Mtumiki (sallallahua alaih wasallam) atapanga Hijrah (atasamukira) kupita ku Madina Munawwarah adamanga nzikiti. Atamanga nzikiti adakambirana ndi ophunzira ake nkhani yopezera njira imene angamawaitanire anthu kuti adzaswali. Lidali Khumbo la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti anthu adzisonkhana ndikuswalira pamodzi munzikiti. Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sankasangalatsidwa kuti masahabah adzaswali aliyense payekha payenkha munzikiti ngakhalenso m’nyumba zawo.
Masahabah (radhiyallahu anhum) adapereka maganizo awo osiyanasiyana okhudza m’mene anthu angamaitaniridwire kudzapemphera, maganizo amasahabah ena anali oti moto udziyatsidwa kapena mbendera idzikwezedwa m’mwamba ndicholinga choti anthu akaona malawi a moto kapena mbendera itakwezedwa azizindikira kuti nthawi yoswali yakwana ndipo awadziwitse ena kuti abwere kunzikiti.
Maganizo ena anali oti chitoliro chidzilizidwa kapena Naaquus (ndodo ziwiri) zizimenyetsedwa kuwadziwitsa anthu kuti nthawi yaswalah yakwana.
Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sadakhutitsidwe ndi maganizo onsewa.
Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sadafune kuti ummah wake utengere a khirisitu, Ayuda ndi anthu achikunja onse njira zawo zochitira zinthu za Dini kapena Dziko. Asilamu akadati atengere njira zimenezi ndiye kuti zikadafanana ndi makafiri komanso padakakhala kupombonezeka popeza anthu sakadamasiyanitsa chifukwa anthu osakhulupilira akugwiritsira ntchito njira zomwezo powaitanira anthu awo kumapemphero.
Padalibe nfundo yeniyeni yomwe adagwirizana pa nkumano umenewu ndipo nsonkhano udatha popanda Kugwirizana nfundo yeniyeni.
Anthu asadabalalikane pa nsonkhanowu Sayyiduna Umar (radhiyallahu anhu) adapelekako maganizo kunena kuti, popeza palibe nfundo yomwe tagwirizana, kwanthawi imeneyi bwanji titasankha munthu amene nthawi ya swalah ikakwana adziyenda m’nyumba za anthu kuwadziwitsa kuti nthawi ya swalah yokwana.
Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adagwirizana ndi maganizo a Sayyiduna Umar radhiyallahu anhu ndipo adasankha Sayyiduna Bilaal (radhiyallahu anhu) kuti agwire ntchito imeneyi, kotero nthawi yoswali ikakwana Bilaal (radhiyallahu anhu) ankayenda m’makomo ndi kwadziwitsa anthu kuti Jamaat yatsala pang’ono kuti iyambe.
Mtima waswahabah aliyense udadzadza ndi lingaliro la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) lokhudza njira imene igwiritsidwe ntchito kuwaitanira anthu kuti adzaswalire pamodzi munzikiti.
Nkhani siikuthera pompa, sipadadutse masiku ambiri pambuyo pa zimenezi, usiku wina Sayyiduna Abdullah bin Zaid (radhiyallahu anhu) atakagona adalotetsedwa maloto ndi Allah, kumalotoko adamuona mngelo komano anali mmaonekedwe a munthu amene adavala mikanjo iwiri ya ntundu wa gilinindipo adanyamula Naaquus, swahabayu adamufunsa mngeloyo kuti oh kapolo wa Allah! Kodi Naaquus watengayi ndiyogulitsa? Mngelo uja adayankha pomufunsa kuti “ukufuna ukagwiritse ntchito yanji? Abdullah bin Zaid (radhiyallahu anhu) adati ndikagwiritsa ntchito kuwaitanira anthu kubwera kuswalah” mngelo uja adayankha adati “kodi ndisakuuze njira yabwino kwambiri kuposa kumenyetsa Naaquusiyi?” Sayyiduna Abdullah (radhiyallahu anhu) adafunsa kuti “ndi njira yanji yomwe ndi yabwino kwambiri” mngelo uja adayankha kuti “udziitana adhaan” pambuyo pake mngelo uja adamuphunzitsa Abdullah (radhiyallahu anhu) mawu opangira adhaan.
Atadzuka m’mawa wake adapita kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndipo adamulongosolera Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) zamaloto ake aja. Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) atanva zamalotowa adati, “ndithudi mal0to amenewa ndi owona takhala pambali ndi Bilaal (radhiyallahu anhu) ndipo umuphunzitse mawu a Adhaan amene udaphunzitsidwa kumalotowo kuti apange Adhaan ndi mawu amenewa. Mulore Bilaal (radhiyallahu anhu) kuti apange Adhaan popeza iyeyo mawu ake ndi okwera Kusiyana ndi ako ndipo mawu akewo anvekera patali.
Umar (radhiyallahu anhu) atanva Adhaan ya Bilaal (radhiyallahu anhu) adatenga nsalu yake mwachangu ndikuthamangira kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Atafika uko pagulu pomwe padali Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) mwaulemu adati, “Oh Mtumiki wa Allah! Ndikulumbilira amene adakusankha iwe kukhala Mtumiki wake kuti udzafalitse chisilamu chenicheni ndinalota maloto ndipo kumalotoko ndidaphunzitsidwa mawu a Adhaan” Mtumiki (sallallahu alai wasallam) atanva mawuwa adasangalala kwambiri ndipo adati, izi zatsimikizira kukhala zoona kuchokera kwa Allah.”
Zafotokozedwa kuti masahabah oposera khumi adalotetsedwa maloto onga omwewa ndipo kumalotoko adaphunzitsidwa mawu a Adhaan ndipo mwa masahabah amenewa mudalinso Sayyiduna Abu Bakar komanso Umar (radhiyallahu anhuma).