Tafseer Ya Surah Qadr

بِسمِ اللّٰـهِ الرَّحمٰنِ الرَّحيمِ

اِنَّا أَنزَلنٰهُ فى لَيْلَةِ القَدْرِ ﴿١﴾ وَما أَدرىٰكَ ما لَيلَةُ القَدرِ ﴿٢﴾ لَيلَةُ القَدرِ خَيرٌ مِن أَلفِ شَهرٍ ﴿٣﴾ تَنَزَّلُ المَلـٰئِكَةُ وَالرّوحُ فيها بِإِذنِ رَبِّهِم مِن كُلِّ أَمرٍ ﴿٤﴾ سَلـٰمٌ هِىَ حَتّىٰ مَطلَعِ الفَجرِ ﴿٥﴾

Ndithudi, Tayimvumbulutsa Qur’an mu usiku wa Qadr (olemekezeka kwambiri). Ndipo chingakudziwitse nchiyani za usiku olemekezeka kwambiriwu (Usiku wa qadar). Usiku olemekezeka kwambiriwu (waqadar) ndiwabwino kwambiri kuposera miyezi chikwi chimodzi (1000).Angelo komanso Mngelo Jibril (alayhis salaam) amatsika ndichilorezo cha Mbuye wawo kukakwaniritsa lamulo lililonse. Mu (usiku umenewu) mumakhala mtendere mpaka kutuluka kwa m’bandakucha.

Omasulira Qur’an yolemekezeka akufotokoza kuti chifukwa chomwe idamvumbulutsidwira surah imeneyi, Mtumiki wa Allah (sallallahu alayhi wasallama) adawawuza maswahaba nthawi ina zokhudza munthu wina womenya nkhondo panjira ya Allah (Mujaahid) yomwe anali ochokera mwa ana a Israel yemwe anamenya Jihaadi kwa miyezi yokwa chikwi chimodzi (1000).Pamene maswahabah (radiyallahu anhu) adamva kulimbikila kwamunthu ameneyu adadabwisidwa ndipo adasilila kwambiri pazimenezi.

Choncho pambuyo pake Allah Ta’ala adasitsa surah imeneyi ngati mphatso komanso kukhala mdalitso ku ummah uno. Mdalitso wapadera omwe womwe watchulidwa mu surah imeneyi ndiwoti ngati munthu ochokera mu ummat uno amene angapembedze Allah mu utsiku umenewu wa (laylatul qadri),adzapeza malipiro omupembedza Allah Ta’ala kuposera miyezi yokwana chikwi chimodzi (1000) zomwe ndi zaka zokwana 83.

اِنَّا أَنزَلنٰهُ فى لَيْلَةِ القَدْرِ ﴿١﴾

Ndithudi,Tidayitsitsa Quran mu usiku olemekezeka kwambiri (Qadar)

Mndime imeneyi ,Allah Ta’ala akulongosora kuti adayitsitsa quran yolemekezeka mu usiku wa laylatul qadri. Mahadith ena akulongosora kuti Quran yolemekedzekayi idatsitsidwa kwa Mtumiki (sallallahu alayihi wasallama) kwa nthawi ya zaka zoposa 23.

Otanthauzira Quran yolemekezeka akulongosora kuti Quran yolemekezeka poyamba idatsitsidwa kuchokera kumalo otchedwa Lawhu mahafuz kupita ku thambo loyamba mmwezi wa Ramadhan mu usiku wa Laylatul Qadr. Pambuyo pake, Qur’an yonse imatsitsidwa kwa Mtumiki sallallahu alayhi wasallama kuchokera pa Thambo loyamba kupitsidwa kwa Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) kwa nthawi yoposera zaka 23.

وَما أَدرىٰكَ ما لَيلَةُ القَدرِ ﴿٢﴾ لَيلَةُ القَدرِ خَيرٌ مِن أَلفِ شَهرٍ ﴿٣﴾

Ndipo chingakudziwitse nchiyani zokhudza usiku wa Qadar (olemekezeka kwambiriwu). Usiku wa qadar umenewu ndiwabwino kwambiri kuposera miyezi chikwi chimodzi.

Usiku umenewu umadziwika kuti ndi usiku wa qadar. Tanthauzo lina lamawu oti Qadar, ndiye kuti Ulemelero ochuluka ndikulemekezeka. Chifukwa chimene usiku umenewu udapatsidwira dzina limeneri ndichifukwa choti tsiku limeneli limapangitsa ummah uno kupeza ulemu ndi ulemelero ochuluka pamaso pa Allah Ta’ala. Choncho, munthu aliyense payekhapayekha akuyenera kulimbikira kumupembedza  Allah Ta’ala mu utsiku umenewu  ndikuti apeze madalitso ochuluka a usiku umenewu. Ngakhale ngati munthu atakhala oipa kwambiri  ndipo wadziika iye mwini pochita uchimo, Utsiku umenewu ukumupatsa mwayi wopambana kuti adzibweretse iye mwini  ku ulemelero wapamwambawu  kupyolera  mukupempha chikhululuko kwa Allah Ta’ala pa zoipa zake komanso adzipereke popanga ma ibaadah osiyanasiyana mu usiku odalitsikawu.

وَما أَدرىٰكَ ما لَيلَةُ القَدرِ ﴿٢﴾ لَيلَةُ القَدرِ خَيرٌ مِن أَلفِ شَهرٍ ﴿٣﴾

Ndipo chingakudziwitse mchiyani za usiku wa Qadariwu? Usiku wa Qadariwu ndiwabwino kwambiri kuposera miyezi chikwi chimodzi (1000).

Otanthauzira Quran akufotokozanso kuti tanthauzo lina la Qadar ndiye kuti CHIKONZERO.

Usiku umenewunso umatchuridwa kuti ndi usiku wa CHIKONZERO chifukwa usiku umenewu Allah Ta’ala amakwaniritsa zikonzero zimene zingafikire zolengedwa zake zimene amabweretsa angelo. Angelo amawuzidwa za munthu amene abadwe ndi amene atamwalire mkatikati mwachaka chimenecho komanso za riziki yamunthu wina aliyense imene Allah adzamupatse munthuyo.

Choncho pali mfundo ziwiri zolongosora nkhani yachikhonzero cha zolengedwa za Allah Ta’ala; Mfundo yoyamba imalongosora kuti chikonzero cha Allah (Qadar) chimatsitsidwa kwa angelo mu usiku wa Laylatul Baraah (pa 15 usiku wa mwezi wa shaaban) ndipo mfundo ina yachiwiri ikulongosora kuti Qadar chikhozero cha Mulungu chimatumizidwa kwa angelo mu usiku wa Laylatul Qadri  –Mfundo zonse ziwirizi ndizolondola.

Maulamaa asiyanitsa pakati pa  mfundo ziwiri zonsezi polongosora kuti pa 15 usiku wamwezi wa shaaban womwe umadziwika kuti Laylatul Baraah angelo amadziwitsidwa zinthu zosiyanasiyana  zomwe zakonzedwa kuti zichitike mchaka chotsatiracho. Mwachitsanzo, Chikonzero cha Mulungu chimakwaniritsidwa kwa munthu amene adzamwalire ndi amene adzakhale moyo komanso ndimariziq ochuluka bwanji amene adzapatsidwe munthu aliyense, ndimunthu wanji apatsidwe mwayi oti akapange mapemphero a Haji ndi umrah ndizina zotero. Cimodzimodzinso mndandanda onse okhudzana ndi munthu umalembedwa ndikukhonzedwa mu usiku wa laylatul baraaah ndipo angelo amawuzidwa zokhudza maganizowa.

Pambuyo pake mu usiku olemekezeka kwambiri (wa laylatul qadar) mapulani onse omwe adakonzedwa mu usiku wa Baraah (pa 15 shaban) amapatsidwa kwa angelo kuti akakwaniritse malamulo a Allah.

تَنَزَّلُ المَلـٰئِكَةُ وَالرّوحُ فيها بِإِذنِ رَبِّهِم مِن كُلِّ أَمرٍ ﴿٤﴾ سَلـٰمٌ هِىَ حَتّىٰ مَطلَعِ الفَجرِ ﴿٥﴾

Angelo pamodzi ndi (mngelo) jibril (Alayhi salaam) amatsika mu usikuwu ndichilolezo cha Mbuye wawo ndilamulo lilonse. Mtendere (usiku umenewu) umakhala mpakana mbandakucha.

Mu usiku umenewu, kuphatikizapo chifundo ndi mdalitso wa Allah Jibril amatsika nawo kuchokera ku Sidratul muntaha pamodzi ndi angelo. Sidratul muntaha ndimalo apatali kwambiri amene angelo amatha kukwelako kumwambako. Pamene mngelo Jibril pamodzi ndi angelo amabwera padziko lapansi amapereka malonje amtendere kwa okhulupilira wachimuna kapena wachikazi. Komabe angelo amenewa sapereka malonje amtenderewa kwamunthu omwa mowa komanso odya nyama yankhumba.

