9. Werenganinso ayah zitatu zomaliza za Surah Baqarah musanagone. Kwanenedwa kuti Ali (Radhwiyallahu anhu) adati: “Sindikuganiza kuti aliyense wanzeru angagone popanda kuwerenga ma aya (atatu) omaliza a Surah Baqarah, chifukwa ndithu iwowo ndi chuma chochokera pansi pa Arsh. 10. Werengani Surah Faatihah ndi Surah Ikhlaas musanagone. Anas (Radhwiyallahu anhu) akusimba …
Read More »Surah Zokhala ndi nthawi zake zowerenga komanso nthawi zake zosiyanasiyana zomwe zikuyenera kuwerenga 3
6. werengani Surah Sajdah musanagone. Olemekezeka Jaabir (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) sankagona mpaka atawerenga Surah Sajdah ndi Surah Mulk.[1] Khaalid bin Ma’daan rahimahullah, Taabi’ee, adatchula izi: “Ndithu Surah Sajdah idzakangana m’manda poteteza amene ankaiwerenga. Idzati, ‘O, Allah! Ngati ndili ochokera ku chitaab Chanu, muvomereni chiwombolo changa …
Read More »Surah Zokhala ndi nthawi zake zowerenga komanso nthawi zake zosiyanasiyana zomwe zikuyenera kuwerenga 2
4. Werengani Surah Yaasiin m’mawa ndi madzulo aliwonse. Ibnu Abbaas (Radhwiyallahu anhu) adati: “Amene angawerenge Surah Yaasiin m’bandakucha, ntchito yake ya tsiku lonse idzafewetsedwa, ndipo amene angaiwerenge madzulo, ntchito yake mpaka m’mawa idzafewetsedwa.”[1] Olemekezeka Jundub (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) anati: “Amene angawerenge Surah Yaasiin usiku ndi …
Read More »Surah Zokhala ndi nthawi zake zowerenga komanso nthawi zake zosiyanasiyana zomwe zikuyenera kuwerenga
Pali Surah zina zomwe zalamuridwa kuti ziziwerengedwa nthawi yodziwika usiku ndi usana kapena masiku ena a sabata. Ndi mustahab kwa munthu kuwerenga ma surah amenewa mu nthawi yake yoikidwa. 1. Werengani Surah Kaafiroon musanagone. Olemekezeka Jabalah bun Haarithah (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (Swallallah alaihi wasallam) adati: “Ukamakagona, werenga Surah …
Read More »Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 10
23. Ngati mudaloweza pamtima gawo lina lake la Qur’an Majiid, onetsetsani kuti mukulibwereza nthawi zonse kuti musaiwale. Hadith yachenjeza za kunyalanyaza kuwerenga Quraan ndi kuiwala zomwe waloweza pamtima.[1] Olemekezeka Abu Musah Ash’ari (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah Adati: “Isamareni Qur’an Majiid. Ndikulumbirira Amene m’manja Mwake muli moyo wanga, (Qur’an Majiid) …
Read More »Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 9
21. Mukamaliza kuwerenga Qur’an yonse mpaka kukafika Surah Naas, zili mustahab kuti muyambirenso kuwerenga poyambiranso ndi Surah Faatihah ndi aya zoyambira za Surah Baqarah mpaka ulaaika humul muflihuun. 22. Mukamaliza kuwerenga Quraan yonse, werengani dua iyi: اَللّٰهُمَّ ارْحَمْنِيْ بِالْقُرْآنْ وَاجْعَلْهُ لِيْ إِمَاماً وَّهُدًى وَّرَحْمَةً اَللّٰهُمَّ ذَكِّرْنِيْ مِنْهُ مَا نَسِيْتُ وَعَلِّمْنِيْ …
Read More »Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 8
19. Ngati mukufuna kusintha zobvala zanu m’chipinda chosungiramo Quraan Majiid, muyenera kuika kaye Qur’an Majiid m’kabati, m’dilowa ndi zina zotero musanavule. Kuvula pamaso pa Quraan Majiid ndikotsutsana ndi ulemu wa Quraan Majiid. 20.Ngati ukuwerenga ndime ya Sajdah kapena kuimvera ikuwerengedwa, zidzakhala Waajib (zokakamizidwa) kwa iwe kuchita Sajdah. Kapangidwe ka sajdah-e-tilaawat …
Read More »Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 7
17. Nkosaloredwa kwa munthu yemwe ali ndi Janaabah kapena mkazi wa Haidh kuwerenga Quraan Majiid. Komabe, zikuloredwa kwa iwo kuwerenga ma Aayaah omwe ali mu Quraan Majiid omwe ndi ma dua (mapempho) kwa Allah komanso Aayaah omwe amawerengedwa kuti udziteteze ku ma shayaatiin, zoipa, ndi zina zotero. Akamawerenga ma Aayaah …
Read More »Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 6
14. Pamene mwatanganidwa ndi kuwerenga Qur’an Majiid, onetsani chidwi chanu pa Qur’an Majiid. Musatanganidwe ndi zokambirana zapadziko lapansi pakati panu mkatikati mowerenga, makamaka pamene Quraan ili yovundukura. Ngati pakufunika kuyankhula, ndiye kuti mutsirize Aayah yomwe mukuiwerengayo, mutseke Quraan mwaulemu, kenako yankhulani. Zanenedwa kuti Ibnu Umar (radhwiyallahu anhuma) akamawerenga Qur’aan Majiid, …
Read More »Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 5
13. Iwerengere Qur’an Majeed momveka bwino. Komabe, muyenera kupewa kutengera nyimbo ndi njira za oimba, ndi zina zotero. Baraa bin Aazib (Radhwiyallah anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) anati: “Kongoletsani (kuwerenga kwanu) Qur’an Majeed kudzera m’mawu anu (poiwerenga momveka bwino). Huzaifah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) …
Read More »