Chikondi cha Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) Kugwirizana ndi Chikondi cha Rasulullah (Sallallahu ‘alaihi wasallam)

Bambo ake a Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) atalowa Chisilamu. Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) adalankhula kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) kuti:

“Ndikulumbirira amene anakuikani m’choonadi! Ngakhale ndiri mchisangalaro kuti bambo anga alowa chisilamu, ndikadakhala osangalala kwambiri zikanakhala kuti omwe alowa chisilamu ndi amalume anu Abu TaalibChifukwa chake ndi chakuti ngati amalume anu, Abu Talib, akanavomereza Chisilamu, izi zikanabweretsa chisangalalo chachikulu m’moyo mwanu (kuposa chisangalalo chomwe mwachipeza pa Chisilamu cha abambo anga).

Atamva izi, Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adakondwera kwambiri ndi Hazrat Abu Bakr. (Radhwiyallahu ‘anhu) nachitira umboni za chikondi chake chenicheni pa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa sallam). Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Ndithu, wanena zoona.”

Check Also

Muvi Oyamba kulasa Mchisilamu

Olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) adali m’gulu la ma Swahaabah omwe Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawatumiza …