Mtsutso Wa Pakati Pa Nabi Ebrahim (alaihis salaam) Ndi Namruud

Namrud idali mfumu yopondereza komanso yankhanza imene inkanena kuti iye ndi mulungu ndipo inkalamula anthu kuti adzimulambira.

Nabi Ebrahim (alaihis salaam) atapita kwa Namrud ndikumuitanira ku umodzi wa Allah, Namrud chifukwa cha kudzikweza kwake ndi kukakamira kwake, sadavomere ndipo adafunsa Nabi Ebrahim (alaihis salaam) kuti angachite chiyani Mbuye wake.

Nabi Ibrahim (alaihis salaam) adati kwa Namrud: “Mulungu ndi Yemwe amapereka moyo ndi imfa.” Namrud, posadziwa zenizeni za kupereka moyo ndi kubweretsa imfa, mopusa anayankha kuti, “Inenso ndili ndi mphamvu zopatsa moyo ndi imfa!”

Pofuna kutsimikizira zonena zake, anaitanitsa anthu awiri omwe anaweruzidwa kuti aphedwe ndipo analamula kuti mmodzi aphedwe ndipo winayo amasuridwe n’kuloledwa kukhala ndi moyo.

Namrud analephera kuzindikira kuti zimatanthauza chani akamati kupereka moyo ku chinthu chopanda moyo, kumatanthauza kuika mzimu mkati mwake ndikuuchotsa kumoyo wosakhalapo n’kukhalapo.

Chimodzimodzinso, iye analephera kumvetsa kuti kuchititsa imfa kwa chamoyo kumatanthauza kuchotsa moyo m’thupi (ngakhale kuti kuchititsa imfa kwa chamoyo kumatanthauza kuchotsa moyo m’thupi).

Poona kuti lingaliro silinathe kulowa m’mutu wa Namrud, Nabi Ebrahim (alaihis salaam) anaganiza zosintha mtsutso wake ndikupereka mfundo otsatirayi.

Adati: “Mulungu wanga ndi Yemwe amatulutsira Dzuwa kuchokera Kum’mawa ndikulilowetsa kuzambwe. E, iwe Namrud! Ngati ukudzitcha kuti ndiwe Mulungu, bwanji osayesa kutembenuza mayendedwe ake ndi kulipangitsa Dzuwa kuti lilowere kotulukira kuchokera kumadzulo ndi kukhala kummawa?”

Mtsutso uwu udali woti Namrud adalephera kuyankha ndipo adangoti kakasi komanso adalibe chonena.

Mwanjira imeneyi, m’bwalo la mtsutso, Nabi Ibrahim (alaihis salaam) adamugonjetsa Namrud natsimikiza kuti Allah yekha ndiye ali ndi mphamvu pa chinthu chilichonse ndipo Allah yekha ndiye woyenera kupembedzedwa.”

Check Also

Mariziq Ali M’manja Mwa Allah Yekha

Cholengedwa chilichonse chimafunikira kudya kuti chipitilire kukhala ndi moyo, ndipo chakudya chili m’manja mwa Allah …