu saidi (Radiyallah anhu) adati kwa iye; Ine ndikuona kuti umakonda kuweta ziweto zako kutchire. Pamene iweyo uli ndiziweto zakozo kapena uli kutchireko (ndipo nthawi yoswali ndikukwana) kenako iweyo wafuna kupanga Adhaan, Ukuyenera pamenepo kupanga Adhaan mokweza mau kwambiri, Ndithudi! popeza Ziwanda, anthu ndicholengedwa chilichonse chimene chingamve mau a Adhaan (zolengedwazi) zidzamuchitira umboni munthu yemwe akupanga Adhaanayo patsiku la Qiyaamah. Olemekedzeka Abu Saeed (radhiyallahu anhu akunena kuti, ndidanva hadith imeneyi kuchokera Kwa Mtumiki wa Allah madaritso ndi mtendere za Allah zipite kwa iye.