Monthly Archives: December 2023

Mtsutso Wa Pakati Pa Nabi Ebrahim (alaihis salaam) Ndi Namruud

Namrud idali mfumu yopondereza komanso yankhanza imene inkanena kuti iye ndi mulungu ndipo inkalamula anthu kuti adzimulambira. Nabi Ebrahim (alaihis salaam) atapita kwa Namrud ndikumuitanira ku umodzi wa Allah, Namrud chifukwa cha kudzikweza kwake ndi kukakamira kwake, sadavomere ndipo adafunsa Nabi Ebrahim (alaihis salaam) kuti angachite chiyani Mbuye wake. Nabi …

Read More »

Ubwino Owerenga Quraan Majeed 2

Mngelo Kuteteza Mphotho Sayyiduna Ali (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Munthu akagwiritsa ntchito miswaak kenako n’kuimirira kuswali, mngelo amaima pambuyo pake ndikumvetsera kuwerenga kwake Qur’an Majiid. Kenako mngeloyo amayandikira kwa iye mpaka kukumanitsa pakamwa pake ndi pakamwa pake (pa owerengayo). gawo lilichonse la Qur’an Majiid lomwe …

Read More »

Chilungamo cha Ali (radhwiyallahu ‘anhu)

Ali bun Rabii’ah akusimba kuti nthawi ina Ja’dah bin Hubairah (radhwiyallahu ‘anhu) adadza kwa Ali (radhwiyallahu ‘anhu) nati: “E inu Amiir-ul-Mu’miniin! Anthu awiri akabwera kwa inu (ndi mkangano wawo) Mmodzi mwa awiriwo amakukondani kwambiri kuposa banja lake ndi chuma chake, pomwe winayo ndi woti akadakhoza kukuphani, akadachita. choncho (chifukwa cha …

Read More »

Ubwino Owerenga Quraan Majeed

Muuni Padziko Lapansi ndi chuma cha tsiku lachiweluzo Abu Zarr (radhwiyallahu anhu) anati: “Nthawi ina ndinamufunsa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) kuti, ‘E, Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam), chonde ndipatseni malangizo.” Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) anayankha: “Igwiritsitse taqwa; Adati: “E, Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam), chonde ndipatseninso malangizo ena.” Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) …

Read More »

Kukonda Kwambiri kwa Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) kumukonda Ali (radhwiyallahu ‘anhu)

Sayyiduna Ali (radhwiyallahu ‘anhu) akuti: Nthaŵi ina yake ndinadwala. Ndikudwala choncho Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) anabwera kudzandiona. Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) atalowa mnyumba mwanga, ndinali nditagona. Atandiwona momwe ndinaliri Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adadza pafupi nane ndipo adavula nsalu yomwe adavala ndikunsifundika nayo. Kenako Rasulullah (swallallaahu …

Read More »