Tafseer Ya Surah Kaafiroon

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ

قُلْ يَا أَيُّهَا الْكَافِرُونَ ‎﴿١﴾‏ لَا أَعْبُدُ مَا تَعْبُدُونَ ‎﴿٢﴾‏ وَلَا أَنتُمْ عَابِدُونَ مَا أَعْبُدُ ‎﴿٣﴾‏ وَلَا أَنَا عَابِدٌ مَّا عَبَدتُّمْ ‎﴿٤﴾‏ وَلَا أَنتُمْ عَابِدُونَ مَا أَعْبُدُ ‎﴿٥﴾‏ لَكُمْ دِينُكُمْ وَلِيَ دِينِ ‎﴿٦﴾‏

Nena: “E, inu anthu osakhulupirira! Ine sindingapembedze (mafano) amene mukuwapembedza, ndiponso simum’pembedza Amene ine ndikum’pembedza (Allah Ta’ala). Ndipo inu simunhampembedze (Allah) Amene ine ndikumupembedza (Allah Taala) inu muli ndi chipembedzo Chanu, ndipo ine ndili so ndi chipembedzo Changa.”

Sura ziwiri, Surah Kaafiroon ndi Surah Ikhlaas, zili ndi tanthauzo lalikulu ndi ubwino. Hazrat Nabiy (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) ankawerenga ma surah awiriwa mu ma sunnat a Fajr ndi Maghrib. Ndipo adalangizanso kuti Surah Kaafiroon idziwerengedwa usiku uliwonse munthu usanagone, chifukwa ndi kulengeza kudzipatula ku shirk ndi ukafiri.

Tsiku lina Nabi (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adalumidwa ndi pimbinyolom/nankalizi. Kotero adawerenga Surah Kaafiruun pamodzi ndi Surah Falaq ndi Surah Naas, ndipo adapaka madzi amchere pamalo pomwe adalumidwapo. Kupyolera mmadalitso a Surah zimenezi adachila.

Chifukwa chomwe chidachititsa kuti surayi ivumbulutsidwe monga momwe Hazrat ibnu Abbaas (Radhiyallaahu ‘anhuma) adanenera, ndikuti nthawi ina gulu la makuraishi lidadza kwa Nabiy (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) namufunsa zotsatirazi. (Iwo) adati: “Tikupatsa chuma chambiri kotero kuti udzakhala munthu wolemera kwambiri ku Makkah Mukarramah yonse. Tidzakupatsa mkazi amene wamfuna kumukwatira ndipo tidzakutsata ndi kumvera iwe monga Mtsogoleri wathu wosatsutsika – ngati utero. usanene zoipa za milungu yathu (mafano). Ngati simuvomereza izi, tivomere kuti upembedze milungu yathu kwa chaka chimodzi, ndipo ife tidzampembedza Mulungu wakonso mchaka chotsatira.

Pazimenezi Hazrat Jibriyl (‘alaihis salaam) adatsika ndi Surah Kaafiroon.

Malinga ndi malipoti ena, zanenedwa kuti ena mwa anthu osapembedza Allah a ku Makkah Mukarramah adapempha Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) pomunyengelera kuti azipembedza milungu yawo. Komabe, Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adakana. Pamenepo iwo adati: “Ee, Muhammad (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) ngati siukufuna kupembedza milungu yathu, ingoyikhudza ina mwa milungu yathu. Ngati uyikhudze, tikukhulupirira ndi kulowa chisilamu.” Apa ndipamene idavumbulutsidwa surayi.

Kwenikweni, makafiri adapereka malingaliro atatu kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘ alayhi wasallam).

Lingaliro loyamba lidali lakuti Mtumiki (Swallallaahu ´alayhi wasallam), asalankhule zotsutsana ndi mafano awo.

Ngati sadakonzekere izi, ndiye kuti lingaliro lachiwiri lidali loti avomereze aphatikize kupembedza kwake ndi kupembedza kwawo ndi chipembedzo chake ndi chipembedzo chawo popembedza milungu yawo kwa chaka chimodzi ndi kuti azipembedza Allah Taala kwa chaka chimodzi.

Lingaliro lachitatu lomwe adapereka kwa iye linali lakuti Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) akhudze mafano awo ndi cholinga chosonyeza ulemu. Komatu Allah Ta’ala adavumbulutsa surayi kumuletsa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) kuvomera chilichonse mwa malingaliro awo.

Uthenga omwe uli mu Surayi

Sura iyi ikunena poyera kuti Chisilamu sichingalumikizidwe kapena kusakanikirana ndi chipembedzo cha makafiri. M’surayi Allah Taala akudzudzula poyera m’chitidwe wa makafiri ndipo akulamula Asilamu kuti apembedze Allah Taala yekha munjira yoti palibe shirk kapena chigololo ndi ukafiri wamtundu uliwonse.

Chifukwa chake Allah Ta’ala akumuletsa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) ndi Ummah kuvomera zonena za makafiri ndikuti chipembedzo cha Chisilamu ndi chipembedzo choyera, changwiro, chokwanira komanso chokhazikika chozikidwa pa mfundo za Tawheed. (umodzi wa Allah Taala) ndi kumvera lamulo la Allah Taala yekha.

Choncho, chipembedzo ichi sichingaphatikizidwe ndi chipembedzo china chilichonse, monganso chipembedzo china chilichonse kupatula Chisilamu chozikidwa pa ukafiri ndi shirk pomwe chipembedzo cha Chisilamu chazikidwa pa ungwiro, tawheed (umodzi wa Allah Taala) ndi kumvera Allah Ta’ala yekha kotheratu.

قُلْ يَا أَيُّهَا الْكَافِرُونَ ‎﴿١﴾‏ لَا أَعْبُدُ مَا تَعْبُدُونَ ‎﴿٢﴾‏ وَلَا أَنتُمْ عَابِدُونَ مَا أَعْبُدُ ‎﴿٣﴾‏ وَلَا أَنَا عَابِدٌ مَّا عَبَدتُّمْ ‎﴿٤﴾‏ وَلَا أَنتُمْ عَابِدُونَ مَا أَعْبُدُ ‎﴿٥﴾‏ لَكُمْ دِينُكُمْ وَلِيَ دِينِ ‎﴿٦﴾‏

Nena: “E, inu anthu osakhulupirira! Ine sindingapembedze (mafano) amene mukuwapembedza, ndiponso simum’pembedza Amene ine ndikum’pembedza (Allah Ta’ala). Ndipo inu simunhampembedze (Allah) Amene ine ndikumupembedza (Allah Taala) inu muli ndi chipembedzo Chanu, ndipo ine ndili so ndi chipembedzo Changa.”

Tikawamvetsetsa mavesi ameneŵa, mwachionekere zikuoneka kuti abwerezedwa. Komabe, pali kusiyana pakati pa mavesi awiri oyambirira poyerekezera ndi mavesi achiwiri.

Ndime ziwiri zoyamba zikunena za nthawi yomwe ili pano ndipo ndime ziwiri zachiwiri zikulozera ku nyengo yamtsogolo kutanthauza kuti panopa, ife sitidzapembedza zimene mukuzipembedza ndiponso sitidzapembedza zimene mukuzipembedza. Choncho musayembekezere kuti tidzakutsatani pazimene mukuzipembedza nthawi iliyonse. Malinga ndi kulongosola uku, “maa” m’ndime zonse zinayi akugwira ntchito ngati “maa mausuula” kutanthauza chinthu chopembedzedwa – ife tikupembedza Allah Taala ndipo inu mukupembedza mafano anu.

Kufotokozera kwachiwiri kwa ayah komwe wapereka ndi Allaamah Ibnu Katheer (rahimahullah), ndiko kuti ‘maa’ m’ndime ziwiri zoyambilira adzamasulira kuti “maa mausuula, ndipo ‘maa’ mu ndime ziwiri zachiwiri atanthauziridwa kuti “Maa mausoola” maa masdariyya”. Mogwirizana ndi izi, ma aya awa adzamasuliridwa kuti: “Sindipembedza (mafano) amene mukuwapembedza, ndiponso simupembedza amene ndikumpembedza (Allah Ta’ala). Ndipo ine sindipembedza m’njira imene mukuipembedza, ndiponso inu simukupembedza m’njira imene ndikupembedza”.

M’mawu ena, malinga ndi kufotokoza kumeneku, mavesi aŵiri oyambirira akusonyeza kuti cholinga cha kulambira kwathu ndi kulambira kwanu n’zosiyana. Ife tikupembedza Allah Taala ndipo inu mukupembedza milungu yanu. Mavesi aŵiri aŵiri akusonyeza kuti ndife osiyana pa kulambira kwathu. mwachitsanzo, njira zathu zolambirira ndizosiyana kotheratu ndipo ndi mitengo yosiyana wina ndi mzake. Pomwe mukufuna kukhalabe panjira yanu yabodza, musayembekezere kuti ine ndichoka panjira ya haq ndikugwirizana ndi njira zanu zopembedzera zolakwika, ndipo sindidzayembekezeranso kuti mugwirizane ndi mapemphero anga. Palibe kuyanjanitsa pakati pa njira zathu zolambirira popeza zonse ndi zosiyana kwa wina ndi mzake.

Kunena zoona ma ayah awa akusonyeza kuti njira ya Chisilamu ndi njira yoyera ndi yolungama, njira yokhulupirira ndi kupembedza Allah Taala yekha ndi kumvera ndi kugonjera zimene wanena yekha popanda kusokonekera kulikonse. M’malo mwake, njira ya shirk ndi Kufr imatsutsana kwambiri ndi njira ya Chisilamu chifukwa ikufuna kuvomereza chilichonse kusiya Allah Ta’ala. Choncho, Msilamu ndi amene sali Msilamu ali m’njira zosiyanasiyana ndipo Msilamu sangatsatire amene sali Msilamu pa mapemphero awo, miyambo, mafashoni, zikondwerero, mabizinesi kugonjera mwa Allah Tabaaraka wata’ala.

Surayi ikufotokoza tanthauzo la Tawheed ndi kugonjera kumalamulo a Allah Taala yekha ndi kufunika kwa wokhulupirira kusonyeza kugonjera kopanda chikaiko ndi kukhulupirika m’mbali zonse za moyo wake wapadziko lapansi ndi wa deen. Wokhulupirira sali ngati wosakhulupirira amene amayenda ndi nthawi ndikusintha ndi zochitika. Koma muzochitika zonse, wokhulupirira amakhalabe wokhulupirika kwa Allah Ta’ala. Ziribe kanthu kuti ingakhale nthawi yanji ya chaka komanso malo omwe amakumana nawo, kaya ali kumudzi kwawo kapena ali patchuthi, kaya m’moyo wake wapakhomo, kapena m’zamalonda – iye amakhalabe wolimba pa deen kwatnthu chifukwa chodziwa kuti iye ndi woyankha kwa Allah Taala.

Iye satengeka ndi miyambo ndi zichitochito za makafiri nthawi iliyonse, koma amawunikira mfundo zenizeni za Chisilamu kulikonse kumene akupita ndi amene angakumane naye. Mkhalidwe umenewu ndi umene udapezeka mwa ma Swahaabah radhwiyallahu anhum. umene udawapangitsa kukhala opambana kulikonse kumene ankapita pa dziko lapansi ndi kuchititsa mitima ya anthu kukopeka ndi Chisilamu pongokumana nawo.

Check Also

Tafseer ya Surah Ikhlaas

بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ قُلْ هُوَ اللَّهُ أَحَدٌ ‎﴿١﴾‏ اللَّهُ الصَّمَدُ ‎﴿٢﴾‏ لَمْ يَلِدْ وَلَمْ يُولَدْ ‎﴿٣﴾‏ وَلَمْ يَكُن لَّهُ كُفُوًا …