بِسْمِ اللَّهِ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ
تَبَّتْ يَدَا أَبِي لَهَبٍ وَتَبَّ ﴿١﴾ مَا أَغْنَىٰ عَنْهُ مَالُهُ وَمَا كَسَبَ ﴿٢﴾ سَيَصْلَىٰ نَارًا ذَاتَ لَهَبٍ ﴿٣﴾ وَامْرَأَتُهُ حَمَّالَةَ الْحَطَبِ ﴿٤﴾ فِي جِيدِهَا حَبْلٌ مِّن مَّسَدٍ ﴿٥﴾
Manja awiri a Abu Lahab awonongeke, ndipo awonongekeretu! chuma chake sichidampindulire ngakhalenso zomwe adapeza. Posachedwapa adzalowa m’moto wodzadza ndi malawi oyaka, komanso mkazi wake, woipa wonyamula nkhuni . M’khosi mwake adzazingidwa ndi (kolala yachitsulo ngati) chingwe chopota cha ulusi wa masamba a kanjedza.
Pamene Aya yoti (ndikuti achenjeze abale ako a pamtima za chilango cha tsiku lomaliza ngati sadakhulupirire) idavumbulutsidwa kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam), Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adakwera pa phiri la Safaa naitana anthu osiyanasiyana. Mafuko a makuraishi, “O Bani Abd Manaaf! O Bani Abdul Muttalib!” ndi ena.
Pamene mafuko osiyanasiyana a makuraishi adamva kuitana kwake, adasonkhana kwa iye kuti amve zomwe wawaitanira.
Kenako anawauza kuti: “Nditakuuzani kuti gulu lankhondo lamanga msasa m’munsi mwa phiri ili ndipo likufuna kumenyana nanu m’bandakucha, kodi mungandikhulupirire?”
Onse adayankha ndi liwu limodzi kuti: “Ndithu titha kukukhulupirira chifukwa sitidakupezeko kuti ndiwe wabodza kapena wosakhulupirika.”
Kenako Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawachenjeza kuti: “Ngati mukulephera kuvomereza uthenga wanga, ndikukuchenjezani za moto woyaka moto umene ukukuyembekezerani tsiku lomaliza.
Abu Lahab (m’modzi mwa amalume a Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)) atamva uthenga uwu kuchokera kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adakwiya kwambiri, ndipo mokwiya adamuwuza Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) kuti: Kodi ndi chifukwa chake umatisonkhanitsa pamodzi? uwonongeke! Kodi ndi cholinga chokhacho watisonkhanitsira pano?
Apa ndipamene idavumbulutsidwa surayi.
M’surayi Allah Ta’ala akuyankha temberero la Abu Lahab kwa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndi mawu omwewo omwe Abu Lahab adawagwiritsa ntchito potemberera Mtumiki (Swallallaahu ‘alaihi wasallam).
Allah Taala akuti,
تَبَّتْ يَدَا أَبِي لَهَبٍ وَتَبَّ ﴿١﴾
Manja awiri a Abu Lahab awonongeke, ndipo awonongekeretu!
M’ndime imeneyi, mawu akuti “yad” anatchulidwa. Mawu akuti “yad” kwenikweni amatanthauza “dzanja”.
Chifukwa chomwe dzanja likutchulidwira ndikuti dzanja limagwira ntchito yofunika kwambiri pokwaniritsa ntchito ndi zosiyanasiyana za anthu.
Choncho, m’ndime iyi, Allah Ta’la akunena kuti awonongeke manja a Abu Lahab.
Nthaŵi zina, m’chinenero cha Chiarabu, liwu lakuti dzanja limatchulidwa, koma munthu mwiniyo amalingaliridwa.
M’ndime iyi, manja a Abu Lahab akutchulidwa, koma umunthu wake wonse ndi cholinga, popeza thupi lake lonse lidzalandira chilango ndipo lidzapsa ndi moto wa Jahannum.
M’mahadith ena zanenedwa kuti surayi idavumbulutsidwa pa nthawi imene Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndi ma Swahaabah ake (Radhwiyallahu ‘anhum) adanyanyalidwa ndikusungidwa moumirizidwa m’chigwa cha Abu Taalib. Inali nthawi imeneyo pamene Abu Lahab anakumana ndi anthu ena n’kuwauza kuti: “Muhammad (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) akutichenjeza za zinthu zambiri zomwe zidzachitike pambuyo pa imfa (mwachitsanzo chilango cha kumanda, ndi zina zotero) koma ine sindikuona Chilichonse mwa izi ziikuchitika kwa amene adamwalira pakati pathu (omwe sadalandire chipembedzo chake). Manja anga adzalandira chilango chanji? Kenako adauzira m’manja mwake nati: “Uwonongeke, koma ndithu, sindikuona kuti zimene Muhammad (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) akunena ndi zoona.” Pambuyo pake surayi idavumbulutsidwa.
Abu Lahab anapitirizabe kumunyoza Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam), kumunyoza ndi kumudzudzula chifukwa chofalitsa deen kwa anthu, koma Allah Ta’ala anateteza ulemu ndi nyota ya Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndipo adantemberera Abu Lahab m’bukhu lake lolemekezeka la Qur’aan Majeed.
