Hazrat Abu Bakr Siddeeq (Radhwiyallaahu ‘anhu) akusimba motere za ulendo wa Hijrah ndi Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam):
Tinayenda mofulumira usiku wonse ndi gawo lina la tsiku lotsatira mpaka kutentha kwamasana kunakula kwambiri. Kenako ndinapeza kuti mseu mulibe munthu aliyense woyendamo. Ndinayang’ana kutsogolo kuti ndione ngati ndingapeze mthunzi uliwonse kuti tibisalemo. Kenako ndinaona thanthwe lalikulu limene pansi pake panali mthunzi kuti tithawireko kuti tisamatenthedwe.
Ndinaima pafupi ndi thanthwe (kuti tipume mumthunzi wake), ndipo ndinagwiritsa ntchito manja anga kuti nthaka ikhale yosalala kuti Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) agone ndi kupumula. Kenako ndinayala chikopa chanyama ndikumuuza kuti: “Pumulani Mtumiki wa Allah (Swallallaahu ‘alayhi wa sallam) ndipo ndiyang’anira dera lomwe lakuzungulirani inu”.
Nthawi ina Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adagona kuti apumule, ndidapita kuti ndikaone ngati ndingapeze aliyense amene amatisaka. Kenako ndinaona m’ busa wa ziweto akubwera ku thanthwe kuti nayenso akapume pamthunzi pamene tinali kupuma.
Ndidamufunsa kuti mwini wake ndi ndani, ndipo adatchula munthu wa ku Makka yemwe ndimamudziwa. (Monga momwe chidali chizolowezi chodziwika pa nthawiyo kuti anthu amalola kuti apaulendo apindule ndi mkaka wankhosa zawo, Hazrat Abu Bakr Siddeeq radhwiyallahu anhu adapempha m’busayo mkaka.)
Hazrat Abu Bakr Siddeeq radhwiyallahu ‘anhu) akuti: Ndinamufunsa m’busa kuti, “Kodi mbuzizi zili ndi mkaka?” M’busayo anayankha kuti, Inde. Kenako ndinamufunsa kuti, “Kodi ungandikamileko?”
M’busayo anavomera, koma asanayambe kukama mkaka wa mbuziyo, anamuuza kuti, “Onetsetsani kuti mwayamba mwafuwula mabere a mbuziyo n’kuchotsa fumbi, ubweya ndi dothi lina. M’busayo anaikama mbuziyo n’kuthira mkakawo m’chiwiya changa. Ndinathira madzi ku mkaka kuti aziziziritse mkakawo omwe udali wotentha. Kenako ndinatenga mkakawo kuti ndikaupereke kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam). Sindinafune kusokoneza tulo ta Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) pomudzutsa, koma nditafika, ndinamupeza ali maso.
Kenako ndinam’patsa mkakawo n’kunena kuti: “Imwaniko zimenezi, Oh Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam). Kumuona kwa Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) akusangalala ndi mkaka omwe ndinabweretsa kunabweretsa chisangalalo chachikulu mumtima mwanga.
Kuchokera pankhaniyi, tikuona chikondi chachikulu chomwe Hazrat Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) adali nacho kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam), kuti kuona Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) akumwa mkaka kunabweretsa chisangalalo chachikulu mumtima mwake pomwe sanali amene ankasangalala ndi mkakawo.
Zimenezi zingafanane ndi chikondi chimene mayi ali nacho pa mwana wake akamaona mwanayo akudya mosangalala kumuonako kumadzetsa chimwemwe mumtima mwake.