binary comment

Ubwino Owerenga Quraan Majeed 2

Mngelo Kuteteza Mphotho

Sayyiduna Ali (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Munthu akagwiritsa ntchito miswaak kenako n’kuimirira kuswali, mngelo amaima pambuyo pake ndikumvetsera kuwerenga kwake Qur’an Majiid. Kenako mngeloyo amayandikira kwa iye mpaka kukumanitsa pakamwa pake ndi pakamwa pake (pa owerengayo). gawo lilichonse la Qur’an Majiid lomwe amaliwerenga limatetezedwa m’mimba mwa Mngelo (ndipo kenako limatetezedwa ndi Allah). Choncho, onetsetsani kuti mwayeretsa mkamwa mwanu musanawerenge Qur’an Majeed.[1] 

Allah Ta’ala Kumvetsera mwansangala munthu Amene akuwerenga Qur’an

Sayyiduna Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Allah samvetsera kalikonse (mosangalala kwambiri) monga momwe amamvetselera Nabii okhala ndi mawu okongola yemwe akuwerenga Qur’an mokweza.[2] 

Maduwa kuyankhidwa pa kutha kuwerengedwa kwa Qur’an

Hazrat Ubaidah ibn Saariyah radhwiyallahu anhu akunena kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) anati: “Amene waswali swalah yake (motsatira lamulo) duwa yake idzayankhidwa, yemweso watsiriza kuwerenga Quran ali mwayi oyankhidwa Dua yake.[3] 

Angelo Opemphera Chikhululuko Kwa Yemwe Wamaliza Qur’an

Sa’d bin Abi Waqqaas (radhwiyallahu anhu) adati: “Munthu akamaliza kuwerenga Qur’an madzulo, angero amamupemphera chikhululuko kwa Allah mpaka m’bandakucha, ndipo akamaliza kuwerenga Qur’an m’bandakucha, angelo amamupemphera chikhululuko mpaka m’bandakucha. usiku”[4] 


[1] مسند البزار، الرقم: 550، وقال العلامة الهيثمي رحمه الله في مجمع الزوائد، الرقم: 2564: رواه البزار ورجاله ثقات وروى ابن ماجه بعضه إلا أنه موقوف وهذا مرفوع

[2] صحيح البخاري، الرقم: 7544

[3] المعجم الكبير للطبراني، الرقم: 647، وقال العلامة الهيثمي رحمه الله مجمع الزوائد، الرقم: 11712: رواه الطبراني، وفيه عبد الحميد بن سليمان وهو ضعيف

[4] سنن الدارمي، الرقم: 3526 وقال: هذا حسن عن سعد

Check Also

Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 7

17. Nkosaloredwa kwa munthu yemwe ali ndi Janaabah kapena mkazi wa Haidh kuwerenga Quraan Majiid. …