Uthenga Wa Sayyiduna Sa’d (Radhwiyallahu Anhu) Kupita Kwa Asilamu Onse

Nkatikati mwa nkhondo ya Uhud, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adafunsa, “kodi Sa’d Bin Rabee alikuti? Sindikudziwa m’mene alili. ’kenaka, m’modzi mwa masahabah adatumizidwa kuti akamuyang’ane Sa’d (radhwiyallahu anhu), adapita pa malo pomwe anthu ofera ku nkhondo adagonekedwa.

Adaitana mokuwa uku akutchula dzina la Sa’d kuti mwina adakali moyo. malo ena ake, nkatikati molengeza kuti watumidwa ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti amuyang’ane Sa’d radhwiyallahu anhu, adanva mawu cha pansi pansi akuyankhulidwa mofooka kuchokera mbali ina, adatembenukira mbali imeneyo ndipo adampeza Sa’d bin Rabee atagona m’chigulugulu cha anthu omwalira ali pafupi kumwalira.

Sayyiduna Sa’d (radhwiyallahu anhu) adanveka kuyankhula mawu oti; mundipelekere salaam kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) pamodzi ndi Uthenga uwu, “’O Mtumiki wa Allah! Allah akulipireni malipiro ochuluka kwambiri komanso okongora kudzera (mu Duwa yanga) mwa ine zimene Nneneri wina aliyense sanalipidweko kudzera mwa (duwa ya) omutsatira wake wina aliyense. ‘”

Kenaka adamuuza munthu amene adatumidwa kuti akamuyang’ane uja kuti, ukawadziwitse asilamu anzanga kuti sadzakhululukidwa patsiku la Qiyamah ngati adani achisilamu angamufikire ndikumupha Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) (ndikupezeka kuti) iwowo asanamwalire, Pamapeto pa mawu amenewa, Sayyiduna Sa’d (radhwiyallahu anhu) adapuma mpweya wake omaliza ndikusiyana nalo dziko lino.

Ma sahabah adasonyeza kudzipereka kwawo pa Mtumiki (sallallahua alaih wasallam), uku atavulazidwa mabala uku akupuma mpweya wawo omaliza, adalibe nkhawa ina iliyonse apalilime pawo ndipo adalibe maganizo ena koma kuganiza za m’mene Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adaliri, Allah atidalitse ndikutipatsa mtima omukonda Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ngakhale chitakhala chochepa ngati njere ya mpilu chomwe ma sahabah adali nacho.

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …