Kuwerenga durood pamene muli pa nsonkhano

عن ابن عمر رضي الله عنهما قال قال رسول الله صلى الله عليه وسلم زينوا مجالسكم بالصلاة علي فان صلاتكم علي نور لكم يوم القيامة (الفردوس بماثور الخطاب، الرقم: ٣٣٣، وإسناده ضعيف كما في القول البديع ص٢٧٨)

Sayyiduna Abdullah bin Umar (radhiyallahu anhuma) akusimba kuti Sayyiduna Rasulullah (sallallahu alaih wasallam) adati; Kongoletsani misonkhano yanu pondiwerengera Durood (pondifunira zabwino) popeza durood yanuyo kudzakhala kuwala patsiku lachiweruzo.

Kupulumuka Ku Mazunzo Obwera Pa Nthawi Yomwalira Kudzera Mu Kuwerenga Durood

Mu Chitabu chotchedwa Nuzhatul Majaalis mukupezeka nkhani iyi:

Tsiku lina munthu wina wake adakamuyendera nzake amene adadwazika kwambiri pamenepo nkuti ali pafupi kumwalira, adamufunsa odwalayo kuti ‘’ukuwunva bwanji ululu wa infa pa nthawi ino pamene ukunyamuka?’’ Iye adayankha nati; “palibe ululu ulionse umene ndikunva, ndidanva ma Ulama (mashehe) akunena kuti munthu amene angawerenge durood mowirikiza ponfunira zabwino Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adzatetezeka ku ululu wa imfa panthawi Yomwalira.’’ (Fadaile Durood, Pg, 181)

Check Also

Kuwerenga Durood musanapange Dua

عن فضالة بن عبيد قال: بينا رسول الله صلى الله عليه وسلم قاعد إذ دخل …