بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ
قُلْ أَعُوذُ بِرَبِّ الْفَلَقِ ﴿١﴾ مِن شَرِّ مَا خَلَقَ ﴿٢﴾ وَمِن شَرِّ غَاسِقٍ إِذَا وَقَبَ ﴿٣﴾ وَمِن شَرِّ النَّفَّاثَاتِ فِي الْعُقَدِ ﴿٤﴾ وَمِن شَرِّ حَاسِدٍ إِذَا حَسَدَ ﴿٥﴾
Nena (iwe Muhammad (Swallallaahu ‘alayhi wasallam): “Ndikudzitchinjiriza mwa Mbuye wa m’bandakucha, ku zoipa zonse zomwe Adazilenga, ndi ku zoipa za mumdima (wa usiku) pamene mdima wake ukufalikira; ndi ku zoipa za amene amauzira mfundo (panthawi yochita ufiti ndi matsenga), ndiponso ku zoipa za wansanje pamene akuchita nsanje.
بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ
قُلْ أَعُوذُ بِرَبِّ النَّاسِ ﴿١﴾ مَلِكِ النَّاسِ ﴿٢﴾ إِلَٰهِ النَّاسِ ﴿٣﴾ مِن شَرِّ الْوَسْوَاسِ الْخَنَّاسِ ﴿٤﴾ الَّذِي يُوَسْوِسُ فِي صُدُورِ النَّاسِ ﴿٥﴾ مِنَ الْجِنَّةِ وَالنَّاسِ ﴿٦﴾
Nena (iwe Muhammad (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)) Ndikudzitchinjiriza mwa Mbuye wa anthu, Mfumu ya anthu, Opembedzedwa wa anthu ku zoipa za mnong’onezi amene amabwerera (pamene patchulidwa dzina la Allah Ta’ala). Yemwe amanong’oneza m’zifuwa mwa anthu Kuchokera mwa ziwanda ndi anthu.
Suraا ziwirizi, Surah Falaq ndi Surah Naas, zidavumbulutsidwa ku Madina Munawwarah Rasulullah (swallallaahu ‘alaihi wasallam) atasamukira ku Madinah. Choncho surah ziwirizi zimatchedwa kuti ‘Madani Surah’.
Chifukwa chimene surah ziwirizi zidavumbulutsidwira ndikuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adazunzidwa kwambiri ndi sihr (matsenga).
Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) Achitidwa Matsenga
M’chaka cha 6 chisamukireni ku Makkah, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndi ma Swahaabah (radhwiallahu ‘anhum) adapita ku Makka Mukarramah ndi cholinga chokachita Umrah. Komabe adakanizidwa kulowa mu Makkah Mukarramah ndi makafiri a ku Makkah. Pambuyo pake, Pagano la mtendere lidasainidwa ndi Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndipo ma Kuffaar adanenetsa kuti kwa zaka khumi sipadzakhala nkhondo kapena kumenyana pakati pa magulu awiriwa. Panganoli linkatchedwa Sulh Hudaybiyyah (Pangano la Hudaybiyyah).
Panganoli litasainidwa, Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndi Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) adabwerera ku Madina Munawwarah m’mwezi wa Zul Hijjah.
Patatha mwezi umodzi, m’mwezi wa Muharram 7 AH, gulu la Ayuda linadza kwa Labeed bin Aa’sam yemwe anali katswiri wamatsenga ndi ufiti. Ayuda awa adamuuza kuti akhala akuyesetsa kwa nthawi yaitali kumulodza Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndi kumupha, koma matsenga awo onse ndi ufiti wawo sizinaphule kanthu. Choncho anaganiza zopita kwa iye podziwa kuti iyeyo ndi katswiri pa nkhani imeneyi ndipo palibe munthu waluso ngati iye pa zamatsenga. Adampatsa madinaar atatu (ndalama zagolide) kuti akwaniritse ntchito yomupha Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam).
Malinga ndi malipoti ena, Labeed adali Myuda, pomwe nkhani zina zimasonyeza kuti adali munaafiq (wachinyengo), pomwe nkhani zina zikusonyeza kuti adali wochokera ku Answaar a ku Madina Munawwarah.
Hafiz Ibnul Hajar (rahimahullah) akuyanjanitsa pakati pa nkhanizi pofotokoza kuti isanafike hijrah ya Rasulullah (swallallahu ‘alayhi wasallam), Answaar anali pa ubale wapamtima ndi Ayuda. Komabe, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) atapanga hijrah kupita ku Madinah Munawwarah, Answaar adalowa Chisilamu ndi kudula ma ubale ndi Ayuda. Mmodzi mwa iwo anali Labeed bin Aa’sam. Chifukwa cha ubale wake wapamtima ndi Ayuda, ena ankamuona kuti ndi Myuda.
Labeed anali wa fuko la Banu Zuraiq. Ankadzinamiza kuti ndi wokhulupirira ndipo amakapezeka pamisonkhano ya Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam), pomwe Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ankadziwa kuti iye ndi m’modzi mwa ma munaafiqeen (Achiphamaso).
Labeed atalandira malipiro a madinari atatu kuchokera kwa Ayuda, adakumana ndi mnyamata wachiyuda yemwe ankakonda kupita kunyumba ya Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ndi kumamutumikira Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam). Labeed Adapempha mnyamatayo kuti amupatse tsitsi lodalitsika la Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam). Pofuna kuti mnyamatayo amubweretsere tsitsilo, iye anapeka bodza limene anamufotokozera ndikumutsimikizira kuti akufuna kuti tsitsilo agwiritsire ntchito mnjira yabwino. Choncho, mnyamatayo adatenga tsitsi ndi chipeso cha Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) nalipereka kwa iye.
Labeed adagwiritsa ntchito tsitsi lodalitsika la Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam), mano achipeso ndi kanjedza m’matsenga omwe adam’chitira Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam). Malipoti ena afotokozanso kuti iye adapanga chiboliboli chopangidwa kuchokera ku wakisi chofanana ndi Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndikulowetsamo masingano khumi ndi imodzi.
Banja lonse la Labeed bin Aa’sam linatenga nawo gawo kuchita matsengawa, choncho adagwiritsa ntchito ana ake aakazi kuti amuthandize pomulodza Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam). Atamaliza matsengawa, Labeed adatenga zinthuzi ndikuziyika pansi pa thanthwe pansi pa chitsime china ku Madina Munawwarah chotchedwa Bir Zi Azwaam.
Hazrat Aaishah (radhwiyallahu ‘anha) akufotokoza kuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atachitidwa matsenga, anadwala ndipo adayamba kuyiwala zinthu zambiri zochitika padziko lapansi. Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ankaiwala kuti inali nthawi ya ndani mwa akazi ake olemekezeka ndi kupita ku nyumba ya mkazi wina. Komanso sankakhala ndi chilakolako cha chakudya ndi komanso ankafooka. Komabe, pa nkhani ya Dini monga kufikitsa Dini kwa Ummah, kukumbukira wahi umene unavumbulutsidwa kwa iye, kutanthauza kuti matsengawo sadamukhudze chilichonse pa nkhani za Dini. Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adakhala akuvutika ndi matendawa pafupifupi kwa miyezi isanu ndi umodzi.
Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) pamene ankakumana ndi vuto limeneli, poyamba ankaganiza kuti anali matenda chabe. Choncho, Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) ankachotsa magazi oipa m’thupi mwake (hijaamah), koma ataona kuti palibe kusintha, adazindikira kuti pali china chake chomwe chikumusowetsa mtendere.
Kukambirana Kwa Pakati pa Angelo Awiri
Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) nthawi ina adalankhula ndi Sayyidatuna Aaisha (Radhwiyallaahu ‘anha) pamene ankadwala ndipo anamuuza kuti: “Ine ndakhala ndikudwala kwa nthawi yayitali, ndipo ndimapempha Allah Ta’ala mosalekeza kuti andiululire zoona zake za matendawa.
Ndidali chigonere, mkatikati mogona, Allah Ta’ala anatumiza angelo awiri kwa ine (Olemekezeka Jibra’iyl (‘alayhis salaam) ndi Mikaa’eel (‘alaihis salaam)) mmodzi anakhala pafupi ndi mutu wanga. ndi winayo kumapazi anga.
Mngelo amene anali kumutu anafunsa mngelo amene anali ku mapazi anga kuti: “Chachitika n’chiyani munthu ameneyu? akudwala matenda otani?
Winayo anayankha nati, “Wachitidwa matsenga.”
Kenako mngelo amene anali kumutu anafunsa mngelo amene anali ku mapazi kuti: “Ndani wachititsa zimenezi?” Mngelo winayo anayankha kuti, “Labeed bin Asam.”
Mngelo amene anali kumutu anafunsanso mngelo amene anali ku mapazi anga kuti: “Kodi ndi zinthu ziti zimene zinagwiritsidwa ntchito pomuchitira matsengawa?”
Mngeloyo anayankha kuti: “Matsengawa anagwiritsa ntchito tsitsi lake, mano a chipeso chake, ndi pankhuni ngayaye za kanjedza yamphongo.
Atamva kukambirana komwe kunachitika pakati pa angero awiri (omwe kwenikweni anali njira womudziwitsira Mtumiki (swallallaahu wasallam) zomwe zikumuchitikira ochokera kumbali ya Allah Ta’ala), Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adadzuka ndipo adalamula gulu la ma Swahaabah anayi (Hazrat Ali, Ammaar, Jubair ibn Iyaas ndi Qais ibn Mihsan (radhwiyallahu ‘anhum)) kuti lipite kumalo kumene sihr (matsengawa) adayikidwa ndi kuti akachotse.
Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adauzidwanso ndi Allah Ta’ala kumaloto kuti matsengawa aikidwa pachitsime china chake. Zanenedwanso kuti Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) nayenso anapita ku chitsimecho ndipo zinthu zimene ankachitira matsengawo anazichotsa pansi pa mwala omwe unali pansi mchitsimecho ndikubweretsedwa kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam).
Pa nthawi imeneyi ndi pamene Hazrat Jibra’iyl (alaihi Salaam) adatsika kuchokera kumwamba nadza ndi Surah ziwirizi; Surah Falaq ndi Surah Naas, zomwe zidavumbulutsidwa kwa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) panthawiyo. Olemekezeka Jibriyl (alayhis salaam) adamuuza Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kuti awerenge ndime iliyonse ya surah ziwirizi kuyambira kumayambiliro mpaka kumapeto. Pamene Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) akamawerenga ndime iliyonse, mfundo zimamasuka ndipo singano za m’chifanizo cha Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) zimachoka. Pamene mfundo zimamasuridwa, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ululu umatha pang’ono pang’ono, koma pambuyo pake adapeza mpumulo waukulu.
Mahaadeeth ena amanena kuti matsengawa atachotsedwa, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adapeza mpumulo waukulu kotero kuti zidakhala ngati adamasulidwa unyolo pambuyo pomangidwa kwa nthawi yayitali.
Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adafotokoza maonekedwe a mitengo ndi madzi a pachitsimechi kwa Hazrat Aaishah (radhwiyallahu ‘anha) kuti: “Zinali ngati madzi othiriwa mendhi kukhala akuda kwambiri, ndi mitengo yopezeka pafupi ndi chitsimecho inkafanana ndi mitu ya ziwanda zoipa (malipoti ena amanena kuti nthambi za mitengoyo zinkafanana ndi mitu ya njoka).” Awa adali malo owopsa ndi owopsa pomwe kwa Mtumiki (swallallaahu alayhi wasallam) adachitidwira matsengapa.
Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atawerenga mu’awwazatain (Surah Falaq ndi Surah Naas), Hazrat Jibra’eel (‘alaihis salaam) adabwereza dua ili kuti amuthandize Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) pamatsenga akuda adagwidwa ndi:
بِاسْمِ اللهِ أَرْقِيْكَ مِنْ كُلِّ شَيْءٍ يُؤْذِيْكَ مِنْ شَرِّ كُلِّ نَفْسٍ أَوْ عَيْنٍ حَاسِدٍ اللهُ يَشْفِيْكَ بِاسْمِ اللهِ أَرْقِيْكَ
M’dzina la Allah Ta’ala ndikukuwerengerani mawu awa (ndipo ndikukupatsani chithandizo chochokera kwa Allah Ta’ala) ku choipa chilichonse chimene chikukuwawa kuchokera ku ululu uliwonse kapena diso ladumbo. Allah Ta’ala akupatse kuchira. M’dzina la Allah Ta’ala ndikukuwerengera mau awa (ndikukuthandiza kumpempha machilritso kwa Allah Ta’ala).
Khalidwe lodziwika bwino la Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam)
Matsengawa atachotsedwa ndipo Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adapeza mpumulo waukulu, Hazrat Aaishah (radhwiyallaahu ‘anha) adamupempha Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) kuti awayitane anthu ndikuwaululira munthu amene adamuchitira zamatsengazi ndi kuwotcha moto zithumwa zonse pamaso pa anthu onse. Mahadith ena amanena kuti adamupempha Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) kuti amuthamangitse munthu yemwe adapanga zimenezi (Labeed bin Aa’sam) kuchoka munzinda wa Madinah Munawwarah.
Komabe, yankho la Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) linali lakuti, “Oh Aaishah! Allah Ta’ala wandichiritsa, choncho palibe chifukwa choti ndichite izi. Chilango chimene Allah Ta’ala amupatse chikumkwanira.” Komabe, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adalamula kuti chitsimecho chikwiliridwe ndi kusalazidwa kwathunthu.
Chinali chizoloŵezi chodalitsika cha Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndi maonekedwe a khalidwe lake lapamwamba kuti sadabwezere choipa chilichonse chimene wina wake adamuchitira iye mwini. M’malo mwake, nthawi zonse ankakhululukira anthu amene ankamuzunza kapenanso kumupondereza. Labeed bin Aa’sam ankapita ku Majaalis (misonkhano) ya Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam), popeza iye adali wochokera kwa Achiphamaso (ma munaafiq), komabe zalembedwa kuti ngakhale zitachitika izi, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) sanalankhule nayeko (kumufunsa) za izi, kapena kumusinthira chikhalidwe.
Cholinga chakuvumbulutsidwa kwa Surah ziwirizi
Sura ziwirizi, monga tafotokozera kale, zidavumbulutsidwa pa nthawi yomwe matsenga adapangidwa pa Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam). Allah adawatsitsa kuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) achiritsidwe ndi kutetezedwa kudzera m’masurawa, komanso kuti Ummah nawonso uzitha kuchiritsidwa ndi kutetezedwa.
Ma Ulama akufotokoza kuti Surah yoyamba (Surah Falaq) idavumbulutsidwa makamaka kuti ipulumutse munthu ku zowawa zakuthupi, ndipo Sura yachiwiri (Surah Naas) idavumbulutsidwa makamaka kuti ipulumutse munthu ku zovuta zonse zauzimu.
قُلْ أَعُوذُ بِرَبِّ الْفَلَقِ ﴿١﴾
Nena (iwe Muhammad (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)).
Ndikudzitchinjiriza mwa Mbuye wa m’bandakucha M’ndime iyi Allah Ta’ala anatchula mwatchutchutchu mawu oti ‘m’bandakucha’, kutanthauza nthawi ya m’bandakucha pamene kuwala kumaonekera pambuyo pa mdima.
M’menemo muli uthenga kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndi Ummah, owauza kuti monga momwe mdima wa usiku umatsatiridwa ndi kuwala kwa m’bandakucha, momwemonso pambuyo pa nthawi yamavuto ndi zovuta, thandizo la Allah Ta’ala ndithu libwera.
Pamene thandizo la Allah Ta’ala labwera, limachotsa midima yonse ndikupangitsa kuwala kufalikira paliponse. Choncho, munthu akakumana ndi mavuto, mazunzo ndi masautso, atembenukire kwa Allah Ta’ala ndipo asataye chiyembekezo cha chifundo Chake nthawi iliyonse.
