Munthu Wabwino Kwambiri pa Ummah uwu

Hazrat Abu Dardaa radhiyallah anhu wanena kuti: “Nthaŵi ina yake, Mtumiki (Swallallaahu alaih wasallam). adandiona ndikuyenda kutsogolo kwa Hazrat Abu Bakr (Radhiyallahu ‘anhu) “Pamene Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adaona izi, adandiuza kuti: “Usayende kutsogolo kwa amene ali wabwino kuposa iwe.

Pambuyo pake Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adafotokoza za ubwino waukulu wa Hazrat Abu Bakr (Radhiyallahu anhu). Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Abu Bakr (Radhiyallahu ‘anhu) ndi munthu wabwino kwambiri (mu Ummah uno) amene dzuwa lidamutulukira kapena kulowa”.

Check Also

Olemekezeka Abu Zar (Radhwiyallahu ‘anhu) Kulemekeza Alendo

‘Isa bin ‘Umailah (Rahimahullah) akufotokoza za munthu wina amene adawona khalidwe la Abu Zar (Radhwiyallahu …