17. Mukuyenera kuigoneka nyama yanu mbali yakumanzere kwanu itayang’ana ku Qiblah.
عن أنس قال ضحى رسول الله صلى الله عليه وسلم بكبشين أملحين أقرنين ذبحهما بيده وسمى وكبر ووضع رجله على صفاحهما (صحيح البخاري، الرقم: 5565)
Olemekezeka Anas (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adazinga ndi manja akenkhosa ziwiri yakuda ndiyoyera komanso zokhala ndi minyanga uku akuwerenga Tasmiyah ndi Takbeer ndipo adaika mwendo wake m’mbali mwake (chinyamacho chidagonekedwa chakumanzere ndicholinga choti chiyang’ane ku Qiblah).
18. Simukufunika kuyamba kuchotsa chikopa pokhapokha chitamalizika kufa.
19. Pamene mukuzinga muwerenge Takbeer motere:
بسم الله الله أكبر
Bismillaahi Allahu Akbar
Mdzina la Allah mwini chifundo mwini chisoni chosatha, Allah ndi wankulu.
20. Musadayambe kuzinga mudzawerenga Dua iyi:
إنِّي وَجَّهْتُ وَجْهِيَ لِلَّذِي فَطَرَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ عَلَى مِلَّةِ إِبْرَاهِيمَ حَنِيفًا وَمَا أَنَا مِنَ الْمُشْرِكِينَ
إنَّ صَلَاتِي وَنُسُكِي وَمَحْيَايَ وَمَمَاتِي لِلَّـهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ لَا شَرِيكَ لَهُ وَبِذَلِكَ أُمِرْتُ وَأَنَا مِنَ الْمُسْلِمِينَ اللهُمَّ مِنكَ وَ لَكَ
Ndatembukira nkhope yanga kwa yemwe adalenga kumwamba ndi dziko lapansi pamene ndiri mnjira yoongoka ya Ibrahim (alaihis salaam) ndipo sindiri mgulu la ma Mushrikiin. Ndithu mapemphelo anga, Nsembe yanga, moyo wanga ndi imfa yanga ndi za Allah mbuye wa zolengedwa zonse, alibe ophatikizana naye, pa zimenezi ndalamuridwa kutero ndipo ndiine m’modzi wa asilamu. Oh Allah! Nsembe iyi ndiinu amene amene mwatipangitsa kuti tikwanitse ndipo ndi yanu.
عن جابر بن عبد الله رضي الله عنه قال ذبح النبى صلى الله عليه وسلم يوم الذبح كبشين أقرنين أملحين موجئين فلما وجههما قال إنى وجهت وجهى للذى فطر السموات والأرض على ملة إبراهيم حنيفا وما أنا من المشركين إن صلاتى ونسكى ومحياى ومماتى لله رب العالمين لا شريك له وبذلك أمرت وأنا من المسلمين اللهم منك ولك عن محمد وأمته باسم الله والله أكبر ثم ذبح. (سنن أبي داود، الرقم: 2797)
Jaabir (radhiyallah anhu) akusimba kuti tsiku la Qurbaani Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adazinga nkhosa ziwiri yakuda ndi yoyera komanso zokhala ndi minyanga pamene Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adaigoneka kuti aizinge adawerenga Dua iyi:
إنِّي وَجَّهْتُ وَجْهِيَ لِلَّذِي فَطَرَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ حَنِيفًا وَمَا أَنَا مِنَ الْمُشْرِكِينَ
إنَّ صَلَاتِي وَنُسُكِي وَمَحْيَايَ وَمَمَاتِي لِلَّـهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ لَا شَرِيكَ لَهُ وَبِذَلِكَ أُمِرْتُ وَأَنَا مِنَ الْمُسْلِمِينَ اللهُمَّ مِنكَ وَ لَكَ
21. Zanenedwa mmahadith kuti ntchito yabwino imene imachitika pa tsiku la Qurbaani ndiko kuzinga nyama. Koma Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adanena kuti ntchito imene ili ndi sawabu zambiri ndiye kugwirizanitsa ubale. Kotero kumpatikiza kuzinga chinyama tikuyeneranso kumanga ubale.
عن ابن عباس رضي الله عنهما قال قال رسول الله صلى الله عليه و سلم في يوم أضحى ما عمل آدمي في هذا اليوم أفضل من دم يهراق إلا أن يكون رحما مقطوعة توصل (المعجم الكبير للطبراني، الرقم: 10948)
Ibnu Abbaas (radhiyallahu anhuma akulongosora kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) pa Eid adanena kuti:”Palibe ntchito yabwino yomwe kapolo angachite pa tsiku limeneli yokhala ndi malipiro ambiri kuposa kukhetsa mwazi (Qurbaani) kupatula munthu amene angaluzanitse anthu awiri omwe anali pa udani.