Hazrat Umar (radhiyallahu anhu) nthawi zonse ankavomereza udindo wapamwamba wa Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo sankadzitenga ngati iye ndi wofanana ndi Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu).
Ulendo wina gulu la anthu linamutamanda Umar (radhwiyallahu ‘anhu) ponena kuti: “Ndikulumbirira kwa Allah! Sitinaonepo munthu wolungama, wonena zoona, ndi wokhwimitsa zinthu kwambiri kwa achinyengo kuposa inu, Oh Ameer-ul-Muuminii ! Pambuyo pa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) palibenso munthu wina olungama kwambiri kuposa inu (mu Ummah uno)!”
Atamva izi Auf bin Maalik (radhwiyallaahu ‘anhu) adawatsutsa anthu omwe adatchula mawu awa: “Anthu inu simunanene zoona!!”ndikumbira mwa Allah! Ndidamuonapo munthu wina yemwe ndi olemekezeka kwambiri pambuyo Mtumiki (swallallahu alaih wasallam).
Pamene anthu adamufunsa Auf (radhwiyallaahu ‘anhu) kuti akutanthauza ndani, iye adayankha.
Adati: “Ndikunena za olemekezeka Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) (yemwe ndi munthu wamkulu kwambiri wa Ummah uwu pambuyo pa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndi Ambiyaa.”
Kenako Umar (radhwiyallahu ‘anhu) adati: “Ndikulumbirira Allah! Auf (radhwiyallahu ‘anhu) wanena zoona ndipo inu anthu simunanene zoona! Abu Bakr (radhiyallahu ‘anhu) anali wonunkhira kwambiri kuposa musk (pelefyumu) pamene ine ndinali wosokera kwambiri kuposa ngamira yakubanja langa).
Olemekezeka Umar (radhwiyallahu ‘anhu) adazitchula chonchi ponena za nthawi yomwe adali asanalowe Chisilamu, ndipo panthawiyo Abu Bakr (radhwiyallahu ‘anhu) adali kale ndi Imaan ndipo adali atapambana ku Deen).