عن جابر قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: ما اجتمع قوم ثم تفرقوا عن غير ذكر الله وصلاة على النبي صلى الله عليه وسلم إلا قاموا عن أنتن جيفة (مسند أبي داود الطيالسي، الرقم: 1863، ورواته ثقات كما في إتحاف الخيرة المهرة، الرقم: 6062)
Sayyiduna Jaabir (radhiyallahu anhu) akufotokoza kuti nthenga wa Allah (madalitso ndi ntendere zipite kwa iye) adati, nthawi ina iliyonse imene anthu asonkhana ndikumaliza nkumano wawowo ndikumwazikana popanda kumutchula Allah kapena kumufunira zabwino Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) pankumanowo, ziri ngati kukumana pamalo pomwe pali fungo lonyasa la chinthu chakufa ndipo kenaka amwazikana.(nkumano umene wayamba ndikutherapo popanda kutchula dzina la Allah lafaniziridwa ndi malo omwe ndi onyasisitsa lomwe palibe munthu angalakelake kukhalapo.
Sayyiduna Abu Bakr (Radhiyallahu Anhu) Akonzeka Kuzimana China Chirichonse Pa Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasallam)
Nkhondo ya Badr idakali mkati, mwana wa Sayyiduna Abu bakr (radhiyallahu anhu) amene ndi Abdu-Rahman (radhiyallahu anhu) adali mbali ya adani popeza adali asadalowe chisilamu.
Patadutsa nthawi, atalowano chisilamu, ali chikhalire ndi bambo ake omwe ndi Sayyiduna Abu-Bakr Siddeeq (radhiyallahu anhu) adati, oh bambo anga okondedwa, pa nkhondo ya Badr mudayandikana ndiine nditanyamura lupanga langa kangapo konse, komano chifukwa choganizira kuti ndiinu bambo anga, sindikhale ndi maganizo oti ndikupheni. (Tareekh ul khulafaa, 1/33)