Kukhudzika kwa Sayyiduna Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) pa Swalaah

M’mawa womwe Umar (radhwiya allaahu ‘anhu) adabayidwa, Olemekedzeka Miswar bin Makhramah (radhwiyallahu ‘anhu) adadza kudzamuona. Polowa mnyumba adapeza Umar (radhwiyallahu ‘anhu) atafunditsidwa ndi ndi nsalu ali chikomokere.

Olemekezeka Miswar (radhwiyallahu ‘anhu) adafunsa anthu omwe adalipo pamenepo kuti, “Ali bwanji?” Iwo anayankha kuti: “Ali chikomokere monga mukuwoneramu.” Chifukwa panalibe nthawi yochuluka yotsala kuti swalah ya fajr, Hazrat Miswar (radhwiyallahu ‘anhu) adawalangiza kuti: “Mudzutseni pomuitanira Swalah, pakuti palibe chinthu china chimene inu Mungamudzutsire chifukwa chimene chofunika kwambiri kwa iye kuposa Swalaah.”

Iwo adayamba kuyankhula mawu: “Swalah, Oh Ameer-ul-Mu’mineen! Atangochita izi, Umar (radhwiyallahu ‘anhu) adadzuka nati, “Inde! Ndikulumbira mwa Allah! Palibe gawo m’Chisilamu kwa amene ali onyalanyaza Swalaah!”

Umar (radhwiyallahu ‘anhu) pambuyo pake adaswali Swalah yake uku magazi akutuluka pabala lake.

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …