Tafseer Ya Surah Faatihah

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ ‎﴿١﴾‏ الْحَمْدُ لِلَّهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ ‎﴿٢﴾‏ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ ‎﴿٣﴾‏ مَالِكِ يَوْمِ الدِّينِ ‎﴿٤﴾‏ إِيَّاكَ نَعْبُدُ وَإِيَّاكَ نَسْتَعِينُ ‎﴿٥﴾‏ اهْدِنَا الصِّرَاطَ الْمُسْتَقِيمَ ‎﴿٦﴾‏ صِرَاطَ الَّذِينَ أَنْعَمْتَ عَلَيْهِمْ غَيْرِ الْمَغْضُوبِ عَلَيْهِمْ وَلَا الضَّالِّينَ ‎﴿٧﴾‏

Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah, Mbuye wa zolengedwa zonse. Wachifundo Chambiri, Wachisoni. Mbuye wa tsiku lachiweruzo. Inu nokha timakupembedzanindipo kwa Inu nokha ndi kumene timakupemphani chithandizo. Tiwonetseni njira yowongoka Njira ya amene mudawadalitsa (ndi chisomo Chanu), osati njira ya iwo amene mudawakwiyira, kapena njira ya amene asokera.

Sura Yoyamba

Surah Faatihah ndi surah yoyamba mu Qur’aan yopatulika. Si surah yoyamba yokha yomwe ili m’ndondomeko zotsatizana za surah za Qur’aan zomwe zilipo, komanso ndi surah yoyamba imene idavumbulutsidwa ndi Allah Ta’ala. Surah Faatihah isadavumbulutsidwe, ngakhale kuti aya za Surah Alaq ndi Surah Muddathir zidavumbulutsidwa, komabe palibe Sura yathunthu siyidavumbulutsidwe surah Faatihah isanadze.

Chifukwa chomwe Surayi Faatihah idayikidwira patsogolo pa Surah ina iliyonse ya Qur’aan Majiid ndikuti Sura Faatihah ndiye maziko a Qur’aan Majiid, ndipo m’nkhani yake ikuphatikiza mitu itatu ikulu ikulu ya Qur’aan Majiid. Choncho, zili ngati Qur’aan Majiid yotsalayo yomwe yandondozana ndi Surah Faatihah ili ngati ndemanga yake pofotokoza mitu yake itatu.

Mitu itatu ikuluikulu ya Qur-aan Majiid

M’menemo chidziwitso chomwe chili mu Qur’aan Majiid yonse chikukhudzana ndi umodzi mwa mitu itatu; (1) kubweretsa Imaan mu umodzi wa Allah Ta’ala ndi mu makhalidwe (iyeyo kukhala Mulungu) ake umulungu, (2) kuchita a’amaal-e-swaalihah (ntchito zabwino), (3) moyo wa tsiku lomaliza.

Mfundo zazikuluzikulu za mitu yonse itatuyi zatchulidwa ndikusonyezedwa mu Surah Faatihah. Pachifukwa ichi ndipamene mwa maina omwe Surah Faatihah yapatsidwa, monga momwe yatchulidwira mmahadith, ndi maina akuti “Ummul Qur’aan” (Mayi wa Qur’aan), “Ummul Kitaab” (Tsinde la Qur’an). Buku), ndi “Qur’aan-ul-Adhwiim (Qur’aan yolemekezeka)”.

Uthenga wa Surah Faatihah

Munthu akalingalira mwakuya nkhani ya surayi akhoza kuzindikira kuti ndi uthenga ochokera kwa Allah Ta’ala kwa munthu okhudza momwe angapembedzere Allah Ta’ala ndi kufunafuna chiongoko kwa lye. Choncho, M’sura imeneyi, munthu akupempha Allah Taala kuti amuonetse njira ya amene Allah wawaongola ndi kumupulumutsa kunjira ya amene adakwiiridwa ndi njira ya amene adasokera.

Allah Ta’ala akuyankha pempho la munthu pomupatsa chiongoko chomwe chavumbulutsidwa m’Qur’aan Majiid. Choncho, zili ngati kuti Qur’aan Majiid yonse ndi yankho la pempho limene likupezeka mu Surah Faatihah.

Kukhanzikika Kwa uthenga wa Surah Faatihah

Cholinga cha uthenga wa surayi ndikuti munthu apindule kudzela mu Qur’aan Majiid, akufunika kubweretsa imaan m’nkhani zoyamba za chikhulupiriro mwachitsanzo. (1) Kukhulupirira mu umodzi wa Allah Taala (2) kukhulupirira m’mbiri zake zonse za umulungu zokongola (3) Kukhulupirira za tsiku lomaliza (4) kukhulupirira chiwerengero cha tsiku lachiweruzo (5) kukhulupirira utumiki wa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) (6) kutsatira njira ya akapolo osankhidwa a Allah Ta’ala (Ambiyaa [‘Alaihimus salaam]) (7) kusiya njira za adani Ake zomwe zimatsogolera ku kusamuvera kwake.

Momwemonso surayi ikumulondolera munthu kukwaniritsa cholinga chake potembenukira kwathunthu kwa Allah Ta ‘ala pomupembedza, kufunafuna chiongoko ndi chithandizo kwa lye.

Ngati munthu aiwerenga surayi ndi kuiphunzira ndi maganizo otseguka ndi mtima woona, monga ofunafuna chowonadi, ndithudi adzadalitsidwa ndi chiongoko choona chochokera kwa Allah Ta’ala.

Ubwino wa Surah Faatihah

Mwa ma ubwino a Surah Faatihah, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) wanena kuti surayi imachiza matenda amtundu uliwonse. Malinga ndi Hadith ina, surayi ikutchedwanso kuti “As-Shifaa” (Machiritso a Matenda Onse).

Ndipo zanenedwanso kuchokera kwa Anas (radhwiyallahu ‘anhu) kuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) waitcha surayi kuti ndi sura yaikulu kwambiri pakati pa ma surah onse a Qur’aan Majiid.

Mu Hadith ina Abu Hurairah (radhwiyallahu ‘anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Ndikulumbirira Allah Ta’ala yemwe ndi Mbuye wa moyo wanga, kuti palibe bukhu ngakhale Towrah, Injili ngakhalenso Zabuur kapena gawo lina lililonse la Qur’an lomwe lingafanane ndi Surah Faatihah.”

Ma Ulama akufotokoza kuti ma buku omwe adavumbukutsidwa kuchokera kwa Allah alipo pafupifupi 104, ndipo mauthenga a mabuku onsewa ali m’mabuku anayi otchuka; Zabuur, Tawrah, Injili ndi Qur’aan. Uthenga wa mabuku onsewa wafupikitsidwa mu Qur’aan, ndipo uthenga ofunikira wa Qur’aan waphatikizidwa mu Surah Faatihah. Kuonjezera apo, mfundo ndi phata la Surah Faatihah likupezeka m’mawu akuti “Bismillahir Rahmaanir Raheem”

Tsinde la Bismillah

بِسۡمِ اللّٰہِ الرَّحۡمٰنِ الرَّحِیۡمِ

M’dzina la Allah, Wachifundo Chambiri, Wachisoni

Chinali chizolowezi ndi machitidwe a anthu m’nthawi ya umbuli Chisilamu chisanadze kuti akayamba ntchito iliyonse kapena akayamba kalikonse, ankatchula mayina a mafano awo kuti apeze madalitso. Allah Ta’ala adachotsa zoipa za anthu osapembedzazi ndipo adawalangiza kuti m’malo momatchula mayina a milungu yawo yonyenga, azitchula dzina la Allah Ta’ala akamayamba ntchito iliyonse kapena kuchita chilichonse.

Kunena zoona, moyo wa nsilamu umayendetsedwa ndi chikhulupiriro ndi kutsimikiza kuti ndi chisomo cha Allah ndi thandizo la Allah Ta’ala kuti ntchito zonse zitheke. Choncho, nsilamu amaphunzitsidwa kuwerenga Bismillah potsegula kapena kutseka chitseko, povindikira chiwiya chilichonse, poyamba kudya kapena kumwa, ponyamuka ulendo, pokwera kapena potsika, ndi zina zotero.

Pamene tikunena kuti “Bismillah” m’dzina la Allah, ndiye kuti tikunena kuti tikuyamba ntchito yathu ndi dzina la Allah Ta’ala ndi chithandizo Chake ndi madalitso Ake. Mu kuyankhula kwina, tikuvomereza kuti popanda Allah Ta ‘ala, sitingathe kugwira ntchito iliyonse kapena kumaliza ntchito iliyonse, ngakhale ntchitoyo itakhala yochepa bwanji.

Kwenikweni, gawo lililonse la moyo wa nsilamu liyenera kuyamba ndi kutchula dzina la Allah Ta’ala. Choncho, momwemonso, tisanayambe kuwerenga Qur’aan yolemekezeka, tikulamulidwa kuwerenga Bismillah. Chifukwa chowerengera Bismillah ndicholinga chofuna thandizo ndi madalitso a Allah Ta ‘ala kuti awerenge Qur’aan Majiid molondola komanso kuti athe kumvetsa uthenga wa Qur’aan ndi kupeza chiongoko chapadera kudzera m’menemo.

الْحَمْدُ لِلَّهِ

Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah

Sura iyi yayamba ndi mau oti “Alhamdulillah” (Kutamandidwa konse ndi kwa Allah), kutanthauza kuti kuyamikidwa konse ndi kwa Allah Ta’ala yekha. Munthu amene amatamanda cholengedwa chilichonsecho padziko lonse lapansi, ndiye kuti akuyamika mlengi wa zinthu zonse Allah Ta’ala, monga kusangalalira kwa chinthu chilichonse kwenikweni ndiko kukopa kwa ochipanga.

Choncho, pamene Allah Ta’ala ndi Yemwe adalenga chinthu chilichonse, ndiye kuti kuyamika chinthucho ndiko kulemekeza Mlengi wake, popeza Iye ndi amene adachipatsa kukongola ndi kusalala.

Munthu akalilingalira dziko lapansi ndi zolengedwa zapadziko lapansi, ndiye kuti chinthu chilichonse chimakopa chidwi cha munthu ku kukongola kwake ndi kusalala kwake, koma akayang’ana kupyola chophimbacho kuti awone yemwe akulamulira chilichonse m’chilengedwe ndikuchilola kuti chizigwira ntchito mogwirizana. Ndithu munthu adzazindikira kuti si wina koma Allah Taala yekha.

M’menemo, cholengedwa chilichonse, mu kukongola ndi kusalala kwake, ndi chizindikiro cha ukulu ndi mphamvu za Allah Ta’ala yekha.

Munthu akazindikira kuti pali wina wake m’chilengedwe chonse amene ali oyenera kutamandidwa konse, ndiye kuti ayenera kumvetsetsa kuti Umunthu waukulu uwu okha uyenera kukhala oyenera kupembedzedwa. Choncho, tikuwona kuti ngakhale mawu oti “Alhamdulillah” (Kutamandidwa konse ndi kwa Allah) akhala akugwiritsidwa ntchito kutanthauza kutamandidwa, komabe, mwa tanthauzo lake, amadula mizu ya shirk (mishirikina) ndi kupembedza zolengedwa zonse, ndiponso nthawi yomweyo ikukhazikitsa chikhulupiriro cha Tawhiid (kubweretsa chikhulupiriro mu umodzi wa Allah Taala).

Choncho, tikumvetsa kuti ndime yoyamba ya Qur’an yopatulika imakhazikitsa maziko a Chisilamu (Tawhiid – umodzi wa Allah Ta’ala).

Rabbi (Mbuye)wa zolengedwa zonse

رَبِّ الْعٰلَمِينَ

Rabbi (Mbuye)wa zolengedwa zonse

Mawu oti “Rabbi” akutanthauza Munthu amene amabweretsa cholengedwa chilichonse, kenako amachidyetsa ndi kuchisamalira ndi kuchipititsa patsogolo pang’onopang’ono m’milingo yosiyanasiyana ya chitukuko, mpaka kukafika ku ungwiro. Choncho, tikuphunzira kuti mbiri yoti Rabbi ndi yopatulika ndi ya Allah Ta’ala yekha ndipo palibe amene akugawana nayo.

“عٰلمين” (zolengedwa) akutanthauza maiko osiyanasiyana kapena mapulaneti osiyanasiyana amene Allah Ta ‘aala adalenga. Dziko limodzi ndi dziko limene tikukhalali. Dzikoli limaoneka kwa anthu. Komabe, palinso maiko kapena mapulaneti ena ambiri omwe adalengedwa ndi Allah Ta’ala omwe samaoneka kwa munthu.

Mawu oti “عٰلمين” angatanthauzenso mitundu yosiyanasiyana ya zolengedwa monga anthu, nyama, jinnaat (ziwanda) ndi Malaa’ikah (angelo), ndi zina zotero. Zolengedwa izi nthawi zina zimatchulidwa kuti zosiyana dziko (dziko la anthu, dziko la ziwanda, dziko la nyama, etc.).

Choncho, Allah Ta’ala akamanena kuti “الحمد لله رب العٰلمين” (Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah, Mbuye wa zolengedwa), ndiye kuti kutamandidwa konse ndi kwa Iye amene wapereka moyo ku cholengedwa chilichonse, amachidyetsa ndi kuchilera. ndipo amawasamalira kuyambira pachiyambi mpaka kumapeto kwa dziko limene akukhalamo.

Wachifundo Chambiri, Wachisoni

الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ

Wachifundo Chambiri, Wachisoni

“Ar-Rahmaan” ndi “Ar-Rahiim” zonse ndi mbiri ya Allah Ta’ala, kutanthauza chifundo Chake chopyola malire. Koma kusiyana pakati pa mbiri ziwirizi ndi kwakuti “Ar-Rahmaan” ikusonyeza kukula kwa chifundo Chake, pamene “Ar-Rahiim” ikunena za kuzama kwa chifundo Chake.

Mbuye wa tsiku lachiweruzo

مَالِكِ يَوْمِ الدِّينِ ‎﴿٤﴾

Mfumu ya tsiku lachiweruzo

Ngakhale Allah Ta’ala kukhala Mbuye ndi Mwini cholengedwa chilichonse ndi chilichonse chomwe chili m’chilengedwe chonse nthawi zonse, Allah Ta’ala wadzifotokoza yekha m’ndime iyi kuti ndi Mbuye ndi Mwini tsiku lachiweruzo mwachindunji.

Ma Ulama akufotokoza kuti chifukwa cha izi ndikuti padziko lapansi Allah Ta’ala adampatsa munthu umwini wa zinthu zina zapadziko lapansi, ndipo Allah Ta’ala adawapatsa anthu ena mphamvu ndi ulamuliro olamulira anthu ndi mbali zina za dziko, Komabe, pa tsiku lachiweruzo, umwini ndi ulamuliro wa munthu aliyense zidzatha ndipo sipadzakhala cholengedwa chimene chidzakhale ndi ulamuliro pa munthu aliyense kapena chinthu. Kudzakhala chiweruzo cha Allah Ta’ala chomwe chidzapambane onse pa tsiku limenelo. Choncho, Allah Ta’ala akudzifotokoza yekha ngati Mbuye wa tsiku lachiweruzo.

Machitidwe a Dziko Lino Poyerekeza ndi Tsiku Lomaliza

Allah Ta’ala adalenga dziko lapansi kukhala malo ochitirapo zochita, ndi tsiku lomaliza kukhala malo olipidwa zochita zake.

Ngati munthu abweretsa Imaan (chikhulupiliro) ndikuchita zabwino padziko lino lapansi, adzalipidwa popatsidwa Jannah pa zabwino zomwe adachita padziko lapansi. Choncho, ngati munthu alibe Imaan (Dini) ndikukhala moyo wa ukafiri ndi shirk padziko lapansi, ndiye kuti adzalangidwa ndikuponyedwa ku Jahannum pa tsiku lahciweruzo chifukwa chosakhulupirira mwa Allah Ta’ala ndi Dini ya Chisilamu.

Munthu akakapenda kakhalidwe ka dziko lapansi, atha kupeza kuti chilungamo chonse sichingachitike, popeza chuma, mphamvu ndi chikoka zili m’manja mwa anthu abwino ndi oipa. Kotero, nthaŵi zina, chilungamo chimaperekedwa kwa olakwa, ndipo nthaŵi zina, olakwa, chifukwa cha kusonkhenzera kwake, amatha kuthaŵa malamulo a chilungamo. Zotsatira zake n’zakuti anthu osalakwa amaonedwa ngati zigawenga, ndipo aupandu amaonedwa ngati osalakwa. Choncho, Allah Ta’ala adalenga tsiku lomaliza kukhala malo okhalamo pomwe chilungamo chidzaperekedwa kwa aliyense.

Chimenecho chidzakhala chilungamo cha Allah Ta’ala pa tsiku lachiweruzo kuti chikadapondereza chilombo chopanda nyanga padziko lapansi pochidula ndi nyanga zake, Allah Ta’ala adzaziukitsa nyama zonse ziwiri ndikulola chilango kuti chichitike. pakati pawo.

Kunena zoona, Allah Ta’ala adalenga tsiku lomaliza kukhala malo amene chilungamo chidzaperekedwa kwa zolengedwa Zake zonse ndipo zolengedwa zonse zidzalipidwa zochita zawo. Pachifukwachi Allah Ta’ala adadzitcha yekha Mbuye wa tsiku lachiweruzo, chifukwa chidzakhala chigamulo Chake ndi chiweruzo Chake chomwe chidzawapeze onse.

Kutembenukira kwa Allah Ta’ala Yekha Kuti Akuthandize

إِيَّاكَ نَعْبُدُ وَإِيَّاكَ نَسْتَعِينُ ‎﴿٥﴾

Inu nokha tikupembedzani, ndipo kwa Inu nokha ndi komwe timapempa chithandizo.

M’chinenero cha Chiarabu, liwu lakuti ibaadah (kupembedza) limatanthauza kusonyeza kudzichepetsa kotheratu ndi kugonjera chifukwa cha chikondi ndi ulemu waukulu kwa wina. Mkhalidwe woterewu wosonyeza kugonjera ndi mtima wonse, ndi chikondi chachikulu ndi ulemu, sizingagwiritsidwe ntchito mwachilungamo kwa wina aliyense kupatula kwa Allah Ta’ala.

Choncho, pamene tikunena kuti, “Inu nokha ndiye amene tikupembedzani,” ndiye kuti kwenikweni, tikunena kuti tadzipereka tokha ku kumvera ndi kulambira Kwake, ndi chikondi chakuya ndi ulemu, chifukwa chakuti Iye ndiye Mlengi wathu ndi Otisamalira.

Pamene tikunena kuti: “Tikupempha thandizo kwa Inu nokha,” tikuvomereza kuti ndi chigamulo cha Allah ndi lamulo lake kuti chinthu chilichonse chikhalepo, choncho Iye yekha ndi amene ali ndi mphamvu pa zochitika zathu zonse. Choncho, ngati tigwiritsa ntchito njira zapadziko lapansi kupanga zinthu, ndiye kuti tikuchita izi chifukwa cha lamulo Lake, ndipo Sitingakhale ndi maganizo onena kuti ndi njira yabwino yokwaniritsira cholinga chathu, koma tidzakhulupilira kuti ndi chilorezo cha Allah. njirazo zikhoza kukhala zothandiza.

Choncho, njira iliyonse yomwe Allah Ta’ala adailetsa kugwiritsa ntchito munthu ayenera kusiya kugwiritsa ntchito njira imeneyi, chifukwa izi zidzapangitsa munthu kutsutsana ndi Allah Ta’ala ndi kutsamira ku njira za haraam, mwachitsanzo: kutenga ngongole zokhala ndi chiwongola dzanja kubanki kuti munthu adzipeza ndalama zambiri kapena kutenga inshuwaransi kuti ateteze chuma chake.

Tsinde La Mavesi Atatu Oyamba

M’ndime zitatu zapitazi, munthu akuvomereza kudalira kwake mwa Allah Ta’ala m’mbuyomu, masiku ano ndi amtsogolo.

M’ndime yoyamba, Allah Ta’ala akulongosola kuti Allah ndi Mbuye wa zolengedwa zonse. Allah Ta’ala akuti: “Kuyamikidwa konse ndi kwa Allah, Mbuye wa zolengedwa”. Kuchokera m’ndime iyi, tikuphunzira kuti Allah Ta’la yekha ndi Yemwe adampangitsa munthu kuti apezeke pano pa dziko lapansi ndipo Allah Ta’la yekha ndi amene amamudyetsa ndi kumusamalira pamlingo uliwonse wa moyo. Choncho, munthu akuyenera kuvomereza kudalira kwake mwa Allah Ta’ala m’mbuyomu.

M’ndime yachiwiri, Allah Ta’ala akufotokoza ubwino Wake wa umulungu osonyeza kukoma mtima ndi chifundo kwa zolengedwa Zake zonse. Allah Ta’ala akuti: “Wachifundo Chambiri, Wachisoni.” Kuchokera m’ndime iyi, tadziwa kuti nthawi iliyonse ya moyo wa munthu padziko lapansi pano, munthu amadalira Allah Ta’ala kuti apitirizebe kukhala moyo ndi kupulumuka kwake. Choncho, munthu ayenera kuvomereza kudalira kwake mwa Allah Ta’ala padakali pano.

M’ndime yachitatu, Allah Ta’ala akulongosola kuti Iye ndi Mbuye wa tsiku lachiweruzo. Allah Ta’ala akuti: “Mbuye wa tsiku lachiweruzo.” Kuchokera mu aya iyi, tikuzindikira kuti tsiku lomaliza munthu adzadalira Allah Ta’ala kuti apulumutsidwe. Choncho, munthu ayenera kuvomereza kudalira kwake mwa Allah Ta’ala mtsogolomo.

Munthu akazindikira ndikuvomereza kuti adali odalira Allah Taala kale, iye akupitirizabe kudalira Allah Taala pakali pano, ndipo adzadalira Allah Ta’ala kutsogoloku, kenako zotsatira za chilengedwe ndi Zotsatira za kudalira kumeneku ndikuti munthu apembedze Iye yekha ndi kufunafuna chithandizo ndi chipulumutso kwa Iye yekha popeza palibe amene angamthandize kapena kumuthandiza m’njira ina iliyonse kupatula Allah Ta’ala.

Ndime iyi ikutiphunzitsanso kuti poti munthu ayenera kupembedza Allah Ta’ala yekha ndikupempha thandizo kwa Iye yekha, ndiye kuti sajdah, tawaaf kumupempha wina kusiya Allah Ta’ala nkosaloredwa. M’malo mwake, chikondi, mantha ndi chiyembekezo cha munthu mwa Allah Ta’ala ziyenera kukhala zamphamvu kuposa chikondi, mantha ndi chiyembekezo cha munthu kapena chinthu china chilichonse. Palibe chimene chiyenera kukhala chofunika kwambiri kwa munthu kuposa kukhulupirika kwake ndi ubale wake ndi Allah Ta’ala.

Kudzera mu kumupempha Allah Ta’ala kuti atithandize, ndiye kuti tikumupempha chithandizo Chake, kaya pazadziko lapansi kapena tsiku lomaliza.

Chinsinsi cha Surah Faatihah

Ma Ulama a Tafseer akufotokoza kuti tanthauzo la Qur’aan yonse likupezeka mu Surah Faatihah, ndipo tanthauzo la Surah Faatihah likupezeka m’ndime iyi “إياك نعبد وإياك نستعين” (Inu nokha tikupembedzani ndipo inu nokha tikupemphani chithandizo).

Tikaionetsetsa ndime imeneyi, tipeza kuti ili ndi zigawo ziwiri. Gawo loyamba ndi loti, “Inu nokha timakupembedzani”, ndipo gawo lachiwiri ndi loti, “ndipo inu nokha timakupemphani thandizo”.

Gawo loyamba la ndime iyi ndikulengeza kwa munthu kukhala opanda shirk (kumphatikiza Allah ndi zinthu zina).

Gawo lachiwiri ndi kulengeza kwa munthu kudalira Allah yekha, ndipo osayika chidaliro pa cholengedwa chilichonse kuti chikwaniritse zofuna ndi zokhumba zake.

Kufotokozera kwa Gawo Loyamba (Inu nokha timakupembedzani)

Monga tafotokozera kale, liwu lakuti ibaadah (kupembedza) limatanthauza kusonyeza kudzichepetsa kotheratu ndi kugonjera mwa wina wake chifukwa chomukonda kwambiri ndi kumulemekeza. Mwachionekere, kugonjera uku sikungaonetsedwe kwa wina aliyense kupatula Allah Ta’ala.

Choncho, ngati wina ataonetsa kugonjera kopanda malire kwa munthu otero ndi kumumvera iye motsutsana ndi lamulo la Allah, ndiye kuti iyi idzatengedwa kuti shirk.

Kuchokera apa, tikuzindikira kuti shirk (kumphatikiza Allah Ta’ala) siili m’mapemphero opembedza ndipo siimachitika popembedza miyala ndi zitsulo kokha monga momwe amachitira opembedza mafano, koma imachitikanso pomvera, kumulemekeza kapena kumukonda wina pa mlingo oyenera kuonetsa kwa Allah.

M’Qur’aan yolemekezeka, Allah Ta’ala akufotokoza za Ayuda ndi Akhrisitu, ndi zochita za shirk zomwe adali nazo pomvera ndi kulemekeza ma Azibusa ndi Ansembe awo motsutsana ndi malamulo a Allah Ta’ala. Allah akuti:

اتَّخَذُوٓا۟ اَحْبَارَهُمْ وَرُهْبَانَهُمْ أَرْبَابًا مِّن دُونِ اللَّهِ

Adawatenga akatswiri awo achipembedzo ndi ansembe kukhala milungu kusiya Allah Ta’ala… (Surat Taubah v. 31).

Olemekezeka Adiyy bin Haatim (Radhiyallahu ‘anhu) adali Sahaabi wa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) yemwe adali mkhristu asadalowe Chisilamu. Tsiku lina adadza kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) namufunsa kuti: “E, Mtumiki wa Allah! N’chifukwa chiyani Qur’aan imawadzudzula Akhrisitu chifukwa chowatenga akatswiri awo achipembedzo kukhala milungu, pomwe iwo si olakwa pakuchita shirk kudzera mu kuwapembedza?”

Naye Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamufunsa kuti: “Kodi n’zoona kuti akatswiri awo achipembedzo akamalengeza zinthu zina kuti ndi haraam, ngakhale kuti Allah Ta’ala adazilengeza kuti ndi halaal, ndipo adalengeza zambiri kuti halaal pomwe Allah Ta’ala Adalengeza kuti ndi Haram, kenako adamvera akatswiri awo motsutsana ndi lamulo la Allah Taala?

Adiyy bin Haatim (Radhiyallahu ‘anhu) adavomereza kuti izi nzoona. Pamenepo Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Umu ndi momwe amapembedzera ansembe awo.

Izi zikutsimikizira kuti Allah Ta’ala yekha ndiye ali ndi udindo okhazikitsa zomwe zili halaal ndi haraam. Choncho, ngati munthu akhulupirira kuti wina wake ali ndi udindo olengeza kuti halaal ndi haraam, ndiye kuti munthuyo wachita shirk popeza wamupanga wina wake kukhala mnzake wa Allah yemwe ali ndi udindo olengeza kuti halaal kapena haraam. kotero amakhala ngati akumpembedza munthu ameneyo.

Check Also

Tafseer Ya Surah Nasr

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ إِذَا جَاءَ نَصْرُ اللَّهِ وَالْفَتْحُ ‎﴿١﴾‏ وَرَأَيْتَ النَّاسَ يَدْخُلُونَ فِي دِينِ اللَّهِ أَفْوَاجًا ‎﴿٢﴾‏ فَسَبِّحْ …