Choncho, tikupeza kuti ngakhale surayi idavumbulutsidwa, sadasiye zoipa zakezo ndipo adapitiriza kumuononga Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndi Asilamu, poyesetsa kuti athetse ntchito ya Chisilamu.
Tikuwona kuti ngakhale adatsutsana ndi Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) pa nthawi yonse ya utumiki wake, masautso ake adangoyamba kumene, mpaka patangotha sabata imodzi itatha nkhondo ya Badr, adadwala matenda omwe adayamba ndi zilonda kuphulika thupi lake.
Banja lake ndi ana ake onse anamuthawa n’kumusiya mpaka palibe amene ankafuna ngakhale kuyandikira kwa iye. Choncho, iye anafa ali yekhayekha mochititsa manyazi.
Atamwalira, thupi lake lidatsala pang’ono kuvunda komanso kuwola chifukwa palibe amene amafuna ngakhale kukhudza thupilo chifukwa choopa kuti angatenge matendawo.
Patapita nthawi, anthu a m’tauniyo anaumirira kuti mtembowo ukatayidwe kwinakwake Choncho, akapolo ena analembedwa ganyu yokumba dzenje n’kuponya mtembowo. Ngakhale akapolowo sanayerekeze kugwira mtembowo ndi manja opanda kanthu, choncho anagwiritsa ntchito mitengo yokankhira mtembo wake m’dzenjemo ndikuukwirira ndi miyala.
Awa adali masautso ndi mazunzo omwe adakumana nawo adakali padziko lapansi pompano.
Kupitilira pamenepo mazunzo omwe akakumane nawo pa tsiku lachiweruzo ndiye ndi osaneneka,monga m’mene Qur’an ikunenera.
مَا أَغْنَىٰ عَنْهُ مَالُهُ وَمَا كَسَبَ ﴿٢﴾
Chuma chake sichidamupulumutse, ngakhalenso zomwe adapeza.
Nthawi zonse Abu Lahab ankadzitamandira chifukwa cha chuma chochuluka chomwe anali nacho ndi ana ake omwe anali kumbali yake zomwe kumuthandizira. Amatha kuyankhula, ngati zimene Muhammad (swallallahu alaihi wasallam) akunena ndizoona kuti ndikalangidwa m’moyo omwe ulimkudza, ndiye kuti palibe chifukwa choti ndizidandaula chifukwa chuma changa ndi ana anga zidzandithandiza umoyo omwe ulimkudza. ”
Allah ayankha izi kuti ana ake ndi chuma sizidzapindula kwa iye tsiku la chimaliziro, ndipo sadzagwiritsa ntchito zinthu izi kuti azipulumutse yekha ku chilango chamuyaya cha tsiku lomaliza.
Ngakhale asanachoke padziko lino lapansi, Allah anamuonetsa zina mwa zomwe adzakumane nazo pa tsiku lachiweruzo, popeza padalibe china chilichonse monga chuma chake ndi ana ake pamene ankadwala kwambiri komanso ndi nthawi imene zimenezi zidali zofunikira kwambiri pa nthawi imeneyi.
Panalibe aliyense yemwe analipo kumbali yake panthawi yomwe anali chigonere kudwala. Onse anali atamusiya, adamusiya kuti adzifere yekha.
سَيَصْلَىٰ نَارًا ذَاتَ لَهَبٍ ﴿٣﴾ وَامْرَأَتُهُ حَمَّالَةَ الْحَطَبِ ﴿٤﴾
Posachedwa akaponyedwa ku moto wodzala ndi malawi akuyaka, komanso mkazi wake wonyamula nkhuni.
Mkazi wa Abu Lahab, Ummu Jamiil, ngati mwamuna wake, anali mdani woipitsitsa wa Rasulullah (Swallallahu alaih wasallam) Ankamuthandizira mwamuna wake polimbana ndi Rasulullah (Swallallaahu alaih wasallam) ndi Chisilamu.
Chifukwa chake, m’ndime iyi, Allah Ta’ala amamuchenjezanso naye za kulangidwa kwa tsiku lomaliza komwe kumamuyembekezera.
Allah Taala akumutchula iye kuti ‘onyamura nkhuni’.
Malinga ndi malipoti ena, ankakonda kutolera nthambi zamtengo zokhala ndi minga kuchokera m’nkhalango ndikuziika m’njira yodutsa Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) kuti avutike. Uku ndikulongosola kumodzi kwa mawu oti nkhuni ‘.
Malinga ndi mamufassiriina ena, mawu onena kuti “Onyamula nkhuni” ma Arab amagwiritsa ntchito kumutchulira munthu yemwe amatolera nkhani zopititsa udani patsogolo pochita miseche.
Chifukwa chimene Ummu Jamiil anapatsidwira dzina limeneli ndikuti ankapeka nkhani zoipa kumpekera Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) ndicholinga chofuna kukwelezera udani.
فِي جِيدِهَا حَبْلٌ مِّن مَّسَدٍ ﴿٥﴾
Mozungulira khosi lake pali (kolala ya chitsulo ngati) chingwe chopota cha kanjedza.
Umu ndi momwe adzaukitsidwire tsiku la qiyamah, kuti mkhosi mwake mudzakhala kolala ngati chingwe chopota cha kanjedza.