Kuwerenga Durood ka 100 pa Fajr ndi Maghrib

عن جابر رضي الله عنه قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من صلى علي مائة صلاة حين يصلي الصبح قبل أن يتكلم قضى الله تعالى له مائة حاجة يعجل له منها ثلاثين ويدخر له سبعين وفي المغرب مثل ذلك قالوا: وكيف الصلاة عليك يا رسول الله قال: إن الله وملائكته يصلون على النبي يأيها الذين آمنوا صلوا عليه وسلموا تسليما اللهم صل على محمد حتى تعد مائة (رواه أحمد بن موسى الحافظ بسند ضعيف كذا في القول البديع صـ 364)

Olemekezeka Jaabir (radhiyallah anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati “munthu amene angandiwerenge durood ka 100 kungotha kuswali swalah a ya Fajr asadayankhule, Allah adzamukwaniritsira zosowa zake zokwana 100, Allah adzafulumizitsa kukwaniritsa zosowa zake zokwana 30 (padziko pomwe pano) ndiponso Allah adzamusungire kukwaniritsa kwa zosowa zina zokwana 70 ku nkhokwe zake kuti adzampatse pa tsiku lachiweruzo, chimodzi modzinso kwa yemwe angawerenge durood ka 100 kutha kwa swalah ya Maghrib (kutanthauza kuti adzalipidwanso mofanana) “maswahaba (radhiyallahu anhum) adafunsa,” tidzikuwerengerani bwanji Durood oh Mthenga wa Allah” Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adawauza maswahabah kuti adziwerenga Durood iyi:

إِنَّ الله وَمَلئِٰكَتَهُ يُصَلُّوْنَ عَلٰى النِّبِيِّ يٰأَيُّهَا الَّذِيْنَ آمَنُوْا صَلُّوْا عَلَيْهِ وَسَلِّمُوْا تَسْلِيْمًا اَللّٰهُمَّ صَلِّ عَلٰى مُحَمَّد

Olemekezeka Waail radhiyallahu anhu ameta tsitsi lake

Waail (radhiyallahu anhu) akusimba kuti :

Tsiku lina ndidapita kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kukamuyendera pamenepo ndikuti tsiku langa litatalika kwambiri, ndiri chikhalire ndi iye adayankhula mawu oti, “Zubaab,Zubaab” (omwe akutanthauza kuti China chake choipa) ndinaganiza kuti akunena tsitsi langa, ndidabwelera kunyumba ndikumeta tsitsi langa mwachangu. Tsiku lotsatira nditakamuonanso adati, sindimatanthauza tsitsi lako poyankhula mawu amene aja dzulo, komano wachita bwino kumeta tsitsi lako.

Zomwe adachita sahabi ameneyu pamenepa zikungowonetseratu chikondi chenicheni chomwe adalinacho mu mtima mwake pa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam). Sadatenge nthawi poganiza kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sadasangalatsidwe ndi tsitsi lake lalitali, mwachanguchangu adameta tsitsi lake. Wina atha kungoona kuti ichhi ndi chikondi chimene maswahabah adali nacho, kugoganizira chabe kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) wakhumudwa zinkawasowetsa mtendere, kodi pali kuthekera koti akadatha kuphwanya lamulo la Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kapena kutsutsana ndi Sunnah yake? (Sunan Abi Dawood, #4190)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …