Hazrat Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu) akhala Wokonzeka kupereka nsembe ya china Chilichonse

Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa sallam) Pankhondo ya Badr, mwana wa Abu Bakr Siddeeq (radhwiyallahu anhu) Hazrat Abdur Rahmaan (Radhwiyallahu ‘anhu), anamenya nawo mbali ya okanira poti iye adali asadakhulupirirebe Chisilamu.

Pambuyo pake, atalowa Chisilamu, ali chikhalire pansi ndi bambo ake, Hazrat Abu Bakr Siddeeq (Radhwiyallahu “anhu), adati: “E, inu abambo anga okondedwa, pankhondo ya Badr, mudali pafupi ndi lupanga langa kangapo. Komabe, ndidakusiyani chifukwa chakuti ndinu bambo anga.” Abu Bakr Siddeeq (radhwiyallahu ‘anhu) adayankha nati. “Ukadakumana ndi lupanga langa sindikadakusiya chifukwa munkalimbana ndi Mtumiki swallallahu alaih wasallam).

Check Also

Abu Zar (radhiyallahu ‘anhu) Apereka Uphungu kwa Mtsogoleri wa Asilikali Kuti Atsatire Chilungamo

Imaam Bayhaqi (rahimahullah) akunena kuti: Yazid bin Abi Sufyaan (radhiyallahu ‘anhu) pamene adali bwanamkubwa wa …