Olemekezeka Jaabir (radhiyallah anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati "munthu amene angandiwerenge durood ka 100 kungotha kuswali swalah a ya Fajr asadayankhule, Allah adzamukwaniritsira zosowa zake zokwana 100, Allah adzafulumizitsa kukwaniritsa zosowa zake zokwana 30 (padziko pomwe pano) ndiponso Allah adzamusungire kukwaniritsa kwa zosowa zina zokwana 70 ku nkhokwe zake kuti adzampatse pa tsiku lachiweruzo, chimodzi modzinso kwa yemwe angawerenge durood ka 100 kutha kwa swalah ya Maghrib (kutanthauza kuti adzalipidwanso mofanana) "maswahaba (radhiyallahu anhum) adafunsa," tidzikuwerengerani bwanji Durood oh Mthenga wa Allah" Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adawauza maswahabah kuti adziwerenga Durood iyi:
Read More »Yearly Archives: 2022
Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama (qurbaani)
17. Mukuyenera kuigoneka nyama yanu chakumanzere kwanu itayang'ana ku Qiblah.
Olemekezeka Anas (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adazinga ndi manja akenkhosa ziwiri yakuda ndiyoyera komanso zokhala ndi minyanga uku akuwerenga Tasmiyah ndi Takbeer ndipo adaika mwendo wake m'mbali mwake (chinyamacho chidagonekedwa chakumanzere ndicholinga choti chiyang'ane ku Qiblah).
Read More »Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama (qurbaani) 3
Olemekezeka Aliyy (radhiyallahu anhu) akusimba kuti tsiku la Idi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adamuuza bibi Faatimah (radhiyallahu anha) uchitire umboni pamene chinyama chako chikuzingidwa (uwonelere). Pamene dontho la magazi oyamba likugwa pansi machimo akonso amakhululukidwa, nyama ndi magazi ake zidzaikidwa pasikelo ya ntchito zako zabwino ndikuchulukitsidwa ka 70, Abu Sa'eed khudri (radhiyallahu anhu) adamufunsa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti, Oh Mthenga wa Allah kodi malipilo amenewa adzapelekedwa kwa akubanja lanu lokha chifukwa banja lanu limatchuka ndikukhala ndi madalitso kapena sawabu zimenezi ndi za asilamu onse? Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adayankha nati zavumbulutsidwa kwa akubanja langa komano sawabu zake ndi za nsilamu wina aliyense.
Read More »Kuwerenga Durood kokwana ka 10 mmawa ndi madzulo
Olemekezeka Abu Darda (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, munthu amene angawelenge Durood kokwana ka 10 mmawa ndi madzulo adzapeza nawo chiombolo changa pa tsiku lachiweruzo.
Read More »Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama (qurbaani) 2
6.Ndi sunnah osadya chinachirichonse kummawa kwa tsiku la Eidul Adha kufikira mpakana utabwerako ku swalah ya Eid.
Sayyiduna Buraidah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti tsiku la Eidul Fitr Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sankapita kukaswali Eid pokhapokha atadya kenakake, koma tsiku la Eidul Adha sankadya kalikonse pokhapokha atabwerako (kuchokera ku swalah ya Eidul Adha, akabwera ko koswali chinthu choyambilira kudya chinkakhala chiwindi cha nyama yomwe anazinga).
Read More »Tafseer Ya Surah ‘Aadiyaat
Ndikulumbilira akavalo othamanga ali ndi phuma, Ndi otulutsa moto ku zikhotwa (pomenyetsa miyendo m'miyala), Ndi othira nkhondo adani m'mawa (dzuwa lisadatuluke), Ndi kuulutsa fumbi lambiri (kwa adani) nthawi imeneyo, Ndikulowelera mkatikati mwa adani. Ndithu munthu ali okanira mbuye wake (sathokoza Allah pa zimene amdalitsa nazo). Ndithudi iye pa zimenezi ndi mboni (yodzichitira yekha kupyolera mzochitachita zake). Ndipo ndithu iye ndi okonda chuma kwambiri (ndiponso ngwansulizo). Kodi sakudziwa zikadzatulutsidwa za mmanda, Ndikudzasonkhanitsidwa ndikuonekera poyera zomwe zidali m'mitima? Ndithu tsiku limenelo Mbuye wawo adzawadziwa kwambiri (ndikuwalongosolera zonse zochita zawo).
Read More »Tembelero la Jibril (alaihis salaam) komanso Mtumiki Muhammad (sallallah alaih wasallam)
Hazrat Ka'b bin Ujra (radhiyallahu anhu) akulongosora nkhani iyi: tsiku lina lake Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adaitana maswahabah onse (radhiyallahu anhum) "tabwerani ku mimbar" titakhala moyandikira mimbari, Mtumiki sallallahu alaih wasallam adakwera thanthi (sitepe) yoyamba ndipo anatulutsa mawu onena kuti "Aameen" kenako adakweranso thanthi yachiwiri ndi kuyankhulanso kuti "Aameen" adakweranso yachitatu ndikunena mawu omwe aja onena kuti "Aameen", atamaliza kupereka Khutbah ndikutsika pa Mimbari paja tidamufunsa kuti, Oh Mthenga wa Allah, takumvani mukuyankhula mawu omwe sitinakumvenipo ndikale lonse mukuyankhula, (komwe ndikuyankhula mawu oti Aameen mpaka katatu pokwera mimbari)
Read More »Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama(qurbaani)
1. Qurbaani ndi sunna yomwe ili yaikulu kwambiri komanso ubembedzi wapamwamba kwambiri mu Deen. Mu Quraan yotamandika, zatchuridwa mwapaderadera zokhudzana ndi Qurbaani, komanso maubwino ochuluka ndi kufunikira kwake zalimbikitsidwa mma hadeeth a olemekezeka Rasulullaah (sallallahu alaihi wasallam). Allah ta’ala wanena kuti لَن يَنَالَ اللَّـهَ لُحُومُهَا وَلَا دِمَاؤُهَا وَلَـٰكِن …
Read More »Masunnah Ochita Mumzikiti
6. Werengani maduwa pamene mukupita kumzikiti. Ena mwa maduwawo ndi awa:
Dua yoyamba
Amene angawerenge duwa iyi pamene akunyamuka ulendo wakumzikiti amakhala ndichifundo cha Allah chapadera ndiponso angelo okwanira 70,000 amamuchitiranso maduwa.
Read More »Masunnah Ochita Mumzikiti
4. Pitani kumzikiti modekha ndi mwa ulemu. musapite mukuthamanga.
Olemekezeka Abu Hurayrah (radhiyallah anhu) adati; ndinamumva Mtumiki wa Allah (sallallah alayhi wasallam) akunena kuti; Pamene iqqamah yachitidwa, musapite kukapemphera swala pamene mukuthamanga, Mmalo mwake, Mukuyenera kuyenda modekha ndi mwaulemu. Gawo laswalah limene mwalipeza ndi Imaam, pempherani. Ndipo gawo lomwe lakudutsani kwanirisani. (pamene imaam watsiriza swalah)
Read More »