عن ابن عباس رضي الله عنهما قال: ليس أحد من أمة محمد يصلي على محمد أو يسلم عليه إلا بلغه يصلي عليك فلان ويسلم عليك فلان (مسند إسحاق بن راهويه، الرقم: ٩١١، ورجاله ثقات إلا أبا يحيى القتات، ففيه ضعف)
Sayyiduna Ibnu Abbaas (radhiyallahu anhuma) ulendo wina adati, “palibe munthu aliyense ochokera mu ummah wa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) amene amamufunira zabwino Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kupatula kuti Durood (imene anawerengayo) imafikitsidwa kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kudzera mwa angelo ndipo amauzidwa kuti munthu wakutiwakuti wakuwerengera Durood ndipo ujeni wakufunira zabwino pokuwerengera Durood.”
Ulemu wa Imaam Maalik (rahimahullah)
Imaam Maalik (rahimahullah) ankaukonda nzinda wa Madinah Munawwarah kwambiri, ankaukonda nzindawu chifukwa chomukonda Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kwambiri.
Allaamah Ibnu Khallikaan (rahimahullah) adalemba kuti:
Imaam Maalik (rahimahullah) sadakweleko chokwera munzinda olemekezeka wa Madinah Munawwarah. Ngakhale pamene adakalamba kufikira kuti adafooka kukanika Kuyenda chifukwa chokalamba, adasankha Kuyenda wapansi Kusiyana ndikukwera chokwera, Imaam Malik (rahimahullah) atafunsidwa kuti ndi chifukwa chiyani amachita zimenezi, iye adayankha kuti, zimandivuta Kuyenda mu nzinda wa Madinah ndiri pa chokwera kumachita kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adagonekedwa mu nthaka imeneyi yamunzinda wa Madinah. (Wafayatul Aayaan, 136/4)