وَالنَّازِعَاتِ غَرْقًا ﴿١﴾ وَالنَّاشِطَاتِ نَشْطًا ﴿٢﴾ وَالسَّابِحَاتِ سَبْحًا ﴿٣﴾ فَالسَّابِقَاتِ سَبْقًا ﴿٤﴾ فَالْمُدَبِّرَاتِ أَمْرًا ﴿٥﴾
Ndikulumbirira (angelo) amene amachotsa (mizimu ya osakhulupirira) mwaukali, ndi (angelo) amene amachotsa (miyoyo ya okhulupirira) moleza, ndi (Angelo) amene amasambira nayo mizimuyo (m’mlengalenga), ndi (Angelo) amene amapikisana (kukwaniritsa malamulo a Allah Ta’ala).
Monga ziliri kuti Sura Nabai idavumbulutsidwa kuti idzakhazikitse chikhulupiriro cha tsiku la Qiyaamah, momwemonso surayi idavumbulutsidwa kuti idzakambe nkhani zina za Qiyaamah.
M’surayi Allah Ta’ala wayamba ndi kulumbilira machitidwe ena a angero ndi cholinga chofuna kutsimikizira anthu kuti tsiku la Qiyaamah ndi lotsimikizika. Choncho, m’ndime yachisanu ndi chimodzi, atalumbirira machitidwe osiyanasiyana a angero, Allah Ta’ala akuyankhula za tsiku la Qiyaamah.
Popeza ndi zachidziwikire kuti Allah Ta’ala walumbirira angero amene amachotsa miyoyo ya anthu ndi kumudziwitsa munthu kuti Qiyaamah ya munthu aliyense imayamba iye akamwalira. Choncho, kwanenedwa momveka bwino kuti: “Amene wamwalira, Qiyaamah yake yayamba.
Ngakhale Qiyaamah yeniyeni ya zolengedwa zonse idzachitikale kumapeto kwa dziko lapansi, komabe popeza moyo otsatira wa munthu umayambika pa akamwalira, imfa ya munthu aliyense imatengedwa ngati Qiyaamah yake.
Tikaonetsetsa, m’ma aya awa Allah Ta’ala akukamba machitidwe asanu a angero. Makhalidwe asanuwa ndi awa:
Khalidwe loyamba
وَالنَّازِعَاتِ غَرْقًا ﴿١﴾
Ndikulumbirira (angelo) amene amatulutsa (mizimu ya osakhulupirira) mwampamvu
M’ndime iyi, Allah Ta’la akufotokoza za angero a imfa amene amachotsa mizimu ya makafiri mwaukali ndi mwankhanza, osawachitira chifundo. Angero amene amachotsa mizimu ya makafiri ndi angero achilango, ndipo mawu oti “mwankhanza” mu Aayah akutanthauza kuwawa kwauzimu osati kuwawa kwakuthupi. Chifukwa chake, anthu omwe ali pafupi ndi munthu wakufayo sangazindikire ululu wa munthu wakufayo monga momwe ululu umamvekera ndi moyo wa munthu wakufayo, osati thupi lake.
Nthawi zina zimaoneka ngati kuti mzimu wa kaafir umachoka m’thupi lake mosavuta, koma zoona zake n’zakuti sizili choncho, monga momwe zilili m’ndime iyi Allah Ta’ala akutiuza za ululu waukulu ndi masautso amene mzimu wa kafiri umakumana nawo yomwalira.
Ubwino Wachiwiri wa Angelo
وَالنَّاشِطَاتِ نَشْطًا ﴿٢﴾
Ndikulumbilira (angelo) amene amatulutsa (mizimu ya okhulupirira) Modekha
M’ndime iyi, Allah Ta’la akufotokoza za angero amene amatulutsa mizimu ya okhulupirira modekha ndi moleza. Angelo amene amachotsa mizimu ya okhulupirira amatchedwa angelo achifundo. Iwo amalamulidwa ndi Allah Ta’ala kuti achite ndi Asilamu mwaubwino ndi wodekha.
