Olemekezeka Talhah (radhwiyallahu anhu) pa nkhondo ya Uhud

Olemekezeka Zubair bin Awwaam (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti pa nkhondo ya Uhud Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adaphatikiza zovala zozitetezera pa nkhondo.

Mkatikati mwa nkhondo Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adafuna kukwera miyala ikulu ikulu koma ankakanika chifukwa chakulemera kwa zovala za pa nkhondo.Choncho adamupempha Olemekezeka Talha (radhwiyallahu anhu) kuti akhale pansi ndicholinga choti alimbilire mwa iyeyo ndikuti athe kukwera pamwalawo. Olemekezeka Talha (radhwiyallahu anhu) mwansangansanga adakhala pansi namuthandiza Mtumiki (swallallah alayhi wasallama) kukwera chimwalacho.

Olemekezeka Zubayru (radhiyallahu anhu) akusimba kuti adamumva Mtumiki (swallallahu alayhi wasallama) akuyankhula panthawi imeneyo kuti; kwakhala kokakamizika kwa Talha (Jannah yakhala yokakamizika kwa Talha kukalowako).

Pa nkhondo ya Uhud, Olemekezeka Talha (radhiyallahu anhu) molimba mtima anali ndi Olemekezeka Mtumiki (swallallah alayhi wasallama) ndipo adamuteteza. Pamene maswahaba (radhiyallahu anhum) akamakambilana zankhani ya Uhud amayankhula kuti tsiku limeneli (tsiku la nkhondo ya uhud) ndi la Talha (radhiyallahu anhu). Olemekezeka Talha (radhiyallahu anhu) pogwiritsa ntchito thupi lake adamuteteza Mtumiki (swallallahu alayhi wasallama). Adali ndimabala oposa makumi asanu ndi atatu (80) komabe sadasiye kumuteteza Mtumiki (swallallah alayhi wasallama) ngakhalenso mpakana manja ake adapuwala kamba kochuluka mabala.

Check Also

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah …