Ma sunna ndi miyambo ya nsembe ya kuzinga nyama (qurbaani) 2

6.Ndi sunnah osadya chinachirichonse kummawa kwa tsiku la Eidul Adha kufikira mpakana utabwerako ku swalah ya Eid.

عن ابن بريدة عن أبيه رضي الله عنه أن رسول الله صلى الله عليه و سلم كان لا يخرج يوم الفطر حتى يأكل . وكان لا يأكل يوم النحر حتى يرجع (سنن ابن ماجة، الرقم 1756)

Sayyiduna Buraidah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti tsiku la Eidul Fitr Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sankapita kukaswali Eid pokhapokha atadya kenakake, koma tsiku la Eidul Adha sankadya kalikonse pokhapokha atabwerako (kuchokera ku swalah ya Eidul Adha, akabwera ko koswali chinthu choyambilira kudya chinkakhala chiwindi cha nyama yomwe anazinga).

7. Pambuyo pobwerako (kuchokera koswali) chinthu choyambilira kudya izikhala nyama yomwe anazinga (popeza chimenechi ndi chakudya chomwe Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankayambilira kudya akabwerako koswali).

حدثني عبد الله بن بريدة، عن أبيه قال: كان رسول الله صلى الله عليه وسلم لا يغدو يوم الفطر حتى يأكل، ولا يأكل يوم الأضحى حتى يرجع فيأكل من أضحيته (مسند أحمد 38/ 88) وفي رواية البيهقي وكان إذا رجع أكل من كبد أضحيته (السنن الكبرى للبيهقي، الرقم 6161)

Hazrat Buraidah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti tsiku la Eidul Fitr Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) sankapita kukaswali Eid pokhapokha atadya kenakake, koma tsiku la Eidul Adha sankadya kalikonse pokhapokha atabwerako (kuchokera ku swalah ya Eidul Adha, ko koswali chinthu choyambilira kudya chinkakhala chiwindi cha nyama yomwe anazinga).

Mu hadith ya Baihaqi zanenedwa kuti chakudya choyambilira chomwe Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ankadya chinkakhala chiwindi cha nyama yomwe inazingidwa ngati nsembe.

8. Sizoloredwa kuti munthu asale kudya mmasiku monga pa 10,11, 12 ndi pa 13 Dhul-Hijjah.

عن نبيشة الهذلي رضي الله عنه قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم أيام التشريق أيام أكل وشرب وذكر الله (صحيح مسلم، الرقم: 1141، مسند أحمد، الرقم: 20722)

Zanenedwa kuchokera kwa Nubaish (radhiyallahu anhu) kuti Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adati, “masiku a Tashriiq ndi masiku odya chakudya, kumwa ndikumbukira Allah”.

9. Wina aliyense akuyenera kuyesetsa m’mene angakwanitsire kugula chinyama chabwino (chapamwamba/chodulirako) komanso chathanzi, ndipo motengera ndi kulongosora kwa chinyama ndi mmeneso adzapezere sawabu (malipiro).

عن عائشة وعن أبي هريرة أن رسول الله صلى الله عليه و سلم كان إذا أراد أن يضحي اشترى كبشين عظيمين أقرنين أملحين موجوءين . فذبح أحدهما عن أمته لمن شهد لله بالتوحيد وشهد له بالبلاغ . وذبح الآخر عن محمد وعن آل محمد صلى الله عليه و سلم (ابن ماجة رقم 3122)

Aishah (radhiyallah anha) komanso Abu Hurairah (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) akafuna kupha chinyama cha Qurbaani ankagula nkhosa ziwiri zazikulu, zokhala ndi nyanga, yakuda ndi yoyera. Ankazinga imodzi mmalo mwa ummah wake (omwe umakhulupilira umodzi wa Allah komanso kuti Muhammad (sallallahu alaih wasallam) ndi Mthenga wake) ndipo inayo amazizingira yekha ndi akubanja kwake(kutanthauza kuti sawabu za chinyama choyamba zimapita kwa ummah wake onse ndipo nyama yachiwiriyo sawabu zake zimapita kwa iye mwini ndi akubanja kwake)

10. Ziri Mustahabb kuchinenepetsa chinyama cha nya Qurbaani pochidyetsa bwino.

قال يحيى بن سعيد سمعت أبا أمامة بن سهل قال كنا نسمن الأضحية بالمدينة وكان المسلمون يسمنون (صحيح البخاري، الرقم 5553)

Olemekezeka Yahya bin Sa’eed rahmatullah alaih akufotokoza kuti adamumva Abu Umaamah (radhiyallahu anhu) akunena kuti ndinkakonda kuzinenepetsa nyama zathu za Qurbaani ku Madinah Tayyibah ndipo asilamu onse ( maswahabah) ankachita chimodzimodzi.


 

Check Also

Chikondi Cha Sayyiduna Abu Bakr (radhwiyallahu anhu) Kumukonda Nabi (sallallahu alaih wasallam)

Nabi (sallallahu alaih wasallam) adawuyamba nsamuko pamodzi ndi Abu Bakr (radhwiyallahu) anhu chakumadzulo, nkatikati mwa …