Ubwino Waukulu Wowerenga Durood Tsiku la Jumuah

عن أوس بن أوس قال: قال رسول الله صلى الله عليه وسلم: إن من أفضل أيامكم يوم الجمعة فيه خلق آدم وفيه قبض وفيه النفخة وفيه الصعقة فأكثروا علي من الصلاة فيه فإن صلاتكم معروضة علي قال: قالوا: يا رسول الله وكيف تعرض صلاتنا عليك وقد أرمت يقولون بليت فقال: إن الله عز وجل حرم على الأرض أجساد الأنبياء (سنن أبي داود، الرقم: 1047، وقال الحاكم في مستدركه، الرقم: 1029: هذا حديث صحيح على شرط البخاري ولم يخرجاه وأقره الذهبي)

Hazrat Aws bin Aws (radhwiyallahu anhu) akuti: Rasulullah (Swallallahu alaih wasallam) Adati: “M’masiku anu abwino tsiku la ljuma ndi tsiku labwino kwambiri, Lachisanu, Adam (alaih salaam) adalengedwa, lachisanu ndi lomwe adamwalira, lipenga lidzalira tsiku la Jumuah komanso lachisanu zolengedwa zonse zidzakomoka, adamwalira,kotero Chulukitsani kundiwerengera duruud tsiku limeneli popeza idzandifika. Swahaabah mmodzi adafunsa: “E, Mtumiki wa Allah: “Kodi Duruud yathu idzaonetsedwa kwa inu bwanji pomwe thupi lanu lidzakhala lavunda m’manda?” Adayankha Mtumiki (swallallahu alaih wasallam): “Ndithu, Allah waletsa nthaka kudya matupi a Aneneri.”

Kuchokera Mchitabu chotchedwa ‘Qoot-ul-Quloob’, Allaamah Sakhaawi (rahimahullah) adagwira mawu akuti ‘Durood yochuluka’ yomwe yatchulidwa mu Hadith yomwe ili pamwambayi, ikunena zoti ngakhale utamawerenga kakhumi ka 300 tsiku lililonse.

Moulana Rashid Ahmad Gangohi (rahimahullah) adalangizanso omutsatira ake kuti adziwerenga duruud ka 300 tsiku lililonse. Hazrat Zainul Aabidiin, Ali bin Husain (rahimahullah) adanenapo kuti chizindikiro cha Alhlis sunnah wal Jama ndi kochulukitsa kwambiri kuwerenga Duruud pa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam).

Uthenga Wa Sayyiduna Sa’d (Radhwiyallahu Anhu) Kupita Kwa Asilamu Onse

Nkatikati mwa nkhondo ya Uhud, Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adafunsa, “kodi Sa’d Bin Rabee alikuti? Sindikudziwa m’mene alili. ’kenaka, m’modzi mwa masahabah adatumizidwa kuti akamuyang’ane Sa’d (radhwiyallahu anhu), adapita pa malo pomwe anthu ofera ku nkhondo adagonekedwa.
Adaitana mokuwa uku akutchula dzina la Sa’d kuti mwina adakali moyo. malo ena ake, nkatikati molengeza kuti watumidwa ndi Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) kuti amuyang’ane Sa’d radhwiyallahu anhu, adanva mawu cha pansi pansi akuyankhulidwa mofooka kuchokera mbali ina, adatembenukira mbali imeneyo ndipo adampeza Sa’d bin Rabee atagona m’chigulugulu cha anthu omwalira ali pafupi kumwalira.

Sayyiduna Sa’d (radhwiyallahu anhu) adanveka kuyankhula mawu oti; mundipelekere salaam kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) pamodzi ndi Uthenga uwu, “’O Mtumiki wa Allah! Allah akulipireni malipiro ochuluka kwambiri komanso okongora kudzera (mu Duwa yanga) mwa ine zimene Nneneri wina aliyense sanalipidweko kudzera mwa (duwa ya) omutsatira wake wina aliyense. ‘”

Kenaka adamuuza munthu amene adatumidwa kuti akamuyang’ane uja kuti, ukawadziwitse asilamu anzanga kuti sadzakhululukidwa patsiku la Qiyamah ngati adani achisilamu angamufikire ndikumupha Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) (ndikupezeka kuti) iwowo asanamwalire, Pamapeto pa mawu amenewa, Sayyiduna Sa’d (radhwiyallahu anhu) adapuma mpweya wake omaliza ndikusiyana nalo dziko lino.

Ma sahabah adasonyeza kudzipereka kwawo pa Mtumiki (sallallahua alaih wasallam), uku atavulazidwa mabala uku akupuma mpweya wawo omaliza, adalibe nkhawa ina iliyonse apalilime pawo ndipo adalibe maganizo ena koma kuganiza za m’mene Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adaliri, Allah atidalitse ndikutipatsa mtima omukonda Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) ngakhale chitakhala chochepa ngati njere ya mpilu chomwe ma sahabah adali nacho.(Fadail-e-Amaal, Pg, 170)

Check Also

Kuwerenga Durood Pamkumano

عن أنس عن النبي صلى الله عليه وسلم قال: ما من عبدين متحابين في الله …