Kulemba Durood pa kutha kolemba dzina la Mtumiki swallallahu alaih wasallam

عن أبي هريرة قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: من صلى علي في كتاب لم تزل الملائكة تستغفر له ما دام اسمي في ذلك الكتاب (المعجم الأوسط للطبراني، الرقم: 1835، وسنده ضعيف كما في كشف الخفاء، الرقم: 2518)

Olemekezeka Abu Hurairah (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adati “amene angawerenge Durood pambuyo polemba dzina langa Mchitabu chilichonse angelo amampemphera chikhululuko kwa Allah kwa nthawi imene dzinalo lingapezekere mchitabucho.”

Sayyiduna Abu Bakr (Radhiyallahu Anhu) Akonzeka Kuzimana China Chirichonse Pa Mtumiki (Sallallahu Alaih Wasallam)

Nkhondo ya Badr idakali mkati, mwana wa Sayyiduna Abu bakr (radhiyallahu anhu) amene ndi Abdu-Rahman (radhiyallahu anhu) adali mbali ya adani popeza adali asadalowe chisilamu.

Patadutsa nthawi, atalowano chisilamu, ali chikhalire ndi bambo ake omwe ndi Sayyiduna Abu-Bakr Siddeeq (radhiyallahu anhu) adati, oh bambo anga okondedwa, pa nkhondo ya Badr mudayandikana ndiine nditanyamura lupanga langa kangapo konse, komano chifukwa choganizira kuti ndiinu bambo anga, sindikhale ndi maganizo oti ndikupheni. (Tareekh ul khulafaa, 1/33)

Check Also

Kuwerenga Durood Pamkumano

عن أنس عن النبي صلى الله عليه وسلم قال: ما من عبدين متحابين في الله …