Mphavu za Aliyy (radhiyallahu anhu) pa nkhondo ya Uhud

Pa nkhondo ya Uhud ma swahabah (radhwiyallahu anhum) adagonjetsedwa kwambiri ndi adani ndipo ambiri adaphedwa kumene, Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) Adazunguliridwa ndi adani ndikuvulazidwa kwambiri, nthawi imeneyi mphekesera idayamba kumveka kuti Mtumiki waphedwa, maswahabah atamva mphekesera imeneyi adasweka mitima ndikutaya chiyembekezo.
Hazrat Ali (radhwiyallahu anhu) akufotokoza kuti: tidazunguliridwa ndi adani ndipo sindinkamuona Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) ndidakamufufuza mgulu la anthu amoyo kenako ndidakamuyang’ananso mgulu la anthu ophedwa koma sindidamupeze, ndidadziyankhulira ndekha nati: ndi zosatheka kuti iye athawe nkhondo, zikusonyeza ngati Allah waipidwa Nafe chifukwa cha machimo athu, ndipo wamunyamula Mtumiki kunka naye kumwamba, palibe chomwe ndingachitenso koposera kudziponya mchigulugulu cha adani kufikira nditaphedwa.

“kotero ndidalowa mchigulu cha adani ndikuyamba kulimbana nawo mpakana adayamba kuthawa ndipo kenako maso anga adamuona Mtumiki swallallahu alaih wasallam mchigulugulu cha adani, nditamuona ndidasangalala kwambiri ndipo ndidazindikira kuti Allah wakhala akumuteteza kudzera mwa angelo, ndidampitira ndikuima pambali pake, kenaka ndi pamene gulu la adani lidabwera kuti lidzammenye Mtumiki (swallallahu alaih wasallam), Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adati kwa ine; Oh Ali! Tapita ukawathamangitse, ndidawagonjetsa mosavuta ndipo ena adaphedwa, kenako padadzabweranso ena ndipo Mtumiki adandiuza chimodzimodzi ndipo Ndidalimbana nawo mpakana ena mwa iwo adathawa ndipo ena adaphedwa.

Idali nthawi imeneyi pamene Jibril (alaihis salaam) adabwera kwa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) ndikumutamanda Aliy (radhwiyallahu anhu) chifukwa chakulimba mtima komanso mphavu zake komanso kudzipereka kwake kwa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam), Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adati;

إنه مني وأنا منه

Aliy ndi gawo langa ndipo ine gawo lake (tachokera ku banja limodzi komanso komanso ubale wathu ndi wamphanvu۔

Pamenepa Aliy (radhwiyallahu anhu) adayankha nati;

وأنا منكما

Inenso ndi gawo la awirinu.

Taonani mphavu zimene Aliy (radhwiyallahu anhu) adali nazo pamene Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adamuuza kuti akalimbane ndi adani adadziponya mchigulugulu cha adani ndi kulimbana nawo modzipeleka ndicholinga chofuna kumuteteza Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) kwa adani kuti asamupweteke, izi zikungoonetsa chikondi komanso kudzipereka kwake pa Mtumiki Muhammad (swallallahu alaih wasallam).

Check Also

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah (radhiyallahu ‘anhu)

Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) Awonetsa ku Ummah Udindo olemekezeka wa Abu Ubaidah …