Monthly Archives: January 2024

Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 3

8. Umodzi mwa ma ufulu a Quraan Majiid ndi kulingalira zomwe zili mkati mwake ndi matanthauzo ake kuti uchite moyenera malamulo a Quraan Majiid. Choncho, pamodzi ndi kuwerenga Quraan Majiid, munthu ayesetsenso kuphunzira tanthauzo la ma surah osiyanasiyana a Quraan Majiid ndikofunikanso. Izi ziyenera kuchitika pansi pa Aalim oyenerera. Munthu …

Read More »

Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) Kumuyang’anira Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam)

Bibi ‘Aaishah (radhwiyallahu ‘anha) akufotokoza: Titasamuka kupita ku Madina Munawwarah, nthawi ina yake Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) sadagone usiku onse (kuopa kuti adani angamuchite chipongwe). Apa ndi pamene Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Pakadakhala munthu owopa Allah kuti andidikilire usiku uno.” Tili chikhalire choncho, tinamva kulira kwa zida. Rasulullah (swallallaahu …

Read More »

Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 2

6. Ndi zoloredwa kuwerenga Quraan pafoni popanda wudhu. Komabe, munthu apewe kuyika dzanja lake kapena chala chake pa fonipo pomwe ndime za Qur’an zikuwonekera. Zindikirani: Tiyenera kukumbukira kuti ngakhale kuwerenga Qur’an pa foni nkoloredwa, kuwerenga Qur’an kuchokera m’bukhu monga m’mene ilili ndi zokondedwa kwambiri chifukwa kuteroko pali kutetezedwa kwa njira …

Read More »

Du’aa yapadera ya Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)

Olemekezeka ‘Aaishah bint Sa’d (radhwiyallahu ‘anha), mwana wamkazi wa olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu), akufotokoza motere kuchokera kwa abambo ake, Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu): Pa nkhondo ya Uhud. (Pamene adani adaukira kumbuyo kwawo ndipo ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) ambiri adaphedwa pabwalo lankhondo), ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) sadathe kumpeza Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) …

Read More »

Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid

1. Onetsetsani kuti mkamwa mwanu ndimoyera musanambe kuwerenga Qur’an Majiid. Kwanenedwa kuti Ali (radhwiyallahu anhu) adati: “Ndithu, pakamwa panu ndi njira ya Qur’an Majiid (pakamwa panu mumawerenga Qur’an Majiid). Pa chifukwa chimenechi, tsukani mkamwa mwanu pogwiritsa ntchito miswaak. 2. Inyamureni Quraan Majiid Mwaulemu kwambiri ndipo nthawi zonse iyikeni pamalo Olemekezeka …

Read More »

Maloto a Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) Asanalowe Chisilamu

Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) anati: Ndisanalowe Chisilamu, ndinali ndi maloto omwe ndidawona ndili mumdima wandiweyani ndipo sanathe kuwona kalikonse. Mwadzidzidzi, panaoneka mwezi umene unayamba kuwala usiku. Kenako ndinatsatira kuwalako mpaka ndinakaufika mwezi M’malotowo, ndinaona ndithu anthu amene adanditsogolera kufikira mwezi. Ndidamuona Zaid bun Haarithah, Ali bun Abi Taalib ndi Abu Bakr …

Read More »

Mariziq Ali M’manja Mwa Allah Yekha

Cholengedwa chilichonse chimafunikira kudya kuti chipitilire kukhala ndi moyo, ndipo chakudya chili m’manja mwa Allah yekha. Ziyenerezo, mphamvu ndi luntha sizizindikiro zodziwira umoyo wa munthu. Mawu a ndakatulo ndi oonadi: ينال الفتى من عيشه وهو جاهل ويكدى الفتى في دهره وهو عالم ولو كانت الأرزاق تجرى على الحجى هلكن إذا …

Read More »

Ubwino Owerenga Quraan Majeed 3

Ntchito Yokondedwa Kwambiri Kwa Allah ndi Kuwerenga Qur’an mosalekeza Ibnu Abbaas (radhwiyallahu anhuma) akusimba kuti munthu wina adamufunsa Rasulullah swallallahu alaihi wasallam kuti, “Kodi ndi ntchito iti yomwe ili yokondedwa kwambiri kwa Allah? Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) anayankha kuti, ‘Ntchito za halaal ndi murtahil (wapaulendo amene akaima paulendo wake, amayambiranso …

Read More »

Sayyiduna Ali (Radhwiyallaahu ‘anhu) kutumidwa ndi Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) kuti akakonze mitumbira ya Manda, kuswa Mafano ndi kufuta Zithunzi

Olemekezeka Ali (radhwiyallahu ‘anhu) akusimba kuti nthawi ina, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adapita ku maliro a Swahaabah wina wake. Kenako adalankhula ndi ma swahaabah (radhiyallahu ‘anhum) omwe adalipo Ndipo adati: “Ndani mwa inu adzabwerera ku Madinah Munawwarah, ndipo paliponse akakawona fano kapena chiboliboli adzaziphwanya, ndipo paliponse pamene akaone mtumbira wa …

Read More »

Allah Ta’ala Yekha Ndi Amene Amadyetsa Zolengedwa Zonse

Tsiku lina, m’nthawi ya Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) gulu la maswahaaba a fuko la Banu Al-Ash’ar lidayenda kuchokera ku Yemen kupita ku Madina Munawwarah ndi cholinga chopanga hijrah. Atafika ku mzinda odalitsika wa Madinah Munawwarah, adapeza kuti chakudya chawo chomwe adabwera nacho chatha. Choncho adaganiza zotumiza mmodzi mwa maswahaba awo …

Read More »