Amene amakhala kumapanga ma Ibaadah usiku ndithu amenewo ndi anthu amwayi waukulu komanso ndi amene ali ndi mdalitso wochuluka. Angelo amene amatsika kuchokera kumwamba amawapangira maduwa anthu amenewa. Amamupempha Allah kuti awapatse chifundo chake ndi chisoni chake chapadera. Kuonjezera apo Allah Ta’ala amawakhululukira machimo awo ang´onoang´ono akale.

Olemekezeka Abuu Hurayrah (radhiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adati, Amene angayime kupanga ibaadah mu usiku walaylatul Qadr ndichikhulupiliro komanso pofuna kulandila mphotho kuchokera kwa Allah Ta’ala machimo ake onse (ang´ono ang´ono) omwe adachita kale adzakhululukidwa.“

Hadith ina ikukamba kuti pamene mwezi wa Ramadhan udaoneka Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adawayankhula maswahaba (radhiyallahu anhum) nati:“Ndithu mwezi uwu wa Ramadhan wakubwererani inuyo ndipo mkati mwake muli usiku umodzi waukulu ndiwofunikira kuposera miyezi chikwi chimodzi (1000). Munthu amene angamanidwe zabwino zausikuwu ndiye kuti wamanidwa zabwino zochuluka.

Choncho,mkatikati mwa usiku olemekezekawu munthu aliyense awonetsetse kuti akupanga ibaadah ndiponso adzitalikitse kumachimo. Munthunso akuyenera kuchulukitsa maduwa ndikumamupempha Allah Ta’ala kuti amukhululukire machimo ake ndikuti amudalitse ndichifundo chake chapadera.

تَنَزَّلُ المَلـٰئِكَةُ وَالرّوحُ فيها بِإِذنِ رَبِّهِم مِن كُلِّ أَمرٍ ﴿٤﴾ سَلـٰمٌ هِىَ حَتّىٰ مَطلَعِ الفَجرِ ﴿٥﴾

Angelo komanso Mngelo Jibril alayhimus salaam amatsika mu usikuwu mwachilolezo cha Mbuye wawo kudzakwaniritsa lamulo lililonse. Mtendere usiku umenewu umapitilira mpakana kutuluka kwa mmbandakucha.

Olemekezeka Aishah (radhwiyallahu anha) tsiku lina anati kwa Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam), oh inu Mtumiki wa Allah, Ngati ndingawupeze usiku umenewu ndi duwa yanji imene ndingachite? Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adayankha ponena duwa iyi

اَللّٰهُمَّ إِنَّكَ عَفُوٌّ تُحِبُّ الْعَفْوَ فَاعْف عَنِّيْ

O Allah inu ndiinu mwini kukhululukira machimo ndipo mumakonda kukhululuka, choncho ndikhululukireni ine.

Kudzera mu Duwa imeneyi Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) akuuphunzitsa ummah kuti nthawi zonse udzibwelera kwa Allah Ta’ala polapa machimo awo ndipo pasapezeke nthawi yoziwona munthu kuti iyeyo ndiopatulika alibe uchimo.

Ngakhale tsiku la Laylatul Qadr lenileni silinaonetsedwe ku ummah onse, Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adaulangiza ummati kuti udzifufuza laylatul qadr mmwezi wa Ramadhan.

Mumahadith ena zikunenedwa kuti Mtumiki (sallallahu alayhi wasallam) adati “Ifufuzeni laylatul qadr mmasiku khumi (10) otsirizira a mwezi wa Ramadhan” Muhadith ina Mtumiki (salallah alayhi wasallama) adati “Ufufuzeni usiku wa laylatul qadr mmasiku osagawikana ndi nambala ya 2 mumasiku khumi otsirizira a mwezi wa Ramadhan.”

Maulamaa akufotokoza kuti Laylatul Qadr imachitika gawo lirilonse mmwezi wa Ramadhan .Komabe mwachizolowezi imachitika mkatikati mwa masiku khumi otsirizira mmwezi waramadhani amene ali osagawika ndi nambala ya 2.

Check Also

Tafseer ya Surah Ikhlaas

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ قُلْ هُوَ اللَّهُ أَحَدٌ ‎﴿١﴾‏ اللَّهُ الصَّمَدُ ‎﴿٢﴾‏ لَمْ يَلِدْ وَلَمْ يُولَدْ ‎﴿٣﴾‏ وَلَمْ يَكُن لَّهُ كُفُوًا …