Sayyiduna Abdullah bin Masuud (radhwiyallahu anhu) zikunenedwa kuti iye adati: “Sungani Swalah zanu zisanu pa tsiku popemphera pa malo amene adhaan yaitanidwa (monga musjid). Ndithu, Swalah izi (Fardh) m’Musjid ndi zochokera ku Sunan huda (mapembedzedwe olamuridwa mu Deen). Allah wamulamula Nabiy wake sunan huda (mapembedzedwe amenewa ndi chiongoko kwa inu). M’nthawi ya Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) palibe amene ankasiya Swalaah ya pagulu ku musjid kupatula munaafiq woonekera (wachinyengo woonekera), moti ngakhale munthu odwala sankajomba kumzikiti. M’malo mwake, ankatengedwa kupita ku musjid mothandizidwa ndi anthu awiri. Aliyense mwa inu (ma Swahaabah) ali ndi malo ake oikidwa m’nyumba mwake opemphelerapo Swala za sunnah ndi zina zotero. Koma ngati mutayamba Swalah kupemphelera swalah yanu ya fardh kunyumba ndi kusiya kukapemphelera ku musjid, ndiye kuti mukusiya Sunnah yolimbisitsidwa ndi Mtumiki (swallallahu alaih wasallam). Mukangosiya sunna yake yodalitsika, ndithudi musokera.” [1]
[1] عن عبد الله بن مسعود قال حافظوا على هؤلاء الصلوات الخمس حيث ينادى بهن فإنهن من سنن الهدى وإن الله شرع لنبيه صلى الله عليه وسلم سنن الهدى ولقد رأيتنا وما يتخلف عنها إلا منافق بين النفاق ولقد رأيتنا وإن الرجل ليهادى بين الرجلين حتى يقام في الصف وما منكم من أحد إلا وله مسجد في بيته ولو صليتم في بيوتكم وتركتم مساجدكم تركتم سنة نبيكم صلى الله عليه وسلم ولو تركتم سنة نبيكم صلى الله عليه وسلم لكفرتم (سنن أبي داود، الرقم: 550)