Monthly Archives: September 2021

Kuyankhidwa Kwa Ma Duwa

Umar (radhwiyallahu anhu) akulongosora kuti: Duwa imakhala idakali pakati pa mitambo ndi nthaka (munlengalenga). Siimapititsidwa mpakana kumwamba ngati muduwamo simunawerengedwe Durood (kutanthauza kuti sipamakhala chitsimikizo cha kuyankhidwa kwa duwayo).

Read More »

Ubwino wa Muadhin

Adhaan ndi chimodzi mwazizindikiro za chisilamu, chisilamu chimalemekeza kwambiri anthu amene amapanga Adhaan, kuwaitanira anthu kuti adzaswali.Tsiku lachiweluzo anthu adzawasilira anthu amene ankachita adhaan padziko lino lapansi chifukwa cha ulemelero umene anthuwa adzakhale nawo. Ma hadith ochuluka alongosora za maubwino a muadhin ndi zabwino zimene akalandire patsikuli. 1. Muadhin adzakhala …

Read More »

Zikhulupiliro zokhudza mabukhu a Allah

5. Quran ndi bukhu lomaliza ndipo idavumbulutsidwa kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Kudzera mukuvumbulutsidwa kwa Quran mabukhu ena onse adachotsedwa. 6. Allah Ta’ala adatenga udindo oyiteteza Quran kufikira tsiku la Qiyaamah, kotero, palibe kusintha kapena kupungula kulikonse komwe kungachitike ku bukhu limeneri. Tidakali mkati molongosora za mabukhu olemekezeka, Allah adapeleka …

Read More »

Kuona Malo Ako Ku Jannah

Sayyiduna Anas (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “amene anganditumizire Durood ka 1000 tsiku lachisanu, sadzamwalira kufikira ataonetsedwa malo ake ku Jannah.”

Read More »

Zikhulupiliro zokhudza mabukhu a Allah

1. Allah Ta’ala adavumbulutsa mabukhu osiyanasiyana kwa aneneri osiyanasiyana (ntendere wa Allah upite kwa iwo)kuti adzawaongole anthu. Tauzidwapo za mabukhu amenewa mu Quran yolemekezeka komanso mma hadith ndipo za mabukhu ena sitinadziwitsidwe.[1] 2. Timakhulupilira mabukhu onse amene adavumbulutsidwa ndi Allah kwa atumiki onse monga m’mene adavumbulutsidwira. Ndipo sitimakhulupilira m’mabukhu amene …

Read More »

Mngelo amene amaima pa manda a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ndikumapeleka durood imene anthu apanga kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam)

Ammaar bin Yaasir (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adati: “Allah Ta’ala adasankha Mngelo oti akhale pambali pa manda a Mtumiki (sallallahu alaih wasallam), Mngelo amene Allah adampatsa nzeru zodziwa maina (mu hadith ina zanenedwa kuti adapatsidwa kuthekera kokunva mawu) a zolengedwa zomwe zikutanthauza kuti palibe munthu amene angandiwelengere duruud kufikira tsiku la Qiyaamah kupatula kuti (Mngeloyu) amafikitsa duruuduyo kwa ine pamodzi ndi dzina lamunthuyo ndilabambo ake (adzanena kuti) uyu ndi uje mwana wa uje yemwe wakuwerengera duruud.’’

Read More »

Salaat Ndi Salaam Zimufika Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasallam)

Sayyiduna Ibnu Abbaas (radhiyallahu anhuma) ulendo wina adati, “palibe munthu aliyense ochokera mu ummah wa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) amene amamufunira zabwino Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kupatula kuti Durood (imene anawerengayo) imafikitsidwa kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kudzera mwa angelo ndipo amauzidwa kuti munthu wakutiwakuti wakuwerengera Durood ndipo ujeni wakufunira zabwino pokuwerengera Durood.”

Read More »

Adhaan – Chiyambi Chake 1

Mtumiki (sallallahua alaih wasallam) atapanga Hijrah (atasamukira) kupita ku Madina Munawwarah adamanga nzikiti. Atamanga nzikiti adakambirana ndi ophunzira ake nkhani yopezera njira imene angamawaitanire anthu kuti adzaswali. Lidali Khumbo la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti anthu adzisonkhana ndikuswalira pamodzi munzikiti. Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sankasangalatsidwa kuti masahabah adzaswali aliyense payekha …

Read More »

Zikhulupiliro Zokhudza Angelo

10. Angelo amene amamufunsa munthu mafunso m’manda maina awo ndi Munkar ndi Nakiir.[1] ndipo mafunso omwe amafunsa ndi awa: a) Mbuye wako ndindani? b) Ungatiuze chani chokhuza Muhammad sallallah alaih wasallam? c) Chipembedzo chako ndi chiti?[2] 11. Mnsilamu aliyense ali ndi M’ngelo komanso shaitaan, M’ngelo amamulimbikitsa munthuyo kuchita zabwino ndipo …

Read More »