Ma Mufassireen ena akufotokoza kuti mawu oti “Falaq” amatanthauza chigwa cha Jahannam. Kupweteka ndi kuopsa kwa chigwachi ndikuti Jahannam imadzitchinjiriza kwa Allah Ta ‘ala kuchigwacho tsiku ndi tsiku. Munthu angalingalire bwino lomwe vuto lalikulu la awo amene adzaponyedwe m’malo oterowo mu Jahannam.
Choncho kudzera mukulongosora kwa Allah Ta’ala kutchula za chigwachi chomwe chikupezeka mu Jahannam ndi kutchula kuti Iye ndi Mbuye wa chigwachi, pali umboni pa nkhani imeneyi kuti pamene Allah Ta’ala ndi Mlengi wa gwero la masautso, zowawa ndi zopweteka zowopsa zomwe munthu sangathe kulingalira vuto lililonse ndi zovuta kukhala zowawa kuposa zimenezo; munthu azindikire kuti palibe kothawira kwa kupatula iye ndi malo opatulika kupatula kutembenukira kwa Allah Ta’ala. Iye yekha ndiye ali ndi njira yothetsera mavuto onse, mayankho a mafunso onse ndi kuchoka ku zovuta zonse.
مِن شَرِّ مَا خَلَقَ ﴿٢﴾
ku zoipa zonse zomwe Adazilenga,
Ndime iyi ikufungatira (mukupezekamo) zovuta zilizonse kapena zoyipa zomwe zingathe kuganiziridwa, komanso zomwe sizingaganizidwe mwamunthu. Chitetezo chikuyenera kupemphedwa kwa Allah Ta’ala ku zoipa zilizonse kapena mavuto.
M’ndime iyi, Allah Ta’ala akutiuza kuti Iye ndi Mlengi wa mavuto. Choncho, pamene iye ali Mlengi wa mavuto, ndiye kuti tiyenera kupempha chitetezo kwa Iye kuti achotse mavutowo. Choncho tikafuna chitetezo, tidzitchinjirize kwa Mbuye wa m’bandakucha ku zoipa za zolengedwa zake.
M’zimenezi Allah Ta’ala akutilimbikitsa kuti pamene chilichonse chili cholengedwa Chake, ndiye kuti ngakhale choipacho chioneke chochepa kapena choononga motani pamaso pathu, tiyenera kukumbukira kuti zonse ndi zolengedwa zake ndipo Iye ali ndi mphamvu zonse pa izo.
Choncho, munthu sayenera kuthedwa nzeru ndi vuto ndi mkhalidwe umene munthu alimo, koma m’malo mwake aziyang’ana uyo amene analenga chirichonse ndipo ali ndi ulamuliro pa chirichonse.
Zoona zake ndi zakuti, Msilamu ayenera kuzindikira kuti amene ali ndi mphamvu zolenga chinthu alinso ndi mphamvu zochiwononga ndi kuchisowetseratu. Nthawi zina munthu amatanganidwa kwambiri ndi vuto lomwe ali nalo mpaka kuiwala kuti kuli Mlengi.
Pambuyo podzitchinjiriza kwa Allah Ta’ala ku zoipa zonse, Allah Ta’ala pambuyo pake akutiphunzitsa kuti tiyenera kudzitchinjiriza kwa Iye ku zoipa zitatu zomwe zili m’ndime zitatu izi:
وَمِن شَرِّ غَاسِقٍ إِذَا وَقَبَ ﴿٣﴾ وَمِن شَرِّ النَّفَّاثَاتِ فِي الْعُقَدِ ﴿٤﴾ وَمِن شَرِّ حَاسِدٍ إِذَا حَسَدَ ﴿٥﴾
Kuchokera ku kuipa za mumdima (wa usiku) Pamene mdima wake ukufalikira, ndi ku zoipa za amene amauzira mu mfundo (panthawi yochita matsenga), ndi ku zoipa za nsanje pamene ochita nsanjeyo akupanga nsanje.
Ma Ulama akufotokoza kuti chifukwa chimodzi chomwe chachititsa kuti zoipa zitatuzi zitchulidwe ndikunenedwa mwapaderadera makamaka ndi chakuti zoipa zitatuzi zidapezeka pa zomwe zidachitika kuti mpakana masurawa avumbulutsidwe (matsenga adachitidwa kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alaihi wasallam).
- Kuipa kwa usiku wamdima kwatchulidwa potengera kuti matsengawa anachitika usiku.
- Kuipa kwa omwe amkauzira mfundo kwatchulidwa chifukwa omwe adachita nawo zamatsengazi anali ana aakazi a Labeed bin Aa’sam, omwe ankauzira mfundo pa nthawi yomwe adachita matsengawa.
- Kuipa kwa nsanje kukutchulidwa ngati tsinde la chiyambi cha Ayuda kuchita ufiti ndi nsanje yomwe adali nayo m’mitima mwawo pa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) ndi kusafuna kuti nkhani yake ndi ntchito yake (yofalitsa Chisilamu) ifalikire.
Kotero, chitetezo chimapemphedwa mwachindunji kudzera m’mitundu itatu ya mavuto awa:
1. Usiku umene mdima wake ukufalikira.
2. Kuipa kwa akazi amene amauzira mfundo.
3. Kuipa kwa nsanje pamene munthuyo akuchita nsanje.
Kuchokera ku mavuto atatuwa, tikuwona kuti vuto loyamba ndi lachitatu aphatikizidwa ndi ndime. Pankhani ya vuto loyambirira, kuipa kwa usiku kwatchulidwa ndi ndime ya mdima omwe ukufalikira, ndipo pamene vuto lachitatu, kuipa kwa nsanje kwatchulidwa ndi ndime yosonyeza nsanje. Kukamba za vuto lachiwiri, tipeza kuti tazindikira kuti siikugwirizana ndi chilichonse.
Chifukwa chake n’chakuti kuipa kwa usiku kwagona mumdima wake. Mdima ukasinthana ndi m’bandakucha ndiye kuti kuipa kwa usiku kumathera pomwepo. Kuukira kwa mbala ndi afiti, ndi kuvulaza kwa nyama zosiyanasiyana za mtchire, nthawi zambiri zimachitika usiku. Choncho, chitetezo chikapemphedwa kwa Allah Ta’ala ku zoipa za usiku, masautso onsewa amaphatikizidwa m’menemo.
Chimodzimodzinso kuipa kwa wosilira kumangowoneka pamene akuonetsera nsanje yake, apo ayi nsanje yake idzangomupweteka mumtima mwake ndipo siidzachita kanthu kwa munthu amene akumuchitira nsanjeyo. Chifukwa chake, chitetezo chimafunikira kwa wansanje panthawi yomwe akufuna Kutulutsa ndi kuonetsera poyera nsanje yake, popeza iyi ndi nthawi yomwe amawapsinja ena.
Tikanena za ufiti ndi nyanga, zimamupeza munthu usana ngakhale usiku. Chifukwa chake, palibe chiganizo chimene chalumikizana ndi zoyipa izi.
Pothirira ndemanga pa ma ayah awa, Hafidh Ibn Qayyim (rahmatullahi alaih) adanena kuti zomwe zimayambitsa mavuto onse, kaya akuthupi kapena auzimu, zingabwere pazifukwa ziwiri izi:
1) Zopweteka zenizeni za thupi, mavuto kapena tsoka lomwe munthuyo amakumana nalo.
2) Chiyambi chomwe chimabweretsa ululu.
Pankhani ya zowawa zakuthupi, ndiye ndi chifukwa chathupi, ndipo ngati ndi ululu wauzimu ndi chifukwa chauzimu.
Mwachitsanzo, ukafiri, shirk, kusamvera Allah Ta’ala ndi zina zotere ndizomwe zimayambitsa kubwerera m’mbuyo kwauzimu ndi kuonongeka.
Sura iyi, kupyolera mu ayah مِنۡ شَرِّ مَا خَلَقَ , ili ndi mitundu yonse iwiri ya zifukwa ndipo imatiphunzitsa kufunafuna chitetezo kuzinthu zonse zoipa ndi zopweteka.
قُلْ أَعُوذُ بِرَبِّ النَّاسِ ﴿١﴾ مَلِكِ النَّاسِ ﴿٢﴾ إِلَٰهِ النَّاسِ ﴿٣﴾ مِن شَرِّ الْوَسْوَاسِ الْخَنَّاسِ ﴿٤﴾ الَّذِي يُوَسْوِسُ فِي صُدُورِ النَّاسِ ﴿٥﴾ مِنَ الْجِنَّةِ وَالنَّاسِ ﴿٦﴾
Nena (iwe Muhammad (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)) Ndikudzitchinjiriza kwa Mbuye wa anthu, Mfumu ya anthu, Mulungu wa anthu, ku zoipa za mnong’onezi amene amabwerera (pamene latchulidwa dzina la Allah Ta’ala). Yemwe amanong’oneza m’mitima mwa anthu (monga) Ochokera m’ziwanda komanso mwa anthu.
M’sura yapitayi (Surah Falaq) kusakasaka kothawira kunachitika makamaka ku zopweteka zakuthupi (ngakhale kuti zowawa zauzimu zidaphatikizidwanso m’ndime ya Ayah مِنۡ شَرِّ مَا خَلَقَ kuipa kwa zinthu zonse zomwe Allah Ta’ala adazilenga). M’surayi mukupemphedwa chitetezo ku masautso auzimu ndi zopsinja zomwe ndi zoipa za Satana.
Popeza kuonongeka kwa uzimu ndi koipitsitsa komanso kwakukulu kuposa kuvulaza thupi, Qur’aan Majiid yamaliza ndi surayi Pankhani ya kuvulaza kwakuthupi komwe kumakhudza munthu, kuvulaza kumangokhalapo pa nthawi yomwe ali moyo. Akangomwalira, vuto lalikulu lomwe anali kudutsamo limatha. Pankhani ya kuonongeka kwa uzimu kumapitirira ndi kupyola moyo wapadziko lapansi kupita ku moyo wa Tsiku Lomaliza. kotero, tipeza kuti kuvulala kwauzimu n’koopsa kwambiri poyerekezera ndi kuvulala kwuthupi mdziko dziko lino lapansi.
M’sura iyi, mawu oti “An-Naas” abwerezedwa kasanu. Kaŵirikaŵiri, m’nzoyankhula ngati kutchulidwa kwa chinthu chimene chatchulidwa kale kwachitika momvekera bwino, ndiye kuti munthu amangokhutitsidwa pa chizindikiro chabe. Komabe, m’ndime iyi, mawuwo (An-Naas) akubwerezedwanso.
Ma Ulama ena akufotokoza kuti chifukwa chimene liwu loti An-Naas linabwerezedwera kasanu ndi chifukwa cha magawo asanu osiyanasiyana amene munthu amadutsamo pa moyo wake.
Pachiyambi, iye ndi mwana ndipo akusowekera. Allah Ta’ala kwambiri. Choncho, Allah Ta’ala akutiphunzitsa kuti tizifunafuna chitetezo ndi kubisalira kwa Iye. Allah Ta’ala akuti,
قُلْ اَعُوۡذُ بِرَبِّ النَّاسِ
Nena: “Ndikudzitchinjiriza ndi Mbuye wa anthu (Allah Ta’ala).
Rabb akunena za amene amayang’anira zolengedwa zonse, kuwathandiza pamene akukula ndi kupita patsogolo kuchokera ku gawo lina kupita ku gawo, ndi kuona zokonda zawo ndi zosowa zawo nthawi iliyonse. Choncho, pa chiyambi, mwana akamakula, liwu loti Rabb linali loyenera kugwiritsidwa ntchito pofotokoza chosowa cha munthu kwa Allah Ta’ala.
Pamene munthu akupita chitsogolo kukhala m’nyamata ndipamene amakweranso mantha omuopa Allah Choncho, kudzera mu liwu lakuti مَلِکِ النَّاسِ Allah Ta ‘ala akulingalira ndi kuonetsa kuti tiyenera kufunafuna chitetezo kwa mfumu yeniyeni komanso yapamwamba ‘yemwe ndi Allah Ta’ aala.
Gawo lachitatu la moyo wa munthu ndi pamene akukalamba. Nthawi zambiri, munthu akayandikira mapeto a moyo amazindikira kuti akufunika kutembenukira kwambiri kwa Allah Ta’ala pomupembedza ndi kumumvera, ndipo potero amayesetsa kuchita chilungamo ndi kupembedza Allah Ta’ala. Chifukwa chake, ponena za siteji iyi, liwu lakuti اِله النَّاسِ linagwiritsidwa ntchito. M’mawu ena, munthu atembenuke kwambiri kwa Allah Ta’ala ndi kupempha chitetezo kwa Iye, pakuti Iye ndi Allah wa anthu, Mulungu mmodzi yekha. Mbiri zitatuzi ndi mbiri za Allah Ta’ala mwachitsanzo Rabb, Malik ndi Ilaah, zonse zikusonyeza kukwanitsa kuteteza.
Kunena za mawu loti Rabb, m’chiyankhulo cha charabu akanenedwa kuti ndi chinthu, ndiye kuti amapereka tanthauzo la umwini, mwachitsanzo رب الدار– mwini nyumba ndi رب العبد – mwini wa kapolo. kotero, liwu loti “rabbi” limasonyeza kuteteza popeza mwini wake kaŵirikaŵiri amada nkhaŵa ndi zinthu zake ndipo amayesetsa kuzisamalira ndi kuzitetezera.
Mawu oti Malik (mfumu) amatanthauza kuteteza monga momwe mfumu nthawi zambiri imaganizira za ubwino pa chitetezo cha anthu ake.
Momwemonso mau oti Ilaah (Umulungu/Mulungu) akusonyeza kuteteza monga momwe Ilaah (Mulungu/Mulungu) akukhudzidwira ndi zolengedwa Zake. Choncho, pamene Allah Ta’ala ali ndi mbiri zonse zitatuzi, ndiye amafuna kuti Allah Ta’ala ateteze zolengedwa Zake, ndipo sipadzakhala chitetezo choposa chitetezo cha Allah Ta’ala.
Nthawi yachinayi yomwe liwu lakuti An-Naas likutchulidwa, likunena za chikhalidwe chimene munthu amakumana nacho pa moyo wake onse, pamene Shaytwaan nthawi zonse amayesa kumsokeretsa ndi kumusokoneza polowetsa maganizo oipa ndi manong’onong’ono mumtima mwake. Choncho, munthu akuphunzitsidwa kuti ayenera nthawi zonse kufunafuna chitetezo mwa Allah Ta’ala kwa Satana.
Nthawi yachisanu, An-Naas akubwerezedwanso, akunena za atumiki a Shaytaan amene amamuthandiza Shaytaan pa ntchito yake yosokeretsa zolengedwa. Mwa othandizira ake pali ma shayateen ena komanso anthu oyipa. Monga momwe zimawonedwera, anthu omwe munthu amakhala nawo amakhudza kwambiri malingaliro ake ndi khalidwe lake, ndipo mauthenga osakhala bwino amadutsa kuchokera pamtima kupita kumtima, zomwe zimapangitsa kuti kawonedwe ka zinthu kake ndi kaganizidwe kake ka moyo kasinthe.
Satana, M’nong’onezi
M’surayi Allah Ta ‘ala akumutchula Shaitaan kuti الْوَسْوَاسِ. Mawu akuti الْوَسْوَاسِ kwenikweni amatanthauza ‘kunong’ona’, (omwe m’chinenero cha Chiarabu, amaimira tsinde la liwu limene aneni onse amachokera). Choncho, Allah Ta’ala amamutcha Shaitaan ndi dzina limeneli pogwiritsa ntchito tsinde la liwu losonyeza kukhoza kwake kwakukulu komwe ali nako posocheretsa munthu kudzera mu manong’onong’o ake oipa.
Ma Ulama akufotokoza kuti mu mtima wauzimu wa munthu muli zigawo ziwiri. M’gawo lina muli mngelo amene amasonkhezera munthu kuchita zabwino. Izi zili kumanja kwa mtima wa munthu. Kumbali yakumanzere kwa mtima wa munthu muli gawo lina m’mene muli Shaytwaan yemwe amalimbikitsa ndi kumunyengerera munthu kuchita zoipa.