عن أبي الدرداء قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من صلى علي حين يصبح عشرا وحين يمسي عشرا أدركته شفاعتي يوم القيامة (رواه الطبراني بإسنادين وإسناد أحدهما جيد ورجاله وثقوا كذا في مجمع الزوائد، الرقم: ١٧٠٢٢)
Olemekezeka Abu Darda (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, munthu amene angawelenge Durood kokwana ka 10 mmawa ndi madzulo adzapeza nawo chiombolo changa pa tsiku lachiweruzo.
Maswahabah (radhiyallahu anhum) kutsatira sunnah yodalitsika ya Mtumiki Muhammad (sallallahu alaih wasallam) pa chinachirichonse
Tsiku lina munthu wina wake adati kwa Ibnu Umar (radhwiyallahu anhu) “Allah watchula mu Qur’an nkhani yokhudza salaah pa mtendere komanso swalah ukakhala ndi mantha, koma sananeneko za swalah ukakhala pa ulendo”
Ibnu Umar radhiyallahu anhuma adayankha nati “oh mphwanga, Allah adatumiza Muhammad (madalitso ndi mtendere zipite kwa iye) ngati Mtumiki wake kwa ife pamene tidali mbuli ndipo sitinkadziwa chirichonse, tikuyenera kumutsatira chinachirichonse chomwe adachita.”
Zindikirani :Shaikh Zakariyya Kandhelwi (rahimahullah) adati, Izi zikutanthauza kuti sikuti lamulo lirilonse likupezeka mu Qur’an. Umoyo wa Mtumiki (madalitso ndi mtendere zipite kwa iye) komanso ntchito zake ndi chiongoko kwa ife tikadzitsatira. Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati “ndapatsidwa Qur’an yolemekezeka komanso malamulo ena. Samalani nyengo ndi nthawi yomwe ili nkudza posachedwapa, pomwe anthu osasamala malamulo adzakhale m’mipando yawo ya wofuwofu uku akuyankhula kunena kuti” Gwiritsitsani Qur’an yokha, tsatirani malamulo okhawo omwe a kupezeka mmene momo. (Fadaile Amaal, Pg, 106)