Ulemu wa Hazrat Abu Bakr (Radhiyallahu ‘anhu) kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ndi chikondi cha Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) pa Iye

Pa nthawi ya Fat-he-Makkah Mukarramah (Kugonjetsa Makka Mukarramah), Hazrat Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) adabweretsa bambo ake, Abu Quhaafah, kwa Rasulullah kuti akalowe Chisilamu. Pa nthawiyo Abu Quhaafah adali ndi zaka zoposa 90 zakubadwa ndipo adali atasiya kuona.

Atadza kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam), Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamuuza Hazrat Abu Bakr (Radhwiyallahu anhu) nati: “ ndi chifukwa chani siudawasiye Sheikh (munthu wankulu Abu Quhaafah) ndikanatha kubwera kwanu?”

Hazrat Abu Bakr (Radhwiyallaahu ‘anhu) adayankha nati: “Ayi, nkoyenera kuti abwere kwa inu (ngakhale kuti iwo ndi bambo anga, inu ndinu Mtumiki wa Allah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndipo ndinu oyenera kupatsidwa ulemu, choncho nkoyenera kwa ife kubwera kwa inu).

Mu hadith ina, Hazrat Abu Bakr (Radhiyallahu anhu) adafotokoza chifukwa china chomwe adafunira abambo ake kuti abwere kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam), m’malo moti Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) abwere kwa iye.

Adati: “E, Mtumiki wa Allah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Ndinkafuna kuti bambo anga abwere kwa inu kuti iyi ikhale njira yoti Allah Taala awalipire (chifukwa chovutikira kubwera kwa inu, ngakhale kuti anali wosaona). ndi okalamba).

Atamva izi, Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Tidzayesetsa kuwasamalira m’mene tingathere (kutanthauza Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu)).

Kenako Hazrat Abu Bakr (Radhiya Allahu ‘anhu) adawakhazika bambo ake pamaso pa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam), kenako Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adapereka dzanja lake lodalitsika pachifuwa chake nati: “Landirani Chisilamu ndipo mudzadalitsidwa ndi chipulumutso.” Abu Quhaafah adavomera kuitana kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam), ndipo pamenepo adalowa Chisilamu.

Check Also

Muvi Oyamba kulasa Mchisilamu

Olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) adali m’gulu la ma Swahaabah omwe Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawatumiza …