Imaam Shaafi’e (rahimahullah) walemba mu chitabu chotchedwa Ikhtilaaful Hadith kuti:
Sitikudziwa mwa akazi olemekezeka a Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) kusiya nyumba zawo ndikupita kunzikiti kukaswali Swalaah ya Jumuah kapena Swalah ina iliyonse, ngakhale kuti adali akazi olemekezeka a Sayyiduna Rasulullah chifukwa cha udindo wawo wapadera ndi ubale wawo ndi Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam). Zikadakhala zoyenerera kwa iwo kuposa mkazi aliyense kukwaniritsa faraaidh (swalah zokakamizidwa) mu musjid, komabe iwo sadachite izi.
Padali akazi ambiri amene adali pafupi ndi Mtumiki (Swallallahu A’laih Wasallam) mwa akazi a m’banja lake, akazi ake olemekezeka, ana ake aakazi, akapolo ake aakazi ndi akapolo achikazi a m’banja lake; omwe adachoka panyumba kuti akaswali nawo Swalaah ya Jumuah pambuyo pa Mtumiki (swallallah alaihi wasallam), ngakhale kuti Swalaah ya Jumuah inali yokakamizidwa kwa amuna kuposa Swalaah zina zonse. Momwemonso, ine sindikudziwako aliyense mwa iwo amene amachoka m’nyumba kukachita mapemphero awo usiku kapena masana, komanso sadapiteko ku mzikiti wa Qubaa, ngakhale kuti Sayyiduna Rasulullah amapita ku Qubaa, nthawi zina ankapita pachokwera. Ndipo pena ankayenda wapansi, ndipo sadapiteko ku mizikiti ina iliyonse. Ndilibe chikaiko kuti chifukwa cha ubale wawo wapadera ndi Sayyiduna Rasulullah (Swallallaahu alaih wasallam), adali ofunitsitsa kupeza ubwino ndi malipiro ndipo ankadziwa njira zopezera malipiro kuposa akazi ena, komabe sadapite ku Mzikiti kukaswali (ankapemphelera mnyumba).
Sindikudziwapo za akuluakulu athu pa Dini akulamula aliyense mwa akazi awo kuti apite ku Swalaah ya Jumuah ngakhalenso Swalaah zina za pagulu usiku kapena masana. Akadadziwa kuti pali ubwino uliwonse mwa akazi kusiya nyumba zawo ndi kukapemphera Swalah kumzikiti, ndithu, akadawalangiza ndikuwalola kutero. M’malo mwake, zafotokozedwa kuti Mtumiki (swallallahu alaih wasallam) adati:
“Swalah ya mkazi m’chipinda chake ndi yabwino kuposa Swalaah yake m’chipinda chochezera cha m’nyumba mwake, ndipo Swalah yake m’chipinda chochezera m’nyumba mwake ndiyabwino kuposa Swalaah yake ya munzikiti.”