Ubwino wa Muadhin

6. Anthu ochita Adhaan afotokozedwa m’mahadith kuti iwowo ndi akapolo abwino kwambiri mwa akapolo a Allah Ta’ala.

عن ابن أبي أوفى رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم إن خيار عباد الله الذين يراعون الشمس والقمر والنجوم والأظلة لذكر الله (المستدرك على الصحيحين للحاكم، الرقم: 163)[1]

Olemekezeka Ibn Abi Awfaa (radiyallah anhu) akusimba kuti, Mtumiki (salallah alayhi wasallam ) adati; “Ndithudi akapolo abwino kwambiri ndi amene amayang´ana (kutuluka ndikulowa kwa)dzuwa, mwezi, nyenyezi ndi kutalika kwa zithuzithuzi cholinga chomukumbukira Allah Ta’ala. (kukwaniritsa mapemphero awo (ibaadah) panthawi yake yoyenerera mofanana ndi chilamulo cha Allah Ta’ala, uku akusunga nthawi kudzera mukuona dzuwa, mwezi, nyenyezi ndiutaali wazithuzizithuzi monga ngati momwe zafotokozeredwa m’mahadith. Muadhin akuikidwanso munkhani yabwino imeneyi chifukwa choti iyeyo amasunga nthawi ndicholinga choti apange adhaan mu nthawi yake yolondola.)

7. Kupulumutsidwa ku moto kwalonjezedwa kwa munthu amene angakhale akupanga Adhaan kwa zaka zisanu ndi ziwiri (7).

عن ابن عباس رضي الله عنهما أن النبي صلى الله عليه وسلم قال من أذن سبع سنين محتسبا كتبت له براءة من النار (سنن الترمذي، الرقم: 206)[2]

Olemekezeka Ibn Abbas radiyallah anhuma akusimba kuti mthenga wa Allah (madalitso ndi ntendere zipite kwa iye) adati: Amene angapange Adhaan kwa zaka 7 moyera mtima ndimofuna malipiro kwa Allah munthu ameneyo akulandira lonjezo loti adzapulumutsidwa kumoto wa Gahena.

8. Mtumiki wathu Muhammad (salallah alayhi wasallama) adawapangira dua yachikhululuko anthu amene amapanga Adhaan.

عن أبى هريرة رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم الإمام ضامن والمؤذن مؤتمن اللهم أرشد الأئمة واغفر للمؤذنين (سنن أبي داود، الرقم: 517)[3]

Olemekezeka Abuu Hurairah (radiyallah anhu) akusimba kuti; Mtumiki (salallah alayhi wasallam) adanena kuti; Imaam ali ndi udindo (paswalah zonse zapagulu) ndipo muadhin ndi amene adasungitsidwa Nthawi. (iye adaptsidwa udindo oitanira anthu kumapemphero munthawi yake yolondola) “Ambuye Mulungu aongolereni ma imaam (kuti adzikwaniritsa ntchito yawo yopempheretsa swalah moyenerera) Ndiponso akhululukireni mamuazini (pazolakwitsa zawo).


[1]المستدرك على الصحيحين للحاكم، الرقم: ١٦٣، وإسناده صحيح كما قال الذهبي في التلخيص

[2]سنن الترمذي، الرقم: ٢٠٦، وسكت عنه الحافظ في الفصل الثاني من هداية الرواة (١/٣١٨) فلا تقل درجته عن الحسن عنده

[3]سنن أبي داود، الرقم: ٥١٧، وسكت عنه الحافظ في الفصل الثاني من هداية الرواة (١/٣١٨) فلا تقل درجته عن الحسن عنده

Check Also

Mawu A Iqaamah Komanso Njira Ya Sunnat Yopangira Iqaamah

1. Mawu a Iqaamah ndichimodzimodzi ndi azaana. Koma popanga iqaamah mukuyenera kunena kamodzikamodzi kupatula mawu …