Sayyiduna Ali (radhwiyallahu ‘anhu) akuti:
Nthaŵi ina yake ndinadwala. Ndikudwala choncho Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) anabwera kudzandiona. Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) atalowa mnyumba mwanga, ndinali nditagona. Atandiwona momwe ndinaliri Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adadza pafupi nane ndipo adavula nsalu yomwe adavala ndikunsifundika nayo. Kenako Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ataona kufooka kwanga, adayimilira, napita ku nzikiti ndikukaswali swalah za nafl, atamaliza adampempha Allah Taala kuti andidalitse ndi shifa (kuchila).
Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adadza kwa ine, nandivula nsalu yake ija ndikundiuza kuti: “Imirira, iwe mwana wa Abu Taalib! Wachira!” Ndinaimirira momwemo, ndipo ndinadzipeza kuti ndachira kotheratu. Ndinadzipeza ndili mu thanzi loti panalibe chizindikiro cha matenda kapena kufooka komwe kunatsala m’thupi langa.
Kenako Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Nthawi zonse ndikamapempha kwa Allah Ta’ala, Amandilandira du’aa yanga ndikundipatsa zomwe ndidapempha. Ndinakupempheranso, (kuphatikiza shifa yako). (Fazaa’l-ul-Khulafaa li-Abi Na’aim #78)
Kuchokera munkhaniyi, tikuona chikondi chachikulu chomwe Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adali nacho pa Ali (radhwiyallahu ‘anhu). Momwemonso tikumvetsa kuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adatiphunzitsa kudzera mu zochita zake zodalitsika kuti tikadwala, titembenukire kwa Allah Ta’ala pomupempha shifaa, popeza chilichonse chili mkati mwa ulamuliro ndi mphamvu za Allah Ta’ala.