عن عمر بن الخطاب قال: إن الدعاء موقوف بين السماء والارض لا يصعد منه شيء حتى تصلي على نبيك صلى الله عليه وسلم (سنن الترمذي، الرقم: 486)
Umar (radhwiyallahu anhu) akulongosora kuti: Duwa imakhala idakali pakati pa mitambo ndi nthaka (munlengalenga). Siimapititsidwa mpakana kumwamba ngati muduwamo simunawerengedwe Durood (kutanthauza kuti sipamakhala chitsimikizo cha kuyankhidwa kwa duwayo).
Kuvala Buluku Lodutsa Timisomali
Suhail bin Hanzalah (radhwiyallahu anhu) ananenapo kuti:
Nthawi ina yake Rasulullaahi (sallallahu alaih wasallam) anakambapo nkhani yokhudzana ndi Khuraim (radhwiyallahu anhu) amene anali munthu wa mtundu wa chi Asadi kuti iyeyo ndi munthu wa bwino, koma zinthu ziwiri zimamuipitsa, ndipo zinthu zake ndi, amasungira tsitsi lake la m’mutu kuti litalike kwambiri komanso amalilekelera buluku lake kukhala laritali mpakana kufika m’misomali ya phanzi.
Pamene khuraim (radhwiyallahu anhu) anamva nkhani imeneyi anakayepula tsitsi lake malire m’makutu ndipo adayamba kukwezera buluku lake mpakana kufika cha muntunda mwa misomali ya m’miyendo. (Sunan Abi Dawood, #4089)