Liwu loti “النٰشطٰت” likuchokera ku liwu loti “نشط” lomwe kwenikweni limatanthauza “kumasula mfundo”. Izi zikutanthawuza “kumasula mfundo ya chinthu chomwe chili ndi madzi kapena mpweya, kuti madzi kapena mpweya utuluke mosavuta”. Ili ndi fanizo lotulutsa mizimu ya okhulupirira mofatsa, mosiyana ndi mizimu ya osakhulupirira yomwe imatulutsidwa mwankhanza. Zili ngati kuti mzimu wa okhulupirira unali omangidwa m’thupi lake, ndipo thupi linafunika kutsegulidwa kuti mzimuwo utulutsidwe.
Pankhani imeneyinso, liwu lakuti نَشۡطًا lomwe limamasulira kuti “mosalala” kapena “modekha” limatanthauza kufewa kwauzimu kapena kufatsa, osati ku zochitika zakuthupi. Nthaŵi zina, okhulupirira opembedza amaonedwa akukumana ndi vuto linalake panthaŵi ya imfa yake, komabe, zimenezi sizingatanthauze kwenikweni kuti akukumana ndi vuto linalake lauzimu kapena chilango, ngakhale kuti kuthupi, zingamaoneke choncho kwa awo amene ali nawo pafupi.
Ukatulutsidwa mzimu wa kafiri, chithunzi chonse cha chilango cha barzakh (moyo wa pambuyo pa imfa) chimadza pamaso pake. Imakahala nthawi yochititsa mantha ndi kuopsya kwambiri, ndipo munthu amene wamwalirayo amathedwa nzeru ndi zimenezo. Popeza mzimu, ukuchita mantha kwambiri ndi zochitika zachilango, umayamba kusuntha thupi lonse, kuyesa kubisala kapena kuthawa chilango. Komabe, angero a imfa amauchotsa mzimu wake mwamphamvu, kuutulutsa mwamphamvu ndi mwaukali m’thupi lake, monga momwe mzinga umazulidwira mwamphamvu muubweya onyowa (monga momwe tafotokozera mu Hadith ya olemekezeka Baraa bin Aazib (radhiyallahu ‘anhu) yolembedwa mu Musnad-e-Ahmed).
Komano, mzimu wa Msilamu ukachotsedwa, malipiro aakulu ndi madalitso a tsiku Lomaliza amene wamusungira amaperekedwa kwa iye ndipo amapatsidwa nkhani yabwino ndi yosangalatsa, choncho mzimu wake umachoka m’thupi momasuka ndi chisangalalo chachikulu.
Khalidwe Lachitatu la Angelo
وَالسَّابِحَاتِ سَبْحًا ﴿٣﴾
Ndi amene amasambira (nayo mizimuyo) mu mlengalenga (popita nayo ku malo ake oyembekezera.
Mu ayah iyi, Allah Ta‘ala akulankhula za khalidwe lachitatu la angelo. Angelo omwe akutchulidwa mu ndime iyi ndi angelo a imfa omwe, atatulutsa mzimu wa munthu, amayendayenda mofulumira mu mlengalenga atanyamula mzimu kupita kumwamba kuti akaupereke kwa Allah Ta‘ala.
Mawu akuti “سٰبحٰت” amachokera ku mawu akuti “سبح” omwe amatanthauza “kusambira” kapena “kuyandama”, koma m’nkhaniyi, ponena za angelo, tanthauzo la mawuwa ndi “kuyenda mofulumira m’mwamba”.
Nkhalidwe Lachinayi La Angelo
فَالسّٰبِقٰتِ سَبۡقًا ۙ﴿۴﴾
Ndipo ndi (angelo) omwe amathamanga limodzi pa mpikisano (kuti akwaniritse lamulo la Allah Ta‘ala)
Mu ayah iyi, Allah Ta‘ala akulankhula za momwe angelo a imfa amathamangitsirana kupikisana wina ndi mnzake kuti akwaniritse lamulo la Allah Ta‘ala.
Malinga ndi lamulo la Allah Ta‘ala, angelo amatenga miyoyo ya opembedza kupita nayo kumalo awo abwino, ndi mizimu ya oipa kupita nayo kumalo awo oipa. Pambuyo pofunsidwa m’manda, mzimu wa okhulupirira umasamutsidwira ku malo a Illiyyeen komwe udzasangalala ndi madalitso a Paradaiso, ndipo mzimu wa osakhulupirira umasamutsidwira ku Sijjeen komwe umakazunzika ku Gehena. (Al-Rooh tsamba 134)
Khalidwe Lachisanu La Angelo
فَالۡمُدَبِّرٰتِ اَمۡرًا ۘ﴿۵﴾
Ndi iwo (angelo) omwe amayendetsa malamulo (omwe amapatsidwa ndi Allah Ta‘ala pankhani okhudza mizimu ya akufa)
Mu ayah iyi, Allah Ta‘ala akunena za angelo omwe amayendetsa nkhani za omwe amwalira ndikukwaniritsa zomwe Allah Ta‘ala walamula popereka mphotho kwa mizimu yolungama ndikulanga mizimu yoipa.
Mwanjira ina, ntchito yomaliza ya angelo awa a imfa idzakhala kutonthoza mizimu yolungama ndikubweretsa ululu kwa mizimu yoipa. Mizimu ikafika pamalo awo abwino kapena oipa, angelo omwe alamulidwa kupereka mphotho ndi kutonthoza mizimu yabwino amasonkhanitsa njira zowalipirira ndi kuwatonthoza, ndipo angelo omwe alamulidwa kulanga ndi kupereka mavuto ku mizimu yoipa amakonza njira zowazunzira ndi kuwalanga.
Mphotho ndi Chilango Za M’manda
Pakadali pano Surah ikutsimikizira kuti nthawi ya imfa, angelo adzafika ndikutulutsa mzimu wa munthu. Kenako adzautenga kupita kumwamba ndikuunyamula mwachangu kupita nawo malo ake oyenera. Mzimu wabwino udzasamutsidwa kupita nawo kumalo a ntendere, ndipo mzimu oipa udzasamutsidwa kupita nawo kumalo a mavuto. Kumeneko angelo adzakonza njira zopezera mphotho ndi chitonthozo, kapena chilango ndi ululu kwa mitundu iwiri ya mizimu motsatana.
Mavesiwa akusonyeza kuti mphotho ndi chilango zidzachitika m’manda (ngati m’moyo wa barzakh munthu atachoka padziko lapansi). Pambuyo pake, Tsiku la Qiyaamah likadzafika, chigamulo chidzaperekedwa kuti munthu akalowe ku Jannah, kapena ku Gahena.
Kukamba za momwe mzimu wa munthu olungama kapena ochimwa umachotsedwera ndi angelo a imfa, pali Hadith yayitali ya Olemekezeka Baraa bin Aazib (radhwiyallahu ‘anhu) yomwe yalembedwa mu Musnad-e-Ahmad. Hadith iyi ndi iyi. Baraa bin Aazib (radhwiyallahu ‘anhu) akunena kuti:
Nthawi ina, tinatuluka ndi Rasulullah (Swallallahu ‘alaihi wasallam) kuti tikaswalire nawo maliro a munthu wachi Ansaar. Titafika kumanda, tinapeza kuti manda anali asanakumbidwe. Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anakhala pansi, ndipo tinakhala momuzungulira, modekha ngati kuti panali mbalame pamitu pathu.
Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anali ndi ndodo m’manja mwake yomwe ankakanda nayo pansi (popeza ankaganiza kwambiri). Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) kenako ananyamura mutu wake nati kawiri ngati si katatu, “Pemphani chitetezo cha Allah Ta‘ala ku chilango cha manda!”
Pambuyo pake, Rasulullah (swallallahu ‘alaihi wasallam) anati, “Ndithudi, okhulupirira akatsala pang’ono kuchoka padziko lapansi kupita ku Moyo omaliza, angelo amatsika kwa iye kuchokera kumwamba. Nkhope zawo zoyera zimawala kwambiri kotero kuti zimakhala ngati kuti nkhope zawo zonse ndi dzuwa. Amabwera ndi sanda yochokera ku siliki ya ku Jannah, komanso mafuta onunkhira ochokera ku mafuta onunkhira a ku Jannah. Amakhala pafupi naye, komwe angayang’ane.
“Pambuyo pake, mngelo wa imfa amabwera kwa iye ndikukhala pambali pake. Mngeloyu amamulankhula nati, ‘Iwe mzimu oyera! Tuluka, kupita ku chikhululuko cha Allah ndi chimwemwe Chake!’ Mzimuwo umatuluka moyenda bwino, monga momwe dontho la madzi limatulukira m’chikopa cha madzi.
Alislaam Yeretsani mtima wanu potsatira chisilamu