Tafseer Ya Surah Naba

عَمَّ يَتَسَاءَلُونَ ‎﴿١﴾‏ عَنِ النَّبَإِ الْعَظِيمِ ‎﴿٢﴾‏ الَّذِي هُمْ فِيهِ مُخْتَلِفُونَ ‎﴿٣﴾‏ كَلَّا سَيَعْلَمُونَ ‎﴿٤﴾‏ ثُمَّ كَلَّا سَيَعْلَمُونَ ‎﴿٥﴾‏ أَلَمْ نَجْعَلِ الْأَرْضَ مِهَادًا ‎﴿٦﴾‏ وَالْجِبَالَ أَوْتَادًا ‎﴿٧﴾‏ وَخَلَقْنَاكُمْ أَزْوَاجًا ‎﴿٨﴾‏ وَجَعَلْنَا نَوْمَكُمْ سُبَاتًا ‎﴿٩﴾‏ وَجَعَلْنَا اللَّيْلَ لِبَاسًا ‎﴿١٠﴾‏ وَجَعَلْنَا النَّهَارَ مَعَاشًا ‎﴿١١﴾‏ وَبَنَيْنَا فَوْقَكُمْ سَبْعًا شِدَادًا ‎﴿١٢﴾‏ وَجَعَلْنَا سِرَاجًا وَهَّاجًا ‎﴿١٣﴾‏ وَأَنزَلْنَا مِنَ الْمُعْصِرَاتِ مَاءً ثَجَّاجًا ‎﴿١٤﴾‏ لِّنُخْرِجَ بِهِ حَبًّا وَنَبَاتًا ‎﴿١٥﴾‏ وَجَنَّاتٍ أَلْفَافًا ‎﴿١٦﴾‏ إِنَّ يَوْمَ الْفَصْلِ كَانَ مِيقَاتًا ‎﴿١٧﴾‏ يَوْمَ يُنفَخُ فِي الصُّورِ فَتَأْتُونَ أَفْوَاجًا ‎﴿١٨﴾‏ وَفُتِحَتِ السَّمَاءُ فَكَانَتْ أَبْوَابًا ‎﴿١٩﴾‏ وَسُيِّرَتِ الْجِبَالُ فَكَانَتْ سَرَابًا ‎﴿٢٠﴾‏ إِنَّ جَهَنَّمَ كَانَتْ مِرْصَادًا ‎﴿٢١﴾‏ لِّلطَّاغِينَ مَآبًا ‎﴿٢٢﴾‏ لَّابِثِينَ فِيهَا أَحْقَابًا ‎﴿٢٣﴾‏ لَّا يَذُوقُونَ فِيهَا بَرْدًا وَلَا شَرَابًا ‎﴿٢٤﴾‏ إِلَّا حَمِيمًا وَغَسَّاقًا ‎﴿٢٥﴾‏ جَزَاءً وِفَاقًا ‎﴿٢٦﴾‏ إِنَّهُمْ كَانُوا لَا يَرْجُونَ حِسَابًا ‎﴿٢٧﴾‏ وَكَذَّبُوا بِآيَاتِنَا كِذَّابًا ‎﴿٢٨﴾‏ وَكُلَّ شَيْءٍ أَحْصَيْنَاهُ كِتَابًا ‎﴿٢٩﴾‏ فَذُوقُوا فَلَن نَّزِيدَكُمْ إِلَّا عَذَابًا ‎﴿٣٠﴾‏ إِنَّ لِلْمُتَّقِينَ مَفَازًا ‎﴿٣١﴾‏ حَدَائِقَ وَأَعْنَابًا ‎﴿٣٢﴾‏ وَكَوَاعِبَ أَتْرَابًا ‎﴿٣٣﴾‏ وَكَأْسًا دِهَاقًا ‎﴿٣٤﴾‏ لَّا يَسْمَعُونَ فِيهَا لَغْوًا وَلَا كِذَّابًا ‎﴿٣٥﴾‏ جَزَاءً مِّن رَّبِّكَ عَطَاءً حِسَابًا ‎﴿٣٦﴾‏ رَّبِّ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَمَا بَيْنَهُمَا الرَّحْمَٰنِ ۖ لَا يَمْلِكُونَ مِنْهُ خِطَابًا ‎﴿٣٧﴾‏ يَوْمَ يَقُومُ الرُّوحُ وَالْمَلَائِكَةُ صَفًّا ۖ لَّا يَتَكَلَّمُونَ إِلَّا مَنْ أَذِنَ لَهُ الرَّحْمَٰنُ وَقَالَ صَوَابًا ‎﴿٣٨﴾‏ ذَٰلِكَ الْيَوْمُ الْحَقُّ ۖ فَمَن شَاءَ اتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِ مَآبًا ‎﴿٣٩﴾‏ إِنَّا أَنذَرْنَاكُمْ عَذَابًا قَرِيبًا يَوْمَ يَنظُرُ الْمَرْءُ مَا قَدَّمَتْ يَدَاهُ وَيَقُولُ الْكَافِرُ يَا لَيْتَنِي كُنتُ تُرَابًا ‎﴿٤٠﴾‏

Kodi akufunsana zachani? Za chochitika chachikulu chija, chomwe amatsutsana nacho? Ayi! Posachedwapa adzadziwa. Kachiwiri, ayi! Posachedwapa adzadziwa. Kodi sitidaichite nthaka kukhala ngati choyala chapansi, ndi mapiri kukhala ngati zikhomo; Ndipo takulengani awiriawiri (amuna ndi akazi), ndipo Tidalichita tulo tanu kukhala mpumulo. Ndipo taupanga usiku kukhala ngati chovala (pokuvindikirani ndi mdima wake) Ndipo taupanga usana kukhala nthawi yopezera zofunika za pamoyo wanu. Ndipo tamanga pamwamba panu thambo zisanu ndi ziwiri zolimba; Ndipo tidalenga nyali younikira (dzuwa), ndipo tatsitsa madzi ochuluka kuchokera kumitambo yodzadza ndi mvula;

Ndithu, tsiku lachiweruzo ndi nthawi yake (yomwe idakhazikitsidwa kale). Tsiku lomwe lipenga lidzaimbidwa ndipo inu mudzatuluka muli ambiri. Ndipo thambo lidzatseguridwa ndipo lidzakhala makomo makomo. Ndipo mapiri adzachotsedwa m’malo mwake (ndikukhala fumbi) ndipo adzakhala ngati zideruderu. Ndithu, Jahannam ikuwadikira (oipa). (Ndi) malo a anthu otuluka M’chilamulo cha Mulungu. Adzakhala m’menemo kwa muyaya, Ndipo sadzalawa chilichonse choziziritsa m’menemo ngakhale chakumwa kupatula madzi otentha owira ndi mafinya. (Chilangochi) Ndi malipiro oyenera (olingana ndi machimo awo ndi zochita zawo). Ndithu, iwo sadali akuyembekezera Chiwerengero (cha Allah). Ndipo adazitsutsa zizindikiro zathu (zosonyeza kuuka kwa akufa) kotheratu. Ndipo chilichonse (chochokera m’zochita zawo) tachisunga mochilemba. Choncho Lawani (zipatso ndi zotsatira za zochita zanu), ndipo sitikuonjezerani chinthu china koma Chilango pa mwamba pa chilango.

Ndithu, akapolo owopa Allah adzakhala ndi kupambana kwakukulu, minda ndi zipatso za mphesa, ndi ma buthu (anamwali) ofanana misinkhu, ndi zikho zodzaza ndi zakumwa mpaka Mlomo. M’menemo sakamva mawu opanda pake komanso achabe ngakhale bodza. Amenewa ndi malipiro ochokera kwa Mbuye Wako, Mbuye wakumwamba ndi nthaka ndi zonse zapakati pake, Wachifundo Chambiri. Palibe amene adzakhale ndi mphamvu yolankhula Naye, tsiku lomwe mzimu (Jibraiil [‘alaihis salaam]) Ndi angero adzaimirira m’mizeremizere. Sadzayankhula aliyense mwa iwo kupatula yekhayo amene adzaloredwe ndi (Mulungu) Wachifundo Chambiri (Allah), ndipo adzanena zolondora. Limenelo ndi tsiku lenileni (losakaikitsa), ndipo amene afuna adzitchinjirize kwa Mbuye wake. Ndithu, Tikukuchenjezani za chilango chomwe chili pafupi, tsiku limene munthu adzayang’ana zimene manja ake adatsogoza, ndipo kafiri (munthu osakhulupilira) adzati: “Ndikadakhala dothi! (ndiye kuti sindikadakumana ndi chilango cha tsiku lareloli).

Check Also

Tafseer Ya Surah Lahab

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ تَبَّتْ يَدَا أَبِي لَهَبٍ وَتَبَّ ‎﴿١﴾‏ مَا أَغْنَىٰ عَنْهُ مَالُهُ وَمَا كَسَبَ ‎﴿٢﴾‏ سَيَصْلَىٰ نَارًا …