Munthu Woyamba wa Ummah uwu kukalowa ku Jannah

M’ Hadith ya yodaliysika, Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adalongosora kuti Ummah wake udzalowa ku Jannah pamaso pa ma Ummah ena onse, ndipo kuchokera mu Ummah wake wonse, Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) adzakhala munthu woyamba kulowa ku Jannah pambuyo pake.

Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Hazrat Jibreel (‘alaihis salaam) adaonekera patsogolo panga, nandigwira dzanja langa ndikundionetsa khomo la Jannah momwe Ummah wanga udzaloweramo.” Hazrat Abu Bakr (radhiya Allaahu anhu) adayankha: “E, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Ndikadalakalaka ndikadakhala nawe (pamene Hazrat Jibreel alaihis salaam) amakuonetsa khomo la Jannah) kuti ndilionenso!”

Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Koma iwe Abu Bakr, ndiwe munthu woyamba kulowa mu Jannah mu Ummah wanga.”

Check Also

Mantha a Olemekezeka Talha (radhwiyallahu annhu) kuopa kuti Chuma cha Padziko Lapansi chisamuchititse Osakumbukira Allah Ta’ala.

Nthawi ina, Olemekezeka Talha (radhwiyallahu anhu) adalandira ndalama zokwana ma dirham zikwi mazana asanu